-
Anthu a Mitundu Ina Anamva Uthenga WabwinoZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 98
Anthu a Mitundu Ina Anamva Uthenga Wabwino
Atumwi anamvera lamulo la Yesu loti uthenga wabwino ulalikidwe padziko lonse. Mu 47 C.E., abale a ku Antiokeya anatumiza Paulo ndi Baranaba kuti akalalikire. Anthu awiriwa anazungulira ku Asia Minor ndipo anafika ku Debe, ku Lusitara ndi ku Ikoniyo.
Paulo ndi Baranaba ankalalikira kwa aliyense mosaganizira kuti ndi wolemera kapena wosauka, wamkulu kapena wamng’ono. Ambiri ankamvetsera ndithu. Paulo ndi Baranaba akulalikira kwa bwanamkubwa wina dzina lake Serigio Paulo, munthu wina wamatsenga ankafuna kusokoneza. Ndiyeno Paulo anamuuza kuti: ‘Iwe Yehova akulanga.’ Nthawi yomweyo munthuyo anasiya kuona. Bwanamkubwa uja ataona zimenezo anakhala wokhulupirira.
Paulo ndi Baranaba ankalalikira m’nyumba za anthu, m’misika, m’misewu ndiponso m’masunagoge. Atafika ku Lusitara anachiritsa munthu wina wolumala. Ndiyeno anthu ataona zimenezi ankafuna kuwalambira poganiza kuti iwowo ndi milungu. Koma Paulo ndi Baranaba anawauza kuti: ‘Anthu inu, ifetu ndi anthu ngati inu nomwe. Muzilambira Mulungu yekha.’ Koma kenako kunabwera Ayuda amene anasokoneza maganizo a anthu. Nthawi yomweyo anthuwo anayamba kugenda Paulo ndi miyala kenako anamukokera kunja kwa mzinda poganiza kuti wafa. Koma Paulo anali adakali ndi moyo. Kenako abale anapita kukamutenga n’kupita naye mumzinda. Patapita nthawi, Paulo anabwerera ku Antiokeya.
Mu 49 C.E., Paulo anauyambanso ulendo wina. Atachoka ku Asia Minor, anapita kukalalikira ku Ulaya. Iye anafika ku Atene, ku Filipi, ku Tesalonika komanso m’madera ena. Pa ulendowu anali ndi Sila, Luka komanso mnyamata wina dzina lake Timoteyo. Iwo anagwira limodzi ntchito yokhazikitsa mipingo komanso kuilimbikitsa. Paulo anakhala ku Korinto kwa chaka chimodzi ndi hafu n’cholinga choti alimbikitse abale akumeneko. Iye ankalalikira, kuphunzitsa komanso kulemba makalata opita kumipingo yosiyanasiyana. Koma ankagwiranso ntchito yopanga matenti kuti azipezako ndalama. Kenako Paulo anabwerera ku Antiokeya.
Mu 52 C.E., Paulo anauyamba ulendo wachitatu. Atachoka ku Asia Minor anafika ku Filipi, komwe ndi kumpoto kwenikweni ndipo kenako anapita ku Korinto. Iye anakhala zaka zingapo ku Efeso komwe ankaphunzitsa, kuchiritsa anthu komanso kuthandiza mpingo wakumeneko. Tsiku lililonse, ankakamba nkhani muholo yapasukulu ina. Anthu ambiri ankamvetsera uthenga wake ndipo anasintha makhalidwe awo. Paulo atalalikira m’madera ambiri anapita ku Yerusalemu.
“Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse.”—Mateyu 28:19
-
-
Woyang’anira Ndende Anaphunzira Mawu a YehovaZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 99
Woyang’anira Ndende Anaphunzira Mawu a Yehova
Ku Filipi kunali mtsikana wina wantchito amene anali ndi chiwanda. Chiwandacho chinkachititsa kuti mtsikanayo azilosera zam’tsogolo ndipo ankalemeretsa mabwana ake. Ndiyeno Paulo ndi Sila atafika ku Filipiko, mtsikanayo ankawatsatira kwa masiku ambiri. Chiwandacho chinkamuchititsa kufuula kuti: “Anthu awa ndi akapolo a Mulungu Wam’mwambamwamba!” Paulo atatopa nazo anauza chiwandacho kuti: ‘Ndikukulamula m’dzina la Yesu kuti utuluke mwa mtsikanayu!’ Nthawi yomweyo chiwandacho chinamusiya.
Mabwana a mtsikanayu ataona kuti mwayi wawo wopeza ndalama watha, anakwiya kwambiri. Iwo anagwira Paulo ndi Sila n’kuwakokera kubwalo la olamulira ndipo anati: ‘Anthu awa akuphwanya malamulo ndipo akusokoneza kwambiri mzindawu.’ Ndiyeno akuluakulu a boma analamula kuti Paulo ndi Sila akwapulidwe kenako atsekeredwe m’ndende. Anawaika m’ndende yamdima kwambiri ndipo anawamangirira m’matangadza.
M’ndendemo, Paulo ndi Sila ankaimba nyimbo zotamanda Mulungu ndipo akaidi ena ankamvetsera. Ndiyeno pakati pa usiku, kunachitika chivomerezi chomwe chinagwedeza kwambiri ndendeyo. Zitseko zonse zinatseguka ndipo maunyolo a akaidi onse anamasuka. Woyang’anira ndende uja atathamanga n’kupeza kuti zitseko zatseguka anaganiza kuti akaidi onse athawa. Choncho anatenga lupanga kuti adziphe.
Koma Paulo anamuuza kuti: ‘Usadzivulaze! Tonse tili mommuno!’ Woyang’anira ndendeyo analowa msanga n’kugwada pafupi ndi Paulo ndi Sila. Kenako anafunsa kuti: ‘Ndichite chiyani kuti ndidzapulumuke?’ Iwo anamuyankha kuti: ‘Iweyo ndi banja lako muyenera kukhulupirira Yesu.’ Kenako Paulo ndi Sila anayamba kuphunzitsa woyang’anira ndendeyo ndi banja lake Mawu a Yehova ndipo onse anabatizidwa.
“Anthu adzakugwirani n’kukuzunzani ndipo adzakuperekani kumasunagoge ndi kundende. Adzakupititsani kwa mafumu ndi abwanamkubwa chifukwa cha dzina langa. Zimenezi zidzakupatsani mpata woti muchitire umboni.”—Luka 21:12, 13
-
-
Paulo, Sila ndi TimoteyoZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 100
Paulo ndi Timoteyo
Timoteyo anali m’bale wachinyamata mumpingo wa ku Lusitara. Bambo ake anali Mgiriki ndipo mayi ake anali Myuda. Timoteyo anaphunzira Mawu a Mulungu kuyambira ali wakhanda ndipo amene ankamuphunzitsa ndi mayi ake, a Yunike ndi agogo ake, a Loisi.
Paulo atafika ku Lusitara pa ulendo wake wachiwiri, anazindikira kuti Timoteyo amakonda kwambiri abale ndipo ali ndi mtima wofuna kuwathandiza. Choncho Paulo anapempha Timoteyo kuti aziyenda naye. Paulo anaphunzitsa Timoteyo kulalikira komanso kuphunzitsa uthenga wabwino mwaluso.
Mzimu woyera unkathandiza Paulo ndi Timoteyo kulikonse kumene ankapita. Tsiku lina usiku, Paulo anaona m’masomphenya munthu akumuuza kuti apite ku Makedoniya kukawathandiza. Choncho Paulo, Timoteyo, Sila ndi anthu ena anapita kukalalikira ku Makedoniya ndipo anakhazikitsa mipingo.
Atafika mumzinda wa Tesalonika, anthu ambiri anakhala Akhristu. Koma Ayuda ena ankachitira nsanje Paulo ndi anzakewo. Iwo anakopa gulu la anthu n’kutenga Paulo ndi anzakewo kupita nawo kwa olamulira a mzinda. Anthuwo ankafuula kuti: ‘Anthu awa ndi adani a boma la Roma!’ Apa moyo wa Paulo ndi Timoteyo unali pa ngozi choncho kutangoda iwo anathawira ku Bereya.
Anthu a ku Bereya anali ofunitsitsa kumvetsera uthenga wabwino ndipo Agiriki ndi Ayuda omwe, anakhala okhulupirira. Koma Ayuda amene anachokera ku Tesalonika atabwera anayambitsa chipolowe, ndiye Paulo anachoka kupita ku Atene. Timoteyo ndi Sila anatsala ku Bereya komweko kuti azilimbikitsa abale. Patapita nthawi, Paulo anatumiza Timoteyo ku Tesalonika kuti akalimbikitse abale kumeneko, omwe ankazunzidwa kwambiri. Kenako anamutumizanso kumipingo ina kuti akalimbikitse abale ndi alongo.
Paulo anauza Timoteyo kuti: ‘Amene akufuna kutumikira Yehova adzazunzidwa.’ Timoteyo anazunzidwa ndiponso kutsekeredwa m’ndende chifukwa chotumikira Mulungu. Iye ankaona kuti umenewu unali mwayi wake wosonyeza kuti ndi wokhulupirika kwa Yehova.
Paulo anauza Akhristu a ku Filipi kuti: ‘Ndakutumizirani Timoteyo kuti adzakuphunzitseni zoyenera kuchita potumikira Mulungu komanso polalikira.’ Paulo anachita zimenezi chifukwa chakuti Timoteyo anali wodalirika. Paulo ndi Timoteyo ankagwirizana kwambiri ndipo anatumikira Mulungu limodzi kwa zaka zambiri.
“Ndilibe wina amene ali ndi mtima ngati wake, amene angasamaliredi moona mtima zosowa zanu. Anthu ena onse akungoganizira zofuna zawo zokha, osati za Yesu Khristu.”—Afilipi 2:20, 21
-
-
Paulo Anatumizidwa ku RomaZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 101
Paulo Anatumizidwa ku Roma
Ulendo wachitatu wa Paulo unakathera ku Yerusalemu. Atafika kumeneko anamangidwa. Ndiyeno usiku anaona masomphenya. Yesu anamuuza kuti: ‘Udzapita ku Roma ndipo ukalalikira kumeneko.’ Paulo anatengedwa ku Yerusalemu kupita ku Kaisareya komwe anakakhala m’ndende zaka ziwiri. Pa nthawi imene mlandu wake unkazengedwa ndi bwanamkubwa wina dzina lake Fesito, Paulo ananena kuti: ‘Ndikupempha kuti mlandu wangawu ukaweruzidwe kwa Kaisara.’ Ndiyeno Fesito anati: “Popeza wachita apilo kuti ukaonekere kwa Kaisara, udzapitadi kwa Kaisara.” Popita ku Romako Paulo anatengedwa pa sitima yapamadzi ndipo abale awiri, Luka ndi Arisitako anapita nawo.
Ali panyanja kunachitika chimphepo choopsa kwa masiku ambiri. Aliyense ankaganiza kuti palibe amene apulumuke. Koma Paulo ananena kuti: ‘Anthu inu, mngelo wandiuza m’maloto kuti: “Usaope Paulo. Ukafika ku Roma ndipo aliyense musitimayi saafa.” Choncho musachite mantha. Palibe amene afe.’
Chimphepocho chinawomba kwa masiku 14. Kenako anayamba kuona chilumba cha Melita. Koma sitimayo inatitimira mumchenga ndipo inayamba kusweka chifukwa cha mafunde. Ngakhale zinali choncho, anthu onse 276 amene anali mmenemo anakafika kumtunda. Ena anasambira pomwe ena anagwiritsa ntchito zidutswa za sitimayo zomwe zinkayandama. Atafika, anthu apachilumbapo anawalandira bwino n’kuwayatsira moto kuti awothe.
Patapita miyezi itatu, asilikali anatenga Paulo pa sitima ina n’kupita naye ku Roma. Atafika, abale anabwera kudzamuona. Paulo atawaona anathokoza Yehova ndipo analimba mtima. Ngakhale kuti anali mkaidi, ankaloledwa kukhala m’nyumba ina ya lendi ndipo ankalonderedwa ndi msilikali. Iye anakhala kumeneko zaka ziwiri. Anthu akabwera kudzamuona, ankawalalikira za Ufumu wa Mulungu ndiponso za Yesu. Komanso iye analemba makalata opita kumipingo ya ku Asia Minor ndi ku Yudeya. Apatu Yehova anagwiritsa ntchito Paulo kuti uthenga wabwino ufike kwa anthu a mitundu ina.
“Tikusonyeza mʼnjira iliyonse kuti ndife atumiki a Mulungu. Tikuchita zimenezi popirira zinthu zambiri, pokumana ndi mavuto, pokhala opanda zinthu zofunika, pokumana ndi zinthu zovuta.”—2 Akorinto 6:4
-