Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 37 tsamba 90-tsamba 91 ndime 1
  • Yehova Analankhula ndi Samueli

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova Analankhula ndi Samueli
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Samueli Anapitirizabe Kuchita Zabwino
    Nsanja ya Olonda—2008
  • “Anapitiriza Kukula, Akukondedwa Ndi Yehova”
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • “Anapitiriza Kukula, Akukondedwa ndi Yehova”
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Samueli Anapitiriza Kuchita Zinthu Zabwino
    Phunzitsani Ana Anu
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 37 tsamba 90-tsamba 91 ndime 1
Samueli akutsegula chitseko cha chihema

MUTU 37

Yehova Analankhula ndi Samueli

Eli anali mkulu wa ansembe ndipo anali ndi ana awiri amene ankatumikira ngati ansembe kuchihema. Mayina awo anali Hofeni ndi Pinihasi. Anawa sankamvera malamulo a Yehova ndipo ankachitira anthu zoipa. Aisiraeli akabweretsa nsembe zoti apereke kwa Yehova iwo ankatengapo nyama yabwino n’kukadya. Eli anamva zimene ana akewa ankachita koma sanawathandize. Kodi Yehova anangoilekerera nkhaniyi?

Pa nthawiyo Samueli anali wamng’ono koma sanatengere makhalidwe oipawo ndipo Yehova ankasangalala naye. Tsiku lina atagona, Samueli anamva munthu akumuitana. Iye anadzuka n’kupita kwa Eli ndipo atafika anati: ‘Ndabwera.’ Koma Eli anati: ‘Inetu sindinakuitane. Pita ukagone.’ Samueli atabwerera anamvanso kuitana kachiwiri. Ulendo wachitatu, Eli anazindikira kuti amene akumuitana ndi Yehova. Ndiyeno anamuuza kuti akakamuitananso akayankhe kuti: ‘Lankhulani Yehova. Ine mtumiki wanu ndikumva.’

Samueli akuuza Eli zimene Yehova wamuuza

Samueli atapita kukagona anamvanso kuitana kuti: ‘Samueli! Samueli!’ Iye anayankha kuti: ‘Lankhulani, ine mtumiki wanu ndikumva.’ Ndiyeno Yehova anamuuza kuti: ‘Ukamuuze Eli kuti ndimulanga iyeyo ndi banja lake. Akudziwa zoipa zimene ana ake akuchita kuchihema koma akungowalekerera.’ Kutacha, Samueli anakatsegula zitseko za chihema ngati mmene ankachitira nthawi zonse. Iye ankaopa kuuza mkulu wa ansembe zimene Yehova ananena. Koma Eli anamuitana n’kumufunsa kuti: ‘Mwana wanga, kodi Yehova wakuuza kuti chiyani? Ndiuze chilichonse.’ Zitatero, Samueli anauza Eli zonse zimene Yehova ananena.

Yehova anapitirizabe kutsogolera Samueli. Anthu a m’dziko lonse la Isiraeli ankadziwa kuti Yehova anasankha Samueli kuti akhale mneneri komanso woweruza.

“Choncho kumbukira Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako.”​—Mlaliki 12:1

Mafunso: Kodi Samueli ankasiyana bwanji ndi Hofeni komanso Pinihasi? Kodi Yehova anauza Samueli kuti chiyani?

1 Samueli 2:12-17, 22-26; 3:1-21; 7:6

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena