Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 9 tsamba 28-tsamba 29 ndime 1
  • Anakhala Ndi Mwana Atakalamba

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anakhala Ndi Mwana Atakalamba
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Anamutchula Kuti “Mfumukazi”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Abrahamu ndi Sara Mungatsanzire Chikhulupiriro Chawo!
    Nsanja ya Olonda—2004
  • “Ndiwe Mkazi Wokongola”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 9 tsamba 28-tsamba 29 ndime 1
Sara akumvetsera ali mutenti pamene angelo akulankhula ndi Abulahamu

MUTU 9

Anakhala ndi Mwana Atakalamba

Abulahamu ndi Sara anali atakhala m’banja kwa zaka zambiri. Iwo anasiya nyumba yabwino ku Uri n’kumakhala m’matenti. Koma Sara sankadandaula chifukwa ankakhulupirira Yehova.

Sara ankafunitsitsa atakhala ndi mwana, moti anauza Abulahamu kuti: ‘Hagara, wantchito wangayu atakhala ndi mwana ndingamam’tenge ngati wanga.’ Patapita nthawi, Hagara anakhaladi ndi mwana wamwamuna. Dzina lake anali Isimaeli.

Sara ali ndi pakati

Patadutsa zaka zambiri, kunyumba kwa Abulahamu ndi Sara kunafika alendo atatu. Pa nthawiyi n’kuti Abulahamu ali ndi zaka 99 ndipo Sara anali ndi zaka 89. Abulahamu anaitanira alendowo pansi pa mtengo kuti apume ndipo anawakonzera chakudya. Kodi ukudziwa kuti alendowo anali ndani? Anali angelo. Mmodzi mwa angelowo anauza Abulahamu kuti: ‘Chaka chamawa nthawi ngati yomwe ino, iwe ndi mkazi wako mudzakhala ndi mwana wamwamuna.’ Sara ankamvetsera zimenezi ali mutenti ndipo anayamba kuseka. Iye ankaganiza kuti: ‘Koma zoona mmene ndakalambiramu ndingakhaledi ndi mwana?’

Koma chaka chotsatira, zimene mngelo wa Yehova uja ananena zinachitikadi. Sara anabereka mwana wamwamuna. Ndiyeno Abulahamu anamupatsa dzina loti Isaki, kutanthauza “Kuseka.”

Isaki ali ndi zaka 5, Sara anaona Isimaeli akumuseka Isakiyo. Pofuna kuteteza mwana wakeyo, anauza Abulahamu kuti athamangitse Hagara ndi Isimaeli. Poyamba, Abulahamu sankafuna kuchita zimenezi. Koma Yehova anamuuza kuti: ‘Mvera zimene Sara akunena. Ndidzasamalira Isimaeli koma zimene ndinakulonjeza zija zidzakwaniritsidwa kudzera mwa Isaki.’

Sara wagwira Isaki ndipo Hagara ndi Isimaeli akuchoka

“Chifukwa cha chikhulupiriro, Sara nayenso analandira mphamvu yokhala ndi pakati . . . chifukwa ankaona kuti wolonjezayo ndi wokhulupirika.”​—Aheberi 11:11

Mafunso: Kodi Sara anamva angelo akumuuza chiyani Abulahamu? Kodi Yehova anauza chiyani Abulahamu pofuna kuteteza Isaki?

Genesis 16:1-4, 15, 16; 17:25-27; 18:1-15; 21:1-14; Aheberi 11:11

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena