Indonesia
WERENGANI nkhani yosangalatsa yonena za Akhristu odzichepetsa amene anakhalabe olimba mtima pa nthawi imene ankakumana ndi mavuto. Iwo anakumana ndi mavutowa chifukwa cha kusintha kwa zinthu pa nkhani zandale, mikangano ya zipembedzo, komanso kuletsedwa kwa ntchito yawo kwa zaka 25 kumene atsogoleri azipembedzo anachititsa. Mupezanso nkhani ya m’bale amene dzina lake linali pa gulu la anthu omwe ankayenera kuphedwa ndi chipani cha Chikomyunizimu. Mulinso nkhani ya munthu wina yemwe poyamba anali mtsogoleri wa gulu lina la zigawenga koma panopa ndi Mkhristu wodalirika. Muwerenganso nkhani yosangalatsa ya atsikana awiri omwe ali ndi vuto losamva, amene anayamba kugwirizana kwambiri koma kenako anazindikira kuti ndi pachibale. Mudziwanso mmene ntchito ya anthu a Yehova ikuyendera pamene akulalikira uthenga wabwino kwa anthu ambiri omwe ndi achisilamu.