Pamene Kukhala Chete Kusonyeza Kuvomereza
Buku lakuti Betrayal—German Churches and the Holocaust (Chinyengo—Matchalitchi a ku Germany ndi Chipululutso cha Anazi) limafotokoza mosapita m’mbali zomwe chipembedzo chinkachita mu ulamuliro wa Nazi. “Kuchirikiza ulamuliro umenewo kwa Akristu sichinali chinthu chachilendo,” limatsimikizira motero bukulo, “anthu ochuluka kwabasi analephera kudzudzula kuzunzidwa kwa Ayuda. Choncho, kukhala chete kumeneku, kunatanthauza zambiri.”
N’chiyani chomwe chinakopa anthu odzinenera kukhala Akristu kugwirizana ndi ulamuliro wa Nazi? Bukulo limafotokoza kuti, ambiri anakopeka mtima ndi “mmene Hitler anali kuchitira ndi anthu a ku Germany, mwabata ndi mtendere.” Ilo limati: “Iye anali kuletsa mabuku osonyeza umaliseche, uhule, kuchotsa mimba, kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha, komanso ‘zonyansa’ zamakono, ndipo anali kupereka mamendulo opangidwa ndi bronze, siliva, kapena golide kwa akazi amene amabereka ana anayi, asanu ndi mmodzi, kapena asanu ndi atatu, ndipo pochita zimenezi anali kuŵalimbikitsa kuti asasiye miyambo yawo m’mabanja awo. Kuchirikiza miyambo kumeneku, limodzi ndi ulamuliro wa asilikali womwe Hitler anakhazikitsa pambuyo pakuti dzikolo laswa Pangano la ku Versailles, kunachititsa ambiri ngakhalenso Akristu ochuluka ku Germany, kusankha ulamuliro wa Nazi akumaona ngati umenewu ndiye unali wabwino.”
Mosiyana ndi ameneŵa, gulu limodzi linadzipatula kotheratu. Buku la Betrayal limati: “Mboni za Yehova zinakana kuchita ziwawa kapena kuloŵa m’magulu ankhondo.” Mosapeŵeka, zimenezi zinachititsa kuti gulu laling’ono limeneli aliukire mwankhanza, ndipo mamembala ake ambiri anaponyedwa m’ndende zachibalo. Komabe, ena odzinenera kukhala otsatira Kristu sanadzudzule zimenezi. Bukulo limapitiriza kunena kuti: “Akatolika ndi Apulotesitanti omwe anasonyeza udani waukulu kwa Mboni za Yehova osati kuzimvera chisoni, ndipo ankagwirizana kwambiri ndi mfundo zankhanza za Hitler m’malo motsutsa ziwawa ndi nkhondo monga momwe Mbonizo zinkachitira.” Mosakayikira, kukhala kwawo chete kunathandizira kuchitiridwa nkhanza kwa Mboni mu ulamuliro wa Nazi.
Ngakhale kuti kuloŵerera kwa matchalitchi m’ndale za Nazi kukupitirizabe kudzetsa mikangano yamphamvu, buku la Betrayal limatcha Mboni za Yehova kukhala “chipembedzo chomwe chinakana kuvomereza kapena kugwirizana ndi ulamuliro umenewo.”