Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/07 tsamba 5-6
  • Kodi Achinyamata Mukufuna Kuchita Chiyani Pamoyo Wanu?—Gawo 1

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Achinyamata Mukufuna Kuchita Chiyani Pamoyo Wanu?—Gawo 1
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 4/07 tsamba 5-6

Kodi Achinyamata Mukufuna Kuchita Chiyani Pamoyo Wanu?—Gawo 1

1 “Ndikufuna kukhala ndi moyo wabwino kwambiri.” Anatero mtsikana wina. Sitikukayikira kuti nanunso mukufuna moyo wabwino. Koma kodi mungatani kuti mukhale ndi moyo “wabwino kwambiri”? Olemba nkhani ndiponso anzanu, kapenanso aphunzitsi anu amene, anganene kuti munthu amakhala ndi moyo wabwino akakhala ndi ndalama zambiri ndiponso akamagwira ntchito yapamwamba.

2 Koma Baibulo limachenjeza achinyamata kuti kufunafuna chuma ndi “kungosautsa mtima.” (Mla. 4:4) Ndipotu ndi achinyamata ochepa chabe amene amakwanitsa kupeza chuma ndi kutchuka. Amene amakwanitsawo, amadzapeza kuti agwira fuwa la moto. Wachinyamata wina ku Britain amene anachita maphunziro apamwamba anati: “Zimakhala ngati wanyamula bokosi. Ukatsegula, umapeza mopanda kanthu.” Ndi zoona kuti nthawi zina, chifukwa cha ntchito, mungakhale achuma ndi otchuka. Koma singakupatseni ‘zosowa zanu zauzimu.’ (Mat. 5:3) Ndipotu lemba la 1 Yohane 2:17 limachenjeza kuti “dziko likupita.” Choncho, kaya mupeze chuma kapena kutchuka m’dzikoli, zimangokhala zakanthawi chabe.

3 Ndiye chifukwa chake lemba la Mlaliki 12:1 limalimbikitsa achinyamata kuti: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako.” Zoonadi, mungathe kukhala ndi moyo wabwino ngati mukutumikira Yehova Mulungu. Koma pali zimene mufunika kuchita kaye musanayambe kutumikira Mulungu. Kodi muyenera kuchita chiyani? Ndipo kodi moyo wotumikira Mulungu umafuna chiyani?

4 Zimene Mungachite Kuti Mukhale wa Mboni za Yehova: Choyamba muyenera kukhala ndi cholinga chotumikira Mulungu, ndipo cholinga chimenecho sichibwera chokha, ngakhale makolo anu atakhala kuti ndi Akhristu. Inuyo panokha muyenera kukhala bwenzi la Yehova. Mtsikana wina anati: “Pemphero limathandiza kuti munthu akhale bwenzi la Yehova.”—Sal. 62:8; Yak. 4:8.

5 Lemba la Aroma 12:2 limatchula chinthu china chimene muyenera kuchita. Limati: “Muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino ndi chovomerezeka ndi changwiro.” Kodi nthawi zina mumakayikira zinthu zimene mwaphunzitsidwa? Ngati ndi choncho, mufunikira kuti “muzindikire” kuti zimenezi ndi zoona, monga mmene Baibulo latilangizira. Chitani kafukufuku. Werengani Baibulo ndi mabuku olifotokoza. Ngakhale zili choncho, kudziwa Mulungu si nkhani yongowerenga ayi. Kumafunanso kusinkhasinkha zinthu zimene mukuwerenga kuti zilowerere mu mtima mwanu. Mukamatero, mudzayamba kukonda Mulungu kwambiri.—Sal. 1:2, 3.

6 Chinthu chinanso chimene muyenera kuchita ndicho kuuzako ena zimene mukuphunzira mukapeza mpata, mwina kusukulu. Kenako mungayambe kulalikira khomo ndi khomo. N’kutheka kuti nthawi zina mungakumane ndi mnzanu wa kusukulu ndipo mungachite mantha kumulalikira. Koma Baibulo limatiuza kuti ‘tisachite nawo manyazi uthenga wabwino.’ (Aroma 1:16) N’kuchitiranji manyazi pamene mukuwapititsira uthenga wopatsa moyo ndi chiyembekezo?

7 Ngati makolo anu ndi Akhristu, mwina mumapita nawo limodzi kokalalikira. Kodi mumangowaperekeza osalankhulapo chilichonse kapena mumangogawira magazini ndi timapepala? Kodi mukafika pa khomo, mumatha kulankhula ndi munthu kumuuza mfundo za m’Baibulo? Ngati simutero, pemphani makolo anu kapena anthu ena mumpingo kuti akuthandizeni. Yesetsani kuti mukhale wofalitsa wosabatizidwa wa uthenga wabwino.

8 Patapita nthawi mudzafuna kudzipereka, kutanthauza kulonjeza Mulungu mochita kulumbira kuti mukufuna kuyamba kumutumikira. (Aroma 12:1) Koma kudzipereka si nkhani imene mumangochita mu mtima mwanu ayi. Mulungu amafuna kuti tonse ‘tilengeze poyera chikhulupiriro chathu kuti tipulumuke.’ (Aroma 10:10) Nthawi imene mukukabatizidwa, mumayamba ndi kulengeza ndi pakamwa chikhulupiriro chanu. Kenako mumabatizidwa m’madzi. (Mat. 28:19, 20) Ndi zoona kuti ubatizo ndi nkhani yaikulu. Koma musachite mantha kubatizidwa chifukwa choganiza kuti mungadzalakwe. Mukadalira Mulungu, iye adzakupatsani “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti ikuthandizeni kulimba.—2 Akor. 4:7; 1 Pet. 5:10.

9 Nthawi imene mwabatizidwa, mumakhala wa Mboni za Yehova. (Yes. 43:10) Apa ndiye pamasinthira moyo wanu. Kudzipereka kumatanthauza ‘kudzikana nokha.’ (Mat. 16:24) Mumasiya zolinga zanu zina ndi ‘kuyamba kufuna ufumu wa Mulungu.’ (Mat. 6:33) Choncho, mukadzipereka ndi kubatizidwa, mumakhala ndi mwayi wochita zimenezi. Gawo 2 la nkhani ino lidzafotokoza zimene mungachite kuti mutumikire Mulungu muutumiki wa nthawi zonse.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena