MAFUNSO KWA ANTHU AMENE AKUFUNA KUBATIZIDWA
Chigawo Chachiwiri: Moyo Wachikhristu
Kuphunzira Baibulo kwakuthandizani kudziwa zimene Yehova amafuna kuti muzichita ndiponso mmene mungazichitire. Zimene mwaphunzira zachititsa kuti musinthe khalidwe lanu komanso mmene mumaonera moyo. Popeza panopa mwatsimikiza mtima kuti muzitsatira mfundo zolungama za Yehova, ndinu woyenerera kukhala mtumiki wa uthenga wabwino.
Kukambirana mafunso otsatirawa kukuthandizani kuti mumvetse bwino zimene Yehova amafuna komanso kukukumbutsani zinthu zina zimene mungachite kuti mukhale mtumiki wake wovomerezeka. Mfundo zimenezi zikuthandizani kuona kufunika kochita zinthu zonse ndi chikumbumtima chabwino komanso kulemekeza Yehova.—2 Akor. 1:12; 1 Tim. 1:19; 1 Pet. 3:16, 21.
Pofika pano, n’zosakayikitsa kuti mukufunitsitsa kugonjera ulamuliro wa Yehova komanso kukhala m’gulu lake. Mafunso amenewa komanso malembawo akuthandizani kudzifufuza kuti muone ngati mukumvetsa bwino nkhani yogonjera dongosolo la Yehova mumpingo, m’banja, komanso maboma a m’dzikoli. Akuthandizaninso kuona kuti dongosolo limene Yehova anakonza lophunzitsira anthu ake komanso kuwalimbikitsa mwauzimu ndi lofunika kwambiri. Zimenezi zikuphatikizapo misonkhano ya mpingo yomwenso muyenera kupezekapo kupatulapo ngati pali vuto lalikulu.
Komanso m’chigawochi muli mfundo zokhudza kufunika kogwira nawo ntchito yolalikira za Ufumu nthawi zonse, zomwe zimathandiza ena kudziwa Yehova komanso zimene akuchitira anthu. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Chigawochi chikuthandizaninso kuzindikira kuti kudzipereka kwa Yehova komanso kubatizidwa ndi nkhani yaikulu. Musamakayikire kuti Yehova amaona kuti zimene mukuchita posonyeza kuyamikira kukoma mtima kwakukulu kumene wakusonyezani, ndi zofunika kwambiri.
1. Kodi Akhristu amauona bwanji ukwati? Kodi ndi chifukwa chimodzi chiti cha m’Malemba chomwe munthu angathetsere banja?
• “Kodi simunawerenge kuti amene analenga anthu pa chiyambi pomwe anawalenga mwamuna ndi mkazi n’kunena kuti, ‘Pa chifukwa chimenechi mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi’? Chotero salinso awiri, koma thupi limodzi. Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse. . . . Aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatira wina wachita chigololo, kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha dama.”—Mat. 19:4-6, 9.
2. N’chifukwa chiyani anthu amene akukhala limodzi ngati mwamuna ndi mkazi ayenera kukwatirana mwalamulo? Ngati muli pa banja, kodi munakwatirana mwalamulo ndipo ukwati wanu ndi wovomerezeka ndi boma?
• “Pitiriza kuwakumbutsa kuti azigonjera ndi kumvera maboma ndiponso olamulira.”—Tito 3:1.
• “Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatirana pakhale posaipitsidwa, pakuti Mulungu adzaweruza adama ndi achigololo.”—Aheb. 13:4.
. Kodi udindo wanu ndi wotani m’banja?
• “Mwana wanga, tamvera malangizo a bambo ako, ndipo usasiye malamulo a mayi ako.”—Miy. 1:8.
• “Mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake monganso mmene Khristu alili mutu wa mpingo . . . Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu monga mmene Khristu anakondera mpingo.”—Aef. 5:23, 25.
• “Abambo, musamapsetse mtima ana anu, koma muwalere m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.”—Aef. 6:4.
• “Ananu, muzimvera makolo anu pa zinthu zonse, pakuti kuchita zimenezi kumakondweretsa Ambuye.”—Akol. 3:20.
• “Akazi, muzigonjera amuna anu.”—1 Pet. 3:1.
4. N’chifukwa chiyani tiyenera kulemekeza moyo?
• “[Mulungu] amapatsa anthu onse moyo, mpweya, ndi zinthu zonse. . . . Pakuti chifukwa cha iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.”—Mac. 17:25, 28.
5. N’chifukwa chiyani sitiyenera kupha munthu aliyese, kuphatikizapo mwana wosabadwa?
• “Amuna akamamenyana ndipo avulaza kwambiri mkazi wapakati, . . . ngati wina wamwalira, pamenepo uzipereka moyo kulipira moyo.”—Eks. 21:22, 23.
• “Maso anu anandiona pamene ndinali mluza, ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu. M’bukumo munalembamo za masiku amene zinapangidwa koma panalibe ngakhale chiwalo chimodzi chimene chinali chitapangidwa.”—Sal. 139:16.
• ‘Yehova amadana ndi manja okhetsa magazi a anthu osalakwa.’—Miy. 6:16, 17.
6. Kodi lamulo la Mulungu pa nkhani ya magazi ndi lotani?
• ‘Kupitiriza kupewa magazi ndi zopotola.’—Mac. 15:29.
7. N’chifukwa chiyani tiyenera kukonda abale ndi alongo athu?
• “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana. Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.”—Yoh. 13:34, 35.
8. N’chifukwa chiyani munthu amene ali ndi matenda opatsirana sayenera (a) Kusonyeza ena chikondi powakumbatira kapena kuwapsompsona? (b) Kukhumudwa ngati ena sakumuitana kunyumba zawo? (c) N’chifukwa chiyani munthu amene akudzikayikira kuti mwina angakhale ali ndi matenda opatsirana, ayenera kukayezetsa kaye magazi asanayambe kuchita chibwenzi? (d) N’chifukwa chiyani munthu amene ali ndi matenda opatsirana ayenera kudziwitsa wogwirizanitsa ntchito za akulu asanakabatizidwe?
• “Musamakhale ndi ngongole iliyonse kwa munthu aliyense, kusiyapo kukondana. . . . ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’ Chikondi sichilimbikitsa munthu kuchitira zoipa mnzake.”—Aroma 13:8-10.
• “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”—Afil. 2:4.
9. N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti tizikhululukira ena?
• “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake. Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni.”—Akol. 3:13.
10. Kodi mungatani ngati m’bale wakunenerani miseche kapena wakuchitirani zachinyengo?
• “Ngati m’bale wako wachimwa, upite kukam’fotokozera cholakwacho panokha iwe ndi iyeyo. Ngati wakumvera, ndiye kuti wabweza m’bale wakoyo. Koma akapanda kukumvera, upiteko ndi munthu wina mmodzi kapena awiri, kuti nkhani yonse ikatsimikizike ndi pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu. Akapanda kuwamvera amenewanso, uuze mpingo. Ndipo akapandanso kumvera mpingowo, kwa iwe akhale ngati munthu wochokera mu mtundu wina komanso ngati wokhometsa msonkho.”—Mat. 18:15-17.
11. Kodi Yehova amaona bwanji machimo otsatirawa?
▪ Dama
▪ Kugwiritsa ntchito zifaniziro polambira
▪ Kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha
▪ Kuba
▪ Juga
▪ Kuledzera
• “Musasocheretsedwe. Adama, opembedza mafano, achigololo, amuna amene amagonedwa ndi amuna anzawo, amuna ogona amuna anzawo, akuba, aumbombo, zidakwa, olalata, kapena olanda, onsewo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.”—1 Akor. 6:9, 10.
12. Kodi mwatsimikiza kuchita chiyani pa nkhani ya dama, lomwe limaphatikizapo mtundu uliwonse wa kugonana ndi munthu amene sunakwatirane naye?
• “Thawani dama.”—1 Akor. 6:18.
13. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa mankhwala osokoneza bongo?
• “Mupereke matupi anu ngati nsembe yamoyo, yoyera ndi yovomerezeka kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika mwa kugwiritsa ntchito luntha la kuganiza. Musamatengere nzeru za nthawi ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.”—Aroma 12:1, 2.
14. Tchulani zinthu zina zokhudza kukhulupirira mizimu zimene Mulungu amaletsa.
• “Pakati panu pasapezeke munthu wotentha mwana wake pamoto, wolosera, wochita zamatsenga, woombeza, wanyanga, kapena wolodza ena, aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu, wolosera zam’tsogolo kapena aliyense wofunsira kwa akufa.”—Deut. 18:10, 11.
15. Ngati munthu wachita tchimo lalikulu ndipo akufuna kukhalanso pa ubwenzi ndi Yehova, kodi ayenera kuchita chiyani mwansanga?
• “Ndinaulula tchimo langa kwa inu, ndipo sindinabise cholakwa changa. Ndinati: ‘Ndidzaulula kwa Yehova machimo anga.’”—Sal. 32:5.
• “Kodi pali wina amene akudwala pakati panu? Aitane akulu a mpingo, ndipo iwo amupempherere ndi kumupaka mafuta m’dzina la Yehova. Pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa wodwalayo, ndipo Yehova adzamulimbitsa. Ndiponso ngati anachita machimo, adzakhululukidwa.”—Yak. 5:14, 15.
16. Ngati mwadziwa kuti Mkhristu mnzanu wachita tchimo lalikulu, kodi muyenera kutani?
• “Munthu akaona wina akuchita tchimo, kapena wamva kuti wina wachita tchimo, munthu ameneyo ndi mboni. Akamva chilengezo kuti akachitire umboni za wochimwayo koma iye osapita kukanena, ndiye kuti wachimwa. Ayenera kuyankha mlandu wa cholakwa chakecho.”—Lev. 5:1.
17. Ngati paperekedwa chilengezo choti wina wachotsedwa ndipo salinso wa Mboni za Yehova, kodi tiyenera kumachita naye bwanji zinthu?
• “Muleke kuyanjana ndi aliyense wotchedwa m’bale, amene ndi wadama, kapena waumbombo, kapena wopembedza mafano, wolalata, chidakwa, kapena wolanda, ngakhale kudya naye munthu wotereyu ayi.”—1 Akor. 5:11.
• “Wina akabwera kwa inu ndi chiphunzitso chosiyana ndi ichi, musamulandire m’nyumba zanu kapena kumupatsa moni.”—2 Yoh. 10.
18. N’chifukwa chiyani anzanu apamtima ayenera kukhala anthu amene amakonda Yehova?
• “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.”—Miy. 13:20.
• “Musasocheretsedwe. Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.”—1 Akor. 15:33.
19. N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova salowerera ndale?
• “Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine [Yesu] sindili mbali ya dziko.”—Yoh. 17:16.
20. N’chifukwa chiyani muyenera kumvera boma?
• “Munthu aliyense azimvera olamulira akuluakulu, chifukwa palibe ulamuliro umene ungakhalepo kupatulapo ngati Mulungu waulola. Olamulira amene alipowa ali m’malo awo osiyanasiyana mololedwa ndi Mulungu.”—Aroma 13:1.
21. Ngati lamulo la anthu likusemphana ndi lamulo la Mulungu, kodi mungatani?
• “Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”—Mac. 5:29.
22. Kodi ndi malemba ati amene angakuthandizeni kukhalabe wosiyana ndi dziko mukamasankha ntchito?
• “Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.”—Mika 4:3.
• “Tulukani mwa iye [Babulo Wamkulu] anthu anga, ngati simukufuna kugawana naye machimo ake, ndiponso ngati simukufuna kulandira nawo ina ya miliri yake.”—Chiv. 18:4.
23. Kodi ndi zosangalatsa ziti zimene mungasankhe, nanga ndi ziti zomwe mungapewe?
• “Yehova . . . amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa.”—Sal. 11:5.
• “Nyansidwani ndi choipa, gwiritsitsani chabwino.”—Aroma 12:9.
• “Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambiri, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zachikondi, zilizonse zoyamikirika, khalidwe labwino lililonse, ndi chilichonse chotamandika, pitirizani kuganizira zimenezi.”—Afil. 4:8.
24. N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova sachita mapemphero pamodzi ndi zipembedzo zina?
• “Sizingatheke kuti muzidya ‘patebulo la Yehova’ komanso patebulo la ziwanda.”—1 Akor. 10:21.
• “‘Lekanani nawo,’ watero Yehova. ‘Musakhudze chinthu chodetsedwa,’ ‘ndipo ndidzakulandirani.’”—2 Akor. 6: 17.
25. Kodi ndi mfundo ziti zimene zingakuthandizeni kudziwa ngati mukuyenera kuchita nawo chikondwerero chinachake?
• “Anayamba kusakanikirana ndi mitundu ina, ndi kuyamba kuphunzira zochita zawo. Anayamba kutumikira mafano awo, ndipo mafanowo anakhala msampha wawo.”—Sal. 106:35, 36.
• “Akufa sadziwa chilichonse.”—Mlal. 9:5.
• “Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.”—Yoh. 17:16.
• “Nthawi imene yapitayi inali yokwanira kwa inu kuchita chifuniro cha anthu a m’dzikoli pamene munali kuchita zinthu zosonyeza khalidwe lotayirira, zilakolako zoipa, kumwa vinyo mopitirira muyezo, maphwando aphokoso, kumwa kwa mpikisano, ndi kupembedza mafano kosaloleka.”—1 Pet. 4:3.
26. Kodi zitsanzo za m’Baibulo zimakuthandizani bwanji kudziwa ngati kuli koyenera kuti muzikondwerera masiku obadwa?
• “Tsiku lachitatulo linafika, ndipo linali tsiku lokumbukira kubadwa kwa Farao. Mfumuyo inakonzera phwando antchito ake onse. Pa tsikuli, Farao anatulutsa m’ndende mkulu wa operekera chikho ndi mkulu wa ophika mkate, n’kuwaimika pamaso pa antchito ake onse. Farao anabwezeradi pa ntchito mkulu wa operekera chikho uja . . . Koma mkulu wa ophika mkate anam’pachika.”—Gen. 40:20-22.
• “Tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode litafika, mwana wamkazi wa Herodiya anavina pa tsikulo ndipo anasangalatsa Herode kwambiri, mwakuti analonjeza molumbira kuti adzapatsa mtsikanayo chilichonse chimene angapemphe. Tsopano mtsikanayu, mayi wake atachita kum’pangira, anapempha kuti: ‘Ndipatseni mutu wa Yohane M’batizi m’mbale pompano.’ Choncho anatuma munthu kukadula mutu wa Yohane m’ndende.”—Mat. 14:6-8, 10.
27. N’chifukwa chiyani mukufuna kumatsatira malangizo a akulu?
• “Muzimvera amene akutsogolera pakati panu ndipo muziwagonjera. Iwo amayang’anira miyoyo yanu monga anthu amene adzayankhe mlandu. Muziwamvera ndi kuwagonjera kuti agwire ntchito yawo mwachimwemwe, osati modandaula, pakuti akatero zingakhale zokuvulazani”—Aheb. 13:17.
28. N’chifukwa chiyani n’zofunika kwambiri kuti inuyo ndi banja lanu muzikhala ndi nthawi yophunzira Baibulo nthawi zonse?
• “Amakondwera ndi chilamulo cha Yehova, ndipo amawerenga ndi kusinkhasinkha chilamulo chake usana ndi usiku. Munthu ameneyo adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m’mphepete mwa mitsinje ya madzi, umene umabala zipatso m’nyengo yake, umenenso masamba ake safota, ndipo zochita zake zonse zidzamuyendera bwino.”—Sal. 1:2, 3.
29. N’chifukwa chiyani mumakonda kupezeka pamisonkhano komanso kutengapo mbali?
• “Ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga. Ndidzakutamandani pakati pa mpingo.”—Sal. 22:22.
• “Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezere kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.”—Aheb. 10:24, 25.
30. Kodi ntchito yofunika kwambiri imene Yesu anatipatsa ndi iti?
• “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza . . . , ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.”—Mat. 28:19, 20.
31. Tikamapereka zopereka zothandiza pa ntchito ya Ufumu kapena tikamathandiza abale ndi alongo athu, kodi tiyenera kukhala ndi mtima wotani umene umasangalatsa Yehova?
• “Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali.”—Miy. 3:9.
• “Aliyense achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika kapena mokakamizika, chifukwa Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.”—2 Akor. 9:7.
32. Kodi Akhristu amayembekezera kukumana ndi mavuto ati?
• “Odala ndi anthu amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo, pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo. “Ndinu odala pamene anthu akukunyozani ndi kukuzunzani, komanso kukunamizirani zoipa zilizonse chifukwa cha ine. Kondwerani, dumphani ndi chimwemwe, chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba, pakuti umu ndi mmenenso anazunzira aneneri amene analipo inu musanakhaleko.”—Mat. 5:10-12.
33. N’chifukwa chiyani ndi mwayi waukulu kubatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova?
• “Mawu anu amandikondweretsa ndi kusangalatsa mtima wanga, pakuti ine ndimatchedwa ndi dzina lanu, inu Yehova Mulungu.”—Yer. 15:16.