Kodi Mumaona Kuti Anthu Sakumvetsetsani?
ANTONIO anadabwa pamene mwadzidzidzi, mnzake weniweni Leonardo, anasiya kucheza naye popanda chifukwa.a Nthaŵi zina sankayankha akamupatsa moni, ndipo akakhala limodzi, sankachezanso momasuka. Antonio anachita mantha kuti mwina anachita kanthu kena kapena kulankhula zomwe mnzakeyo anaziganizira molakwa. Kodi analakwa chiyani?
Kusamvetsetsana n’kofala. Kaŵirikaŵiri kumakhala kochepa ndipo sikuvuta kukuthetsa. Nthaŵi zina kumakhala kokhumudwitsa, makamaka pamene maganizo olakwika akupitirizabe ngakhale kuti mwayesetsa kuwathetsa. N’chifukwa chiyani pamakhala kusamvetsetsana? Kodi kumawakhudza motani anthuwo? Mungatani pamene ena aganizira molakwika zimene munachita? Ndipo kodi zimene anthu amakuganizirani zili n’kanthu?
Kusamvetsetsana N’kosapeweka
Popeza kuti anthu sangathe kuona maganizo ndi zolinga zathu, ena adzatiganizirabe molakwa pa zomwe tanena kapena kuchita. Pali zambiri zomwe zingapangitse kusamvetsetsana. Nthaŵi zina timalephera kufotokoza malingaliro athu momveka bwino ndi molunjika. Phokoso ndi zosokoneza zina, zingapangitse ena kuvutika kuti atimvetsere mwa chidwi.
Makhalidwe ndi zochita zina, kaŵirikaŵiri zimapangitsa kuganizirana molakwa. Mwachitsanzo, munthu wofatsa, tingam’ganizire kuti ndi wosachezeka, wodzikonda, kapena wonyada. Zomwe tinakumana nazo kale zingatipangitse kukhala wopupuluma m’malo modekha pakachitika zinthu zina. Kusiyana kwa chikhalidwe ndi zinenero kumapangitsa kumvetsetsana kukhala kovuta. Kuwonjezera apo, palinso nkhani zosalondola kwenikweni ndi miseche. Choncho sitiyenera kudabwa pamene anthu ena aona zimene tachita kapena kunena mosiyana ndi cholinga chathu. Inde, zonsezi sizitonthoza mokwanira anthu amene akuona kuti sanamvetsetsedwe.
Mwachitsanzo, Anna ananena mawu abwinobwino za kutchuka kwa mnzake yemwe panalibe. Kenako mawuwo anapotozedwa, ndipo Anna anadabwa ndi kusoŵeratu chochita pamene mnzakeyo mokwiya amam’nena pagulu kuti amachita nsanje ndi chidwi chomwe mwamuna wina ali nacho pa mnzakeyo. Mawu a Anna anawamva molakwa kwambiri, ndipo kuyesetsa kwake kufotokozera mnzakeyo kuti sanatanthauze zimenezo sikunapindule kanthu. Zimenezo zinali zopweteka kwambiri ndipo panapita nthaŵi yaitali kuti Anna athetseretu kusam’mvetsa kumeneko.
Mmene anthu amakuganizirani, ndi mmenenso amakuonerani. Ndiye n’kwachibadwa kukhumudwa ngati anthu akukuganizirani molakwa. Mwina mungakwiye poganiza kuti palibe chifukwa choti wina akumvereni molakwa. Kwa inu kumeneko kungakhale kungokudani chabe, kukunyazitsani ndiponso kukulakwirani. Zimenezi zingakupwetekeni kwambiri makamaka ngati mumalemekeza zonena za anthu amene akukugazirani molakwawo.
Ngakhale kuti mungaipidwe ndi mmene ena amakuonerani, n’koyenera ndithu kulemekeza malingaliro a anthu ena. Mkristu sayenera kunyalanyaza zimene ena amaganiza. Ndipo sitifuna kuti zonena kapena zochita zathu zikhale zopweteka ena. (Mateyu 7:12; 1 Akorinto 8:12) Choncho nthaŵi zina mungafunikire kuyesetsa kuthetsa maganizo oipa omwe munthu wina ali nawo pa inu. Komabe, kukhala ndi nkhaŵa yaikulu kuti ena akukondeni n’kosapindulitsa, ndipo kungakutaitseni ulemu wanu kapenanso mungadzimve kuti ndinu wosafunika. Ndiponsotu kukhala munthu wabwino sikudalira zimene anthu ena amakuganizirani.
Nthaŵi zina, mungazindikire kuti zomwe anthu amakunenerani n’zoona. Zimenezonso n’zowawa. Koma ngati mofunitsitsa ndi moona mtima muzindikira zofooka zanu, zimenezo zingakupindulitseni kwambiri ndipo zingakusonkhezereni kuti musinthe.
Kuipa kwa Kusamvetsetsana
Kusamvetsetsana kungakhale ndi zotsatira zoipa kapena ayi. Mwachitsanzo, ngati muli mu lesitilanti ndiye munthu wina akulankhula mokweza, mungaganize kuti mwina ndi womasuka kwambiri ndi anthu kapena wodzitama. Koma mwina si choncho. N’kutheka kuti munthu yemwe akulankhula nayeyo samva mokwanira. Kapena mungaone kuti wogulitsa m’sitolo ndi wosasangalala, koma mwina n’chifukwa chakuti kasitomala wina sanamulankhule bwino. Ngakhale kuti kuganizirana molakwa kotereku kumapangitsa anthu kukhala ndi malingaliro olakwika, sikukhala ndi zotsatira zoopsa kapena zokhalitsa. Koma nthaŵi zina, kusamvetsetsana kungakhale ndi zotsatira zoopsa kwambiri. Taganizirani zochitika ziŵiri m’mbiri ya Israyeli wakale.
Pamene Nahasi, mfumu ya Amoni anamwalira, Davide anatumiza anthu kukapereka uthenga wopepesa kwa Hanuni mwana wake yemwe anayamba kulamulira m’malo mwa atate ake. Koma molakwa, a Amoni anaganiza kuti alendowo anali akazitape odzazonda dziko lawo. Chotero Hanuni anawanyazitsa alendowo ndipo kenako anachita nkhondo ndi Aisrayeli. Zotsatira zake, anthu pafupifupi 47,000 anafa chifukwa cha kuganizira molakwa cholinga chabwinobwino.—1 Mbiri 19:1-19.
M’mbuyomo zimenezi zisanachitike kusamvetsana kwina kunathetsedwa mosavuta m’mbiri ya Israyeli. Mafuko a Rubeni, Gadi ndiponso fuko la Manase logaŵika pakati anamanga guwa lalikulu la nsembe m’mphepete mwa mtsinje wa Yordano. Mafuko ena onse a Aisrayeli anaona guwalo monga chisonyezero cha kusakhulupirika ndiponso kupandukira Yehova. Choncho anakonzekera kuwathira nkhondo. Asanachite chilichonse, Aisrayeli enawa anatumiza nthumwi zawo kukafotokoza kuipidwa kwawo pa kusakhulupirika komwe enawo anachita. Anachita bwino kukafunsa, pakuti omanga guwawo anati analibe cholinga chilichonse chofuna kusiya kulambira koyera. Koma kuti guwalo linali chowakumbutsa kukhala okhulupirika kwa Yehova. Kusamvetsana kumeneku kukanaphetsa anthu ambiri, koma nzeru inapangitsa kuti zotsatira zoopsazo zipeŵedwe.—Yoswa 22:10-34.
Kambiranani Mwachikondi
Tikuphunzirapo kanthu pa zochitika zimenezi. N’zoonekeratu kuti kukambirana ndiko kwanzeru. M’nkhani yomalizayi, ndani angadziŵe kuchuluka kwa anthu omwe anapulumuka chifukwa chakuti mbali ziŵirizi zinakambirana? Nthaŵi zambiri, miyoyo sikhala pangozi mukalephera kumvetsetsa zolinga za munthu wina, koma maubwenzi angakhale pangozi. Choncho, ngati mukuona kuti wina wakulakwirani, kodi ndinu wotsimikiza kuti mwamvetsetsadi mmene zinthu zilili kapena mukungoganizira molakwa? Kodi cholinga chake chinali chotani? Mufunseni. Kodi mukuona kuti sanakumvetseni? Kambiranani. Musalole kuti kudzikuza kuwononge zinthu.
Yesu anapereka malangizo abwino kwambiri osonkhezera kuthetsa kusamvetsetsana. Iye anati: “Chifukwa chake ngati ulikupereka mtulo wako pa guwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe, usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nuchoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.” (Mateyu 5:23, 24) Choncho, choyenera kuchita ndicho kutengera pambali munthuyo osaloŵetsapo ena. Ngati munthuyo choyamba angamve dandaulo lanu kuchokera kwa ena, nkhaniyo ingaipe. (Miyambo 17:9) Cholinga chanu chiyenera kukhala kukhazikitsa mtendere mwachikondi. Modekha, fotokozani vutolo momveka bwino mosaimba mnzanuyo mlandu. Fotokozani mmene mukumvera. Ndiyeno mvetserani mwachidwi maganizo a mnzanuyo. Musafulumire kuganiza kuti chinali cholinga chake. Khalani wokonzeka kukhulupirira zimene akunena. Kumbukirani, chikondi “chikhulupirira zinthu zonse.”—1 Akorinto 13:7.
Inde ngakhale kuti kusamvetsetsana kungathetsedwe, kukhumudwa kungakhalepobe. Ndiyeno tingatani? Ngati n’koyenera, kupepesa kochokera pansi pa mtima n’kofunika, ngakhalenso kuchita chilichonse chomwe chingathandize kukonza zinthu. Nthaŵi zonse, wolakwiridwayo angachite bwino kutsatira uphungu wouziridwa wakuti: Pitirizani “kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.”—Akolose 3:13, 14; 1 Petro 4:8.
Popeza kuti ndife opanda ungwiro, kusamvetsetsana ndi kukhumudwitsana kudzakhalapobe. Aliyense angalakwe kapena kulankhula mosaganizira bwino ndi mopanda chikondi. Baibulo limati: “Timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mawu, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse.” (Yakobo 3:2) Poti Yehova Mulungu akudziŵa zimenezi, watipatsa malangizo awa: “Usakangaze mumtima mwako kukwiya; pakuti mkwiyo ugona m’chifuwa cha zitsiru. Mawu onsetu onenedwa usawalabadire; kuti usamve kapolo wako alikukutemberera; pakuti kaŵirikaŵiritu mtima wako udziŵa kuti nawenso unatemberera ena.”—Mlaliki 7:9, 21, 22.
“Yehova Ayesa Mitima”
Nanga bwanji ngati zikuoneka kuti n’kosatheka kuthetsa maganizo oipa a munthu wina pa inu? Musade nkhaŵa. Pitirizanibe kukulitsa ndi kusonyeza mikhalidwe yachikristu mmene mungathere. M’pempheni Yehova kuti akuthandizeni kukonza mbali zimene m’malakwitsa. Umunthu wanu weniweni sudalira pa zimene anthu amakuganizirani. Ndi Yehova yekha yemwe ‘angayese mitima’ molondola. (Miyambo 21:2) Nayenso Yesu anthu sanamuone monga wofunika ndipo anam’nyoza. Koma zimenezo sizinasinthe mmene Yehova anali kumuonera. (Yesaya 53:3) Ngakhale kuti ena angakuganizireni molakwa, mungathe ‘kutsanulira mtima wanu’ kwa Yehova ndi chikhulupiriro chakuti amakumvetsani “pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang’ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.” (Salmo 62:8; 1 Samueli 16:7) Ngati mupitirizabe kuchita chabwino, amene amakuonani ndi maganizo oipa m’kupita kwa nthaŵi angazindikire kulakwa kwawo ndi kusintha maganizo awo.—Agalatiya 6:9; 2 Timoteo 2:15.
Kodi mukum’kumbukira Antonio kumayambiriro kwa nkhani ino? Iye analimba mtima kutsatira malangizo a m’Malemba. Analankhula ndi mnzake uja Leonardo kum’funsa chomwe anam’lakwira. Koma Leonardo anadabwa kwambiri. Iye anam’yankha Antonio kuti palibe chomwe anam’lakwira ndipo anam’tsimikizira kuti analibe cholinga chothetsa ubwenzi wawo. Ngati ankaoneka wosachezekanso, mwina n’chifukwa chakuti anali wotanganidwa kwambiri. Leonardo anapepesa kuti anakhumudwitsa mnzakeyo mosazindikira ndipo anam’thokoza chifukwa chom’funsa. Iye anatinso, akhala wosamala kuti asadzateronso kwa ena m’tsogolo. Nkhaŵa yonse inatheratu, ndipo ubwenzi wawo unapitirizabe monga kale.
Kuganiziridwa molakwa n’kosasangalatsa m’pang’ono pomwe. Komabe, ngati mutayesetsa kukuthetsa ndi kugwiritsa ntchito malangizo a m’Malemba a chikondi ndi kukhululukirana, n’kotheka kuti inunso mupeze zotsatira zabwino.
[Mawu a M’munsi]
a Mayina ena asinthidwa m’nkhani ino.
[Zithunzi patsamba 23]
Kukambirana mwachikondi ndiponso kukhululuka kungadzetse mtendere