-
Uthenga Wopita kwa MakoloZimene Ndikuphunzira M’Baibulo
-
-
Uthenga Wopita kwa Makolo
Kodi mphatso yabwino kwambiri imene mungapatse ana anu ndi iti? Ana amafuna zinthu zambiri. Mwachitsanzo, iwo amafuna kuti muziwakonda, kuwauza zoyenera kuchita komanso kuwateteza. Komabe, mphatso yamtengo wapatali kwambiri imene mungapatse ana anuwo ndi kuwathandiza kuti am’dziwe Yehova ndi choonadi chopezeka m’Mawu ake, Baibulo. (Yohane 17:3) Zimenezi zingathandize anawo kuti azikonda Yehova ndi kum’tumikira ndi mtima wonse, kuyambira ali aang’ono.—Mateyu 21:16.
Makolo ambiri akuona kuti ana aang’ono amaphunzira mofulumira ngati akuwaphunzitsa pang’onopang’ono ndi kuwauza zinthu zina zoti azichita. Choncho ndife osangalala kutulutsa kabuku kano kakuti Zimene Ndikuphunzira M’Baibulo. Mutu uliwonse anaupanga m’njira yakuti ukhale wosavuta kuuphunzira. Kabuku kano talembera ana osapitirira zaka zitatu. Taikamo zithunzi ndi mawu ofotokozera zithunzizo komanso zoti ana azichita. Kabukuka si koti anawo aziseweretsa ayi, koma n’koti inuyo makolo muziwawerengera. Zimenezi zidzathandiza kuti muzikhala ndi nthawi yolankhulana ndi anawo.
Tikukhulupirira kuti kabukuka kakuthandizani kwambiri pamene mukuphunzitsa ana anu choonadi cha m’Baibulo ‘kuyambira ali akhanda.’—2 Timoteyo 3:14, 15.
Ndife abale anu,
Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova
-
-
Phunziro 1Zimene Ndikuphunzira M’Baibulo
-
-
Phunziro 1
Kodi ndani analenga dziko lapansili?
Kodi ndani analenga nyanja?
Kodi ndani analenga iweyo ndi ine?
Kodi ndani analenga gulugufe wa mapiko okongola chonchi?
Yehova Mulungu ndi amene analenga zinthu zonse.
ZOTI MUCHITE
Mwana wanuyo muwerengereni:
Muuzeni mwanayo kuti aloze:
Nyenyezi Mitambo Dzuwa
Boti Dziko Nyumba
Nyanja Gulugufe
Mufunseni mwana wanu kuti:
Kodi dzina la Mulungu ndani?
Kodi Yehova amakhala kuti?
Kodi Yehova analenga zinthu ziti?
-
-
Phunziro 2Zimene Ndikuphunzira M’Baibulo
-
-
Phunziro 2
Waziona nyama zimene zili pafupi ndi chingalawa cha Nowa?
Kodi ndi nyama ziti zimene zimalira kuti moo? Nanga ndi ziti zimene zimauwa?
Chingalawa cha Nowa chinapulumutsa nyama zonse, zazifupi ndi zazitali zomwe.
ZOTI MUCHITE
Mwana wanuyo muwerengereni:
Muuzeni mwanayo kuti aloze:
Chimbalangondo Galu Njovu
Kadyansonga Mkango Nyani
Nkhumba Nkhosa
Mbidzi Utawaleza
Muuzeni mwanayo kuti ayerekezere mmene nyama izi zimalirira:
Galu Mbuzi Tambala
Nkhumba Ng’ombe
-
-
Phunziro 3Zimene Ndikuphunzira M’Baibulo
-
-
Phunziro 3
Davide wamva zoti mnzake akudwala.
Choncho akunena kuti: “Ndadziwa chochita.
Ndimulembera kalata yomulimbikitsa, ndipo kenako ndikam’patsa.”
Uzisonyeza ena chifundo, ndipo nonse mudzakhala osangalala.
ZOTI MUCHITE
Mwana wanuyo muwerengereni:
Muuzeni mwanayo kuti aloze:
Nyumba Tebulo Davide
Dzuwa Mbalame Mtengo
Mufunseni mwana wanu kuti:
Kodi ukudziwa aliyense amene akudwala?
Kodi tingamuthandize bwanji kuti achire?
-
-
Phunziro 4Zimene Ndikuphunzira M’Baibulo
-
-
Phunziro 4
Tsiku lina kunja kunkagwa mvula.
Choncho Tomoko anadandaula kuti:
“Ndikulephera kutuluka.
N’chifukwa chiyani mvulayi sikusiya?”
Koma kenako,
mvula ija inasiya.
Ndipo dzuwa linawala.
Tomoko anasangalala kwambiri.
Ndiyeno anathamanga kupita panja ndipo anadabwa kwambiri ndi zimene anaona.
Tomoko ananena kuti, “Sindimadziwa kuti mvula yochokera kwa Mulungu, imakulitsa maluwa.”
ZOTI MUCHITE
Mwana wanuyo muwerengereni:
Muuzeni mwanayo kuti aloze:
Windo Mbalame Tomoko
Mtengo Maluwa
Pezani zinthu zobisika.
Kachilombo Ndege
Mufunseni mwana wanu kuti:
N’chifukwa chiyani Yehova analenga mvula?
-
-
Phunziro 5Zimene Ndikuphunzira M’Baibulo
-
-
Phunziro 5
Mnzako akakupatsa mphatso kapena kukuchitira zabwino umanyadira ndipo umasekerera.
Komabe nthawi zonse uzikumbukira kunena kuti “Zikomo.”
ZOTI MUCHITE
Mwana wanuyo muwerengereni:
Muuzeni mwanayo kuti aloze:
Mphatso Mnyamata
Chitseko Chakudya
Pezani zinthu zobisika.
Apozi Telefoni
Mufunseni mwana wanu kuti:
N’chifukwa chiyani ndi bwino kunena kuti “Zikomo”?
-
-
Phunziro 6Zimene Ndikuphunzira M’Baibulo
-
-
Phunziro 6
Tayang’ana zala zako za m’manjazo ndipo ugwedeze zala zako za kumiyendo.
Loza makutu ako, kenako uloze mphuno yako.
Tayang’ana miyendo yakoyo. Miyendo imeneyi ndi yomwe imakuthandiza kuti uzitha kuthamanga, kudumpha, kupanga masewera ozungulira ndi masewera ena osiyanasiyana.
Yang’ana pagalasi. Kodi ukuona chiyani?
Zonse zimene Yehova anapanga n’zabwino kwambiri.
ZOTI MUCHITE
Mwana wanuyo muwerengereni:
Muuzeni mwanayo kuti aloze:
Zala zake zam’manja Zala zake zakumiyendo Mphuno yake
Makutu ake Pakamwa pake
Pezani zinthu zobisika.
Nkhanu Mphaka
Mufunseni mwana wanu kuti:
Kodi ndani analenga iweyo ndi ine?
-