Zimene Achinyamata Amadzifunsa
Kodi Ndingatani Kuti Ndizisamala Ndalama?
“Nthawi zambiri ndimapezeka kuti ndikuganiza zogula chinthu chinachake chomwe sichofunikira ndiponso choti sindingachikwanitse kwenikweni, chifukwa choti achitsitsa mtengo basi.”—Anatero Anna,a wa ku Brazil.
“Nthawi zina anzanga amandipempha kuti tichite zinthu zinazake zofuna ndalama zambiri. Ndimafuna kukhala ndi anzangawo n’kumasangalala. Palibe amene amafuna kunena kuti, ‘Pepani, ndilibe ndalama zokwanira zochitira zimenezi.’”—Anatero Joan, wa ku Australia.
KODI mumaona ngati nthawi zonse simukhala ndi ndalama zokwanira? Mwina mumaganiza kuti, makolo anu akanakhala kuti amakupatsani ndalama zochulukirapo, mukanatha kugula zoseweretsa zimene mukuzifuna kwambiri zija. Kapena, mukanakhala kuti mumalandira malipiro ochulukirapo, mukanatha kugula nsapato zimene mukuona kuti mukuzifunikira kwambiri zija. Komabe, m’malo molimbana ndi kuganizira za ndalama zimene mulibe, bwanji osaphunzira kusamala ndalama zimene mumakhala nazo?
Ngati ndinu wachinyamata ndipo mukukhala ndi makolo anu, mukhoza kudikira mpaka mutachoka pakhomo pa makolo anu kuti muyambe kuphunzira kusamala ndalama. Koma kumeneko kungakhale ngati kudumpha m’ndege musanaphunzire kugwiritsa ntchito palachuti. N’zoona kuti munthu akhoza kutulukira momwe angagwiritsire ntchito palachutiyo ali m’malere atatsala pang’ono kugwera pansi. Koma kodi sizingakhale bwino kuphunzira kagwiritsiridwe ntchito kake musanadumphe m’ndegemo?
Mofanana ndi zimenezo, nthawi yabwino yophunzirira kusamala ndalama m’pamene musanayambe kukumana ndi mavuto a zachuma. Mfumu Solomo inalemba kuti “ndalama zitchinjiriza,” kapena kuti, zimateteza. (Mlaliki 7:12) Koma zingakutetezeni kokha ngati mwaphunzira kuzisamala. Kuchita zimenezo kungakuthandizeni kukhala odzidalira ndiponso kungachititse makolo anu kuyamba kukulemekezani kwambiri.
Phunzirani Kusamala Ndalama
Kodi munayamba mwafunsapo makolo anu kuti akuuzeni ndalama zimene zimafunika kuti asamale banja? Mwachitsanzo, kodi mukudziwa ndalama zimene amalipirira magetsi, nkhuni, makala, ndi madzi mwezi uliwonse? Nanga bwanji ndalama zimene amafunikira kulipirira thiransipoti, kugula chakudya, ndi kulipirira lendi? Mwina mungaganize kuti zinthu ngati zimenezo zingakhale zosasangalatsa kuzidziwa. Koma kumbukirani kuti inuyo mumagwiritsira nawo ntchito zinthu zimenezo. Komanso, mukadzachoka pakhomo pa makolo anu, mudzafunika kuyamba kulipira nokha zinthu zimenezo. Choncho zingakuthandizeni kudziwa kuti pamafunika ndalama zingati. Afunseni makolo anu ngati angakuonetseni mabilu ena a zinthu zimenezi, ndipo mvetserani mwatcheru pamene akukufotokozerani momwe amachitira bajeti ya zinthu zimenezi.
Mwambi wina wa m’Baibulo umati: ‘Wanzeru amamva, nawonjezera kuphunzira; ndipo wozindikira ndi amene amafikira kuuphungu.’ (Miyambo 1:5) Anna, amene tinamutchula koyambirira uja, anati, “Bambo anga anandiphunzitsa momwe ndingachitire bajeti ndipo anandionetsa momwe kuchita zinthu mwadongosolo kulili kofunika posamalira ndalama za banja.” Panthawi yomweyomweyo, mayi ake a Anna anam’phunzitsa zinthu zina zothandiza. Anna anati: “Anandiphunzitsa phindu loyerekezera mitengo ya zinthu ndisanagule.” Iye anawonjezera kuti, “Mayi anga ankatha kuchita zinthu zambiri ndi ndalama zochepa.” Kodi Anna wapindula bwanji? Iye anati: “Tsopano ndimatha kusamala bwinobwino ndalama zanga. Ndimagula zinthu mosamala, choncho ndili ndi ufulu ndiponso mtendere wa mumtima umene umabwera chifukwa chopewa ngongole zosafunikira.”
Zindikirani Kuti Kusamala Ndalama N’kovuta
N’zoona kuti n’zosavuta kungolankhula za kusamala ndalama, koma kuchitadi zimenezo n’kovuta, makamaka ngati mukukhala pakhomo pa makolo anu ndipo amakupatsani ndalama nthawi zina kapena ngati muli pantchito. Chifukwa chiyani? Chifukwa choti mosakayikira makolo anu ndi amene amalipirira zinthu zambiri panyumbapo. Choncho ndalama zanu zambiri zingakhale zoti muzigwiritsa ntchito iliyonse yomwe mukufuna. Ndipotu, kugula zinthu kumasangalatsa. Paresh, mnyamata wa ku India anavomereza kuti: “Kugula zinthu n’kophweka kwambiri kwa ine, ndipo kumandisangalatsa.” Sarah, wa ku Australia, amaonanso choncho. Iye anati: “Kugula zinthu kumandisangalatsa kwabasi.”
Komanso, anzanu angakukakamizeni kuti muwononge ndalama zochuluka kuposa zimene muyenera kuwononga. Ellena, wa zaka 21 anati: “Anzanga ayamba kuona kuti njira yabwino kwambiri yosangalalira ndiyo kugula zinthu. Ndikapitira nawo limodzi kwinakwake, pamakhala ngati pali lamulo loti tiyenera kuwononga ndalama ngati tikufuna kuti tisangalale.”
N’chinthu chachibadwa kuti muzifuna kuchita zinthu zofanana ndi anzanu. Koma dzifunseni kuti, ‘Kodi ndikuwononga ndalama ndi anzanga chifukwa choti ndingakwanitse kuchita zimenezi, kapena ndikuona kuti ndikuyenera kuchita zimenezi?’ Anthu ambiri amawononga ndalama pofuna kuti anzawo aziwapatsa ulemu. Kuchita zimenezi kungakubweretsereni mavuto aakulu azachuma, makamaka ngati muli ndi khadi la ngongole. Mlangizi wina wa zachuma dzina lake Suze Orman anachenjeza kuti: “Ngati mukuona kuti mumafuna kugometsa anthu ndi zimene muli nazo m’malo mwa khalidwe lanu, ndiye kuti sizingakuvuteni kugwiritsa ntchito molakwika khadi la ngongole.”
M’malo momaliza ndalama zimene mukuloledwa pa khadi lanu la ngongole kapena kumaliza malipiro anu onse apamwezi tsiku limodzi lokha lomwe mwapita kokasangalala, bwanji osayesera zimene amachita Ellena? Iye anati: “Ndikapita kwinakwake ndi anzanga, ndimakonzekeratu ndipo ndimadziwiratu kuchuluka kwa ndalama zimene ndikufuna kuwononga. Malipiro anga apamwezi amapita mwachindunji ku banki ndipo ndimakatenga ndalama zokhazo zomwe ndikufuna kugwiritsa ntchito tsiku limenelo. Ndimaonanso kuti n’chinthu chanzeru kupita kogula zinthu ndi anzanga amene amasamala ndalama ndi amene angandilimbikitse kuyamba ndayendayenda kaye n’kuyerekezera mitengo ya zinthu m’malo mongogula zinthu msangamsanga.”—Miyambo 13:20.
Phunziranipo Kanthu Makolo Anu Akakuyankhani Kuti Ayi
Ngakhale ngati makolo anu sakupatsani ndalama ndiponso simuli pantchito, mukhozabe kuphunzira maphunziro ofunika okhudza ndalama mukukhalabe pakhomo pa makolo anu. Mwachitsanzo, mukawapempha makolo anu ndalama, kapena mukawapempha kuti akugulireni chinthu chinachake, mwina anganene kuti ayi. Chifukwa chiyani? Chifukwa chimodzi chingakhale choti zimene mukufunazo sangazikwanitse chifukwa zikhoza kusokoneza bajeti ya banja lanu. Pokukanirani zimene mwapemphazo, ngakhale ngati angafune kukupatsani, makolo anu akukupatsani chitsanzo chabwino cha kudziletsa. Ndipo kudziletsa n’kofunika kwambiri kuti muthe kusamala ndalama.
Tiyerekezere kuti makolo anu angakwanitse kukupatsani zimene mukufunazo. Ngakhale ndi choncho, akhozabe kunena kuti ayi. Mwina mukhoza kuganiza kuti akungouma mtima basi. Koma ganizirani izi: n’kutheka kuti akufuna kukuphunzitsani phunziro lofunika loti chimwemwe chanu sichidalira pa kupeza chilichonse chomwe mukufuna. Pa nkhani imeneyi, Baibulo limati: “Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu.”—Mlaliki 5:10.
Timaona kuti mawu amenewo ndi oonadi tikaona zomwe zimachitikira achinyamata ambiri amene makolo awo amawagulira chilichonse chomwe akufuna. Pakapita nthawi achinyamatawa amazindikira kuti sali osangalala kwenikweni. Kaya akhale ndi zinthu zochuluka bwanji, amafunabe kugula chinthu china chimodzi chokha choti awonjezere pa mulu wa zinthu zomwe ali nazo kale zija. M’kupita kwa nthawi, achinyamata amene amayembekezera kupatsidwa chilichonse chomwe apempha amadzakhala achikulire osayamika. Solomo anachenjeza kuti: “Ngati munthu akusasatitsa wantchito [kapena mwana] wake kuyambira ali wamng’ono, akadzakula adzakhala wosayamika.”—Miyambo 29:21, NW.
Ndalama Ndi Nthawi
Anthu ena pa chikhalidwe chawo ali ndi mawu akuti, Nthawi ndi ndalama. Mawu amenewa amagogomezera mfundo yakuti anthu amafunika kuwononga nthawi kuti apeze ndalama choncho kuwononga nthawi n’kuwononga ndalama. Mawu ofanana ndi amenewa ndi oonanso, oti ndalama ndi nthawi. Ngati mukuwononga ndalama, ndiye kuti mukuwononga nthawi imene munataya kuti mupeze ndalama zimenezo. Mukaphunzira kusunga ndalama ndiye kuti mwaphunzira kusunga nthawi. Mwa njira yotani?
Taganizirani zimene ananena Ellena. Iye anati: “Ndikamasamala mmene ndimawonongera ndalama, ndimakhala ndi kuchepetsa ndalama zimene ndimafunikira kupeza. Mwa kupanga bajeti yothandiza n’kuimamatira, sindifunikira kugwira ntchito nthawi yaitali kuti ndipeze ndalama zobwezera ngongole zikuluzikulu. Ndimatha kuyendetsa bwino nthawi yanga ndi moyo wanga.” Kodi nanunso simungafune kuti moyo wanu uziyenda bwino choncho?
[Mawu a M’munsi]
a Tasintha mayina.
ZOTI MUGANIZIRE
◼ Kodi zimakuvutani kusamala ndalama? Chifukwa chiyani?
◼ N’chifukwa chiyani muyenera kupewa mtima wokonda ndalama?—1 Timoteo 6:9, 10.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 12]
KODI KUKHALA NDI NDALAMA ZOCHULUKIRAPO KUNGATHANDIZE?
Kodi kungokhala ndi ndalama zochulukirapo kungakhale njira yothetsera vuto lanu lowononga ndalama? Mlangizi wa zachuma Suze Orman anati: “Tonsefe timaganiza kuti kulandira ndalama zochulukirapo ndiye kungakhale yankho la mavuto athu a zachuma, koma nthawi zambiri sizikhala choncho.”
Mwachitsanzo: Ngati mukuyendetsa galimoto ndiye simukutha kuiwongolera bwino kapena muli ndi chizolowezi choyendetsa mutatsinzina, kodi kuthira mafuta ena m’galimotoyo kungakuchititseni kumva bwinoko? Kodi kungakuchititseni kukafika bwino kumene mukupitako? Mofanana ndi zimenezi, ngati simuphunzira kusamala ndalama, kukhala ndi ndalama zochulukirapo sikungakuthandizeni.
[Bokosi/Tchati patsamba 13]
SAMALANI NDALAMA
Kodi mwezi wathawu mwawononga ndalama zingati? Kodi munagulira chiyani? Simukudziwa? M’munsimu muli mfundo zokuthandizani kusamala ndalama kuti kuwononga ndalama kusafike powononga moyo wanu.
◼ Muzilemba. Kwa mwezi umodzi kapena miyezi ingapo, muzilemba ndalama zimene mwalandira ndi deti limene mwazilandira. Lembani chinthu chilichonse chomwe mwagula kapena kulipirira ndiponso mtengo wake. Pamapeto pa mwezi, wonkhetsani ndalama zimene munalandira ndi ndalama zimene mwawononga.
◼ Pangani bajeti. Pa tsamba lopanda kanthu, lembanipo mizere kuti mukhale ndi madanga atatu. M’danga loyamba, lembani ndalama zonse zimene mukuyembekezera kulandira pa mwezi umodzi. M’danga lachiwiri, lembani zinthu zimene mukufuna kugula kapena kulipirira ndi ndalama zimenezo. Gwiritsani ntchito zinthu zimene munalemba zija kuti zikuthandizeni. Mwezi ukamadutsa, lembani m’danga lachitatu ndalama zimene mwawonongadi pa chinthu chilichonse chomwe munalemba kuti mudzagula kapena kulipirira. Lembaninso zinthu zonse zomwe mwagula popanda kukonzekera.
◼ Sinthani mapulani. Ngati mukuwononga ndalama zoposa zomwe munali kuyembekezera pa zinthu zina ndipo mwayamba kugwa m’ngongole, sinthani mapulani anu. Bwezani ngongolezo. Pitirizanibe kusamala ndalama.
[Tchati]
Dulani izi n’kuzigwiritsa ntchito!
Bajeti Yanga Yapamwezi
Ndalama zimene ndimapeza Bajeti ya zinthu zimene ndigule kapena kulipirira Ndalama zimene ndawonongadi
ndalama zimene makolo amandipatsa chakudya
ntchito yaganyu zovala
zinthu zina foni
zosangalatsa
zopereka
zosunga
zinthu zina
Zonse pamodzi Zonse pamodzi Zonse pamodzi
$ $ $
[Chithunzi]
Kumbukirani kuti, ngati mukuwononga ndalama, ndiye kuti mukuwononganso nthawi imene munataya kuti mupeze ndalamazo
[Chithunzi patsamba 11]
Bwanji osafunsa makolo anu kuti akuonetseni mmene amapangira bajeti?