Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • fy mutu 8 tsamba 90-102
  • Tetezerani Banja Lanu ku Zisonkhezero Zowononga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tetezerani Banja Lanu ku Zisonkhezero Zowononga
  • Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KODI NDANI ADZAPHUNZITSA ANA ANU?
  • LINGALIRO LA MULUNGU PA ZAKUGONANA
  • NTCHITO IMENE MAKOLO ALI NAYO
  • MABWENZI A ANA ANU
  • KODI NDI ZOSANGULUTSA ZA MTUNDU WOTANI?
  • BANJA LANU LINGALAKE DZIKO
  • Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Kuphunzitsa ana anu?
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Mungatani Kuti Aliyense Azisangalala M’banja Lanu?​—Mbali Yachiwiri
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Makolo, Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikonda Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Makolo Khalani Chitsanzo Chabwino kwa Ana Anu
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
fy mutu 8 tsamba 90-102

Mutu 8

Tetezerani Banja Lanu ku Zisonkhezero Zowononga

Chithunzi patsamba 91

1-3. (a) Kodi zisonkhezero zoipa zimene zingawononge banja zimachokera kuti? (b) Kodi ndi njira yachikatikati yotani imene makolo afunikira kuitsatira potetezera ana awo?

TINENE kuti mukufuna kutumiza mnyamata wanu wamng’ono kusukulu, ndipo mvula ilikugwa. Kodi mungachite motani? Kodi mudzamlola kutuluka ndi kuthamanga popanda khoti lamvula? Kapena kodi mudzammveka makhoti ochuluka kwakuti alephera ndi kuyenda? Ndithudi, simudzachita chilichonse cha zimenezo. Mudzampatsa choyenera kuti asavumbwe.

2 Mofananamo, makolo ayenera kupeza njira yoyenera yotetezerera banja lawo ku zisonkhezero zowononga zimene zikuvumba pa iwo kuchokera ku mbali zosiyanasiyana—zosangulutsa, zoulutsidwa, mabwenzi, ndipo nthaŵi zina ngakhale masukulu. Makolo ena amachita zochepa kapena samachita kalikonse kuti atetezere banja lawo. Ena, amene amaona zisonkhezero zonse zakunja kukhala zovulaza, ali oletsa kwambiri kwakuti ana awo amamva kukhala opanikizika. Kodi nkotheka kukhala achikatikati?

3 Inde, nkotheka. Kukhala wopambanitsa sikuthandiza ndipo kungadzetse tsoka. (Mlaliki 7:16, 17) Koma kodi ndi motani mmene makolo achikristu amapezera njira yachikatikati yotetezerera banja lawo? Talingalirani mbali zitatu izi: maphunziro, mayanjano, ndi zosangulutsa.

KODI NDANI ADZAPHUNZITSA ANA ANU?

4. Kodi makolo achikristu ayenera kuwaona motani maphunziro?

4 Makolo achikristu amaona maphunziro kukhala ofunika kwambiri. Amadziŵa kuti sukulu imathandiza ana kudziwa kuŵerenga, kulemba, ndi kulankhulana, limodzinso ndi kuthetsa mavuto. Iyeneranso kuwaphunzitsa kaphunziridwe. Maluso amene ana amapeza kusukulu angawathandize kukhala achipambano mosasamala kanthu za mavuto a dziko lalero. Ndiponso, maphunziro abwino angawathandize kuchita ntchito zapamwamba.—Miyambo 22:29.

5, 6. Kodi ndi motani mmene ana kusukulu angakhalire pangozi ya kuphunzitsidwa zosayenera pankhani zakugonana?

5 Komanso, sukulu imabweretsa pamodzi ana osiyanasiyana—ambiri okhala ndi malingaliro osokoneza. Mwachitsanzo, talingalirani za maganizo awo pa zakugonana ndi makhalidwe. Pasukulu ina yasekondale ku Nigeria, mtsikana wina wachiwerewere anali kumalangiza ana asukulu anzake zakugonana. Iwo anamvetsera kwa iye mwachidwi, ngakhale kuti maganizo akewo anali odzala ndi zopusa zokhazokha zimene anaona m’mabuku a zamaliseche. Atsikana ena anatsatira uphungu wake ndi kuchita zimenezo. Chotulukapo, mtsikana wina anatenga mimba yapathengo ndipo anamwalira poyesa kuichotsa yekha.

6 Nzachisoni kuti malingaliro olakwa ena a zakugonana ochokera kusukulu, amaphunzitsidwa ndi aphunzitsi osati ana asukulu. Makolo ambiri akwiya pamene sukulu zaphunzitsa ana awo zakugonana popanda kuwaphunzitsanso za makhalidwe abwino ndi zakukhala ndi thayo. Mayi wina wa mtsikana wazaka 12 anati: “Tikukhala m’dera lachipembedzo ndi losunga mwambo kwambiri, komabe pasukulu yathu yasekondale penipenipo, amagaŵira makondomu kwa achichepere!” Iye ndi mwamuna wake anada nkhaŵa kwambiri pamene anamva kuti anyamata a msinkhu wa mwana wawo wamkazi anali kumpempha kugona naye. Kodi makolo angatetezere motani banja lawo ku zisonkhezero zowononga?

7. Kodi tingachite motani kuti ana asaphunzitsidwe zolakwa ponena zakugonana?

7 Kodi nkwabwino kusatchulira ana kalikonse ponena za nkhani zakugonana? Ayi. Ndi bwino kuphunzitsa ana anu zakugonana inu mwini. (Miyambo 5:1) Nzoona, m’mbali zina za Ulaya ndi North America, makolo ambiri amachita manyazi kutchula za nkhaniyi. Mofananamo, m’maiko ena a mu Afirika, nkwakamodzikamodzi kwa makolo kukambitsirana ndi ana awo nkhani zakugonana. “Si mwambo wachiafirika kuchita zimenezo,” akutero tate wina ku Sierra Leone. Makolo ena amaganiza kuti kuphunzitsa ana zakugonana ndiko kuwapatsa malingaliro amene adzawasonkhezera kuchita chisembwere! Koma kodi lingaliro la Mulungu nlotani?

LINGALIRO LA MULUNGU PA ZAKUGONANA

8, 9. Kodi Baibulo limaphunzitsa zabwino zotani ponena za nkhani zakugonana?

8 Baibulo limasonyeza bwino lomwe kuti kukambitsirana zakugonana m’nkhani yoyenera sikuyenera kuchititsa manyazi. Mu Israyeli, anthu a Mulungu anauzidwa kusonkhana pamodzi, kuphatikizapo “ana aang’ono,” kuti amvetsere kuŵerenga mofuula kwa Chilamulo cha Mose. (Deuteronomo 31:10-12; Yoswa 8:35) Chilamulocho chinatchula mosabisa nkhani zingapo zakugonana, kuphatikizapo kupita kumwezi, kutulutsa ubwamuna, dama, chigololo, mathanyula, kugona ndi wachibale, ndi kugona ndi nyama. (Levitiko 15:16, 19; 18:6, 22, 23; Deuteronomo 22:22) Pambuyo pa kuŵerenga kotero, mosakayikira konse makolo anali ndi zochuluka zofotokozera ana awo olakalaka kudziŵawo.

9 Pali mavesi ena m’machaputala 5, 6, ndi 7 a Miyambo amene amapereka uphungu wachikondi wa makolo pa ngozi za kuchita chisembwere. Mavesi ameneŵa amasonyeza kuti chisembwere nthaŵi zina chingakhale chokopa mtima. (Miyambo 5:3; 6:24, 25; 7:14-21) Koma amaphunzitsa kuti ncholakwa ndipo chili ndi zotulukapo zatsoka, ndipo amapereka chitsogozo chothandizira achichepere kupeŵa njira zoipa. (Miyambo 5:1-14, 21-23; 6:27-35; 7:22-27) Ndiponso, chisembwere chimasiyanitsidwa ndi ukoma wokhutiritsa wa kugonana kwa m’malo ake oyenera, muukwati. (Miyambo 5:15-20) Ndi chitsanzo chabwino chotani nanga cha kuphunzitsa chimene makolo ayenera kutsatira!

10. Kodi nchifukwa ninji kupatsa ana chidziŵitso chaumulungu chonena za kugonana sikungawasonkhezere kuchita chisembwere?

10 Kodi kaphunzitsidwe koteroko kamasonkhezera ana kuchita chisembwere? Ayi. M’malo mwake, Baibulo limaphunzitsa kuti: “Olungama adzapulumuka pakudziŵa.” (Miyambo 11:9) Kodi simufuna kupulumutsa ana anu ku zisonkhezero za dzikoli? Tate wina anati: “Kuyambira pamene anawo anali aang’ono kwambiri, tayesa kukhala omasuka kwa iwo ponena za kugonana. Mwa njira imeneyo, pamene amva ana ena akulankhula zakugonana, samakhala olakalaka kudziŵa. Sichimakhala chinsinsi chachikulu.”

11. Kodi ana angaphunzitsidwe motani pang’onopang’ono nkhani zakugonana?

11 Monga momwe tinaonera m’mitu yapitayo, maphunziro a zakugonana ayenera kuyamba mofulumira. Pophunzitsa ana aang’ono kutchula maina a ziŵalo za thupi, musalumphe mpheto zawo monga kuti zinali zochititsa manyazi. Aphunzitseni maina ake oyenera. M’kupita kwa nthaŵi, kuwaphunzitsa zinthu zamseri ndi zosayenera kuchita kumakhala kofunikira. Ndi bwino kuti makolo onse aŵiri aphunzitse ana awo kuti mbali zimenezi za thupi lawo zili zapadera, ndipo aliyense sayenera kuzigwira kapena kuziona, ndipo siziyenera kukambidwa mwanjira yoipa. Pamene ana akula, ayenera kuuzidwa mmene mwamuna ndi mkazi amakhalira pamodzi kuti akhale ndi mimba ya mwana. Pofika panthaŵi imene matupi awo ayamba kuloŵa m’nyengo yachinamwali, ayenera kukhala atadziŵa kale masinthidwe amene akuwayembekezera. Malinga ndi kufotokoza kwa m’Mutu 5, maphunziro otero amathandizanso kutetezera ana kwa ogona ana.—Miyambo 2:10-14.

NTCHITO IMENE MAKOLO ALI NAYO

12. Kodi ndi malingaliro osokoneza otani amene amaphunzitsidwa kaŵirikaŵiri kusukulu?

12 Makolo amafunikira kukhala okonzeka kulimbana ndi malingaliro ena onama amene angaphunzitsidwe kusukulu—ziphunzitso zadziko zonga chisinthiko, utundu, kapena lingaliro lakuti palibe choonadi chimene chili chenicheni chonse. (1 Akorinto 3:19; yerekezerani ndi Genesis 1:27; Levitiko 26:1; Yohane 4:24; 17:17.) Akuluakulu a sukulu ambiri ofuna kuthandiza amagogomezera mopambanitsa kufunika kwa maphunziro apamwamba. Pamene kuli kwakuti nkhani ya maphunziro owonjezera ili chosankha cha munthu mwini, aphunzitsi ena amanena kuti ndiyo njira yokha yopezera chipambano chaumwini.a—Salmo 146:3-6.

13. Kodi ana opita kusukulu angatetezeredwe motani ku malingaliro olakwa?

13 Kuti makolo alimbane ndi ziphunzitso zosokoneza kapena zolakwa, ayenera kudziŵa zimene ana awo amaphunzitsidwa. Chotero makolo, kumbukirani kuti inunso muli ndi ntchito yanu! Sonyezani chidwi chenicheni m’maphunziro a ana anu. Lankhulani nawo atabwerako kusukulu. Funsani zimene amaphunzira, zimene amakonda kwambiri, ndi zimene zimawavuta kwambiri. Onani homuweki yawo, manotsi awo, ndi zimene amakhoza pamayeso. Yesani kudziŵa aphunzitsi awo. Sonyezani aphunzitsi kuti mumayamikira ntchito yawo ndi kuti mumafuna kuwathandiza m’njira iliyonse imene mungakhoze.

MABWENZI A ANA ANU

14. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuti ana aumulungu asankhe mabwenzi abwino?

14 “Anakuphunzitsa zimenezo ndani iwe?” Kodi ndi makolo angati amene afunsa funso limeneli, pochita mantha ndi chinthu china chimene mwana wawo wanena kapena kuchita chimene chikuoneka kukhala chachilendo kwambiri? Ndipo ndi kangati pamene yankho limatchula bwenzi latsopano kusukulu kapena wachinansi? Inde, mabwenzi amatiyambukira kwambiri, kaya ndife achichepere kapena achikulire. Mtumwi Paulo anachenjeza kuti: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33; Miyambo 13:20) Achichepere makamaka ali pangozi ya kusonkhezeredwa ndi mabwenzi. Iwo amakhala osatsimikiza ponena za iwo eni ndipo nthaŵi zina angatengeke ndi kufuna kukondweretsa mabwenzi awo. Pamenepo, nkofunika chotani nanga kuti asankhe mabwenzi abwino!

15. Kodi makolo angathandize motani ana awo kusankha mabwenzi?

15 Monga momwe kholo lililonse likudziŵira, si nthaŵi zonse pamene ana amasankha bwino; amafunikira chitsogozo. Si nkhani ya kungowasankhira mabwenzi. M’malo mwake, pamene akukula, aphunzitseni luntha ndi kuwathandiza kuona mikhalidwe imene ayenera kufuna mwa mabwenzi. Mkhalidwe wofunika kwambiri ndiwo kukonda Yehova ndi kuchita choyenera pamaso pake. (Marko 12:28-30) Aphunzitseni kukonda ndi kulemekeza awo amene ali ndi kuona mtima, chifundo, kukoma mtima, khama. Paphunziro labanja, thandizani ana kuzindikira mikhalidwe imeneyo mwa anthu a m’Baibulo ndi kuyesa kupeza mikhalidwe imodzimodzi mwa ena mumpingo. Perekani chitsanzo mwa kugwiritsira ntchito njira imodzimodzi posankha mabwenzi anu.

16. Kodi makolo angayang’anire motani ana awo pa mabwenzi omwe asankha?

16 Kodi mumawadziŵa mabwenzi a ana anu? Bwanji osauza ana anu kuti abwere nawo kunyumba kuti muwadziŵe? Mungapemphenso ana anu kukuuzani zimene ana ena amaganiza ponena za mabwenzi ameneŵo. Kodi amadziŵika kukhala odzisunga kapena ali ndi moyo wapaŵiri? Ngati ali amoyo wapaŵiri, thandizani ana anu kulingalirapo ndi kuona kuti mayanjano oterowo angawawononge. (Salmo 26:4, 5, 9-12) Ngati muona masinthidwe osayenera m’khalidwe, mavalidwe, maganizo, kapena malankhulidwe a mwana wanu, mungafunikire kukambitsirana naye ponena za mabwenzi ake. Mwana wanu angakhale akuyanjana ndi bwenzi limene likupereka chisonkhezero choipa.—Yerekezerani ndi Genesis 34:1, 2.

17, 18. Kuwonjezera pa kuchenjeza za mabwenzi oipa, kodi ndi chithandizo chotani chimene makolo angapereke?

17 Komabe, sikokwanira kungophunzitsa ana anu kupeŵa mabwenzi oipa. Athandizeni kupeza abwino. Tate wina akuti: “Nthaŵi zonse tinali kuyesa kupeza choloŵa m’malo. Chotero pamene sukulu inafuna mwana wathu pa timu ya mpira wachitanyu, ine ndi mkazi wanga tinali kukhala naye pansi ndi kukambitsirana chifukwa chake zimenezo sizinali zabwino—kuopera mabwenzi atsopano amene adzakhalako. Komano tinalinganiza kutenga ana ena mumpingo ndi kupita nawo onse ku paki kukaseŵera mpira. Ndipo zimenezo zinathandiza kwambiri.”

18 Makolo anzeru amathandiza ana awo kupeza mabwenzi abwino ndipo amakhala nawo pazosangulutsa zabwino. Komabe, kwa makolo ambiri, nkhani ya zosangulutsa imeneyi imabweretsanso mavuto ake.

KODI NDI ZOSANGULUTSA ZA MTUNDU WOTANI?

19. Kodi ndi zitsanzo za m’Baibulo zotani zimene zimasonyeza kuti kuseŵera m’mabanja sikuchimwa?

19 Kodi Baibulo limaletsa kuseŵera? Kutalitali! Baibulo limanena kuti pali “mphindi yakuseka . . . ndi mphindi yakuvina.”b (Mlaliki 3:4) Anthu a Mulungu mu Israyeli wakale anasangalala ndi nyimbo ndi kuvina, maseŵero, ndi miyambi. Yesu Kristu anapita ku phwando laukwati lalikulu ndi ku “phwando lalikulu” limene Mateyu Levi anamkonzera. (Luka 5:29; Yohane 2:1, 2) Mwachionekere, Yesu sanali woletsa kusangalala. Kuseka ndi kuseŵera zisaonedwe konse kukhala machimo m’nyumba mwanu!

Chithunzi patsamba 99

Zosangulutsa zosankhidwa bwino, monga pikiniki iyi ya banja yokagonera kumsasa, zingathandize ana kuphunzira ndi kukula mwauzimu

20. Kodi makolo ayenera kukumbukiranji pofunira banja zosangulutsa?

20 Yehova ali “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteo 1:11, NW) Chotero kulambira Yehova kuyenera kupereka chikondwerero, osati kukhala kosoŵetsa chisangalalo m’moyo. (Yerekezerani ndi Deuteronomo 16:15.) Ana mwachibadwa ali ansangala ndi anyonga kwambiri imene imawachititsa kuseŵera ndi kusanguluka kwambiri. Zosangulutsa zosankhidwa bwino sizimakhala ndi kuseŵera kokha. Ndiyo njira imene mwana amaphunzirira zinthu ndi kukula. Mutu wa banja ali ndi thayo la kufunira banja lake zosoŵa m’chilichonse, kuphatikizapo zosangulutsa. Komabe, kukhala wachikatikati nkofunika.

21. Kodi ndi mbuna zotani zimene zili m’zosangulutsa za lerolino?

21 ‘M’masiku otsiriza’ ano odzala ndi mavuto, dziko ladzala ndi anthu “okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu,” ndendende ndi mmene kunaloseredwa m’Baibulo. (2 Timoteo 3:1-5) Kwa ambiri, kusanguluka ndiko chinthu chachikulu m’moyo. Pali zosangulutsa zochuluka kwambiri moti zikhoza kuphimba mosavuta zinthu zofunika kwambiri. Ndiponso, zosangulutsa zamakono zambiri zimasonyeza chisembwere, chiwawa, kugwiritsira ntchito anamgoneka, ndi machitachita ena ovulaza kwambiri. (Miyambo 3:31) Kodi tingachitenji kuti titetezere achichepere ku zosangulutsa zovulaza?

22. Kodi makolo angaphunzitse motani ana awo kupanga zosankha zanzeru pazosangulutsa?

22 Makolo afunikira kuika malire ndi ziletso. Koma koposa zimenezo, afunikira kuphunzitsa ana awo kuzindikira chimene chili chosangulutsa chovulaza ndi kudziŵa umene uli mlingo wopambanitsa. Kuphunzitsa koteroko kumafuna nthaŵi ndi khama. Talingalirani chitsanzo. Tate wa ana amuna aŵiri anaona kuti mwana wake wamkulu anali kumvetsera kaŵirikaŵiri ku siteshoni yatsopano ya wailesi. Motero, tsiku lina pamene anali kuyendetsa lole popita kuntchito, tateyo anatsegula siteshoni imodzimodziyo. Amati akayenda, nkuimirira ndi kulemba mawu a nyimbo zina. Tsiku lina anakhala pansi ndi ana akewo ndi kukambitsirana zimene anamva. Anawafunsa mafunso opempha lingaliro, akumayamba ndi lakuti “Kodi mulingalira bwanji?” ndipo anamvetsera moleza mtima mayankho awo. Pambuyo pokambitsirana nkhaniyo mwa kugwiritsira ntchito Baibulo, anyamatawo anavomereza kuti sadzamvetseranso ku siteshoni imeneyo.

23. Kodi makolo angatetezere motani ana awo ku zosangulutsa zosayenera?

23 Makolo achikristu anzeru amafufuza nyimbo, maprogramu a pa TV, mavidiyotepu, mabuku a nkhani zoseketsa, maseŵero apavidiyo, ndi mafilimu amene ana awo amakonda. Amaona pa zithunzi zapachikuto, mawu ake, ndi zoikamo matepu, ndipo amaŵerenga programu ya m’nyuzipepala ndi kuona zithunzi zolengeza filimu. Ambiri amadabwa poona “zosangulutsa” zina zoonetsedwa kwa ana lerolino. Awo amene akufuna kutetezera ana awo ku zisonkhezero zoipa amakhala pansi ndi banja ndi kukambitsirana ngozi zake, akumagwiritsira ntchito Baibulo ndi zofalitsa zozikidwa pa Baibulo, monga buku lakuti Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza ndi nkhani za m’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!c Pamene makolo aika malire okhwima bwino, osasinthasintha ndi oyenerera, kaŵirikaŵiri pamakhala zotulukapo zabwino.—Mateyu 5:37; Afilipi 4:5.

24, 25. Kodi pali mitundu yoyenera yotani ya zosangulutsa imene mabanja angasangalale nayo pamodzi?

24 Ndithudi, kuletsa zosangulutsa za mitundu yovulaza kwangokhala mbali imodzi ya nkhondoyo. Tiyenera kugwiritsira ntchito zabwino kulimbana ndi zoipa, apo phuluzi ana adzaloŵerera m’njira yoipa. Mabanja achikristu ochuluka ali ndi zokumbukira zambiri za nthaŵi zabwino zakusangalala pamodzi—kupita ku pikiniki, kuyenda maulendo, kupita ku pikiniki yokagonera kumsasa, kuchita maseŵero, kuyenda maulendo okachezera achibale kapena mabwenzi. Ena apeza kuti kungoŵerenga mofuula chapamodzi kuti apeze mpumulo kumapatsa chisangalalo chachikulu ndi chitonthozo. Ena amakonda kusimba nthano zoseketsa ndi zokondweretsa. Komabe ena amachita zinthu zapamtima chapamodzi, mwachitsanzo, kupala matabwa ndi ntchito zina za luso la manja, limodzi ndi kuliza ziŵiya zoimbira, kulemba zithunzithunzi, kapena kuphunzira za chilengedwe cha Mulungu. Ana amene amaphunzira kusangalala ndi zinthu zotero amatetezereka ku zosangulutsa zambiri zosayenera, ndipo amaphunzira kuti zosangulutsa zimaloŵetsamo zambiri osati kungokhala pansi ndi kusangalatsidwa. Kaŵirikaŵiri kutengamo mbali kumakhala kokondweretsa kuposa kungopenyerera.

25 Macheza angakhalenso mtundu wopindulitsa wa zosangulutsa. Pamene ayang’aniridwa bwino ndipo osati aakulu kwadzaoneni kapena otenga nthaŵi yaitali, angapatse anawo zochuluka kuposa kuseŵera chabe. Angawathandize kuzamitsa maunansi awo achikondi mumpingo.—Yerekezerani ndi Luka 14:13, 14; Yuda 12.

BANJA LANU LINGALAKE DZIKO

26. Ponena za kutetezera banja ku zisonkhezero zoipa, kodi ndi uti umene uli mkhalidwe wofunika koposa?

26 Mosakayikira, kutetezera banja lanu ku zisonkhezero zowononga za dziko ndiko ntchito yolimba. Koma pali chinthu chimodzi choposa zonse chimene chidzakuthandizani kupambana. Ndicho chikondi! Maunansi olimba achikondi m’banja adzachititsa nyumba yanu kukhala malo achisungiko ndipo adzapititsa patsogolo kulankhulana, kumene kuli chitetezo chachikulu pa zisonkhezero zoipa. Ndiponso, pali kukulitsa mtundu wina wa chikondi kumene kuli kofunika koposa—kukonda Yehova. Pamene chikondi chotero chifunga m’banja, nkothekera kwambiri kuti ana adzaphunzira kunyansidwa ndi lingaliro la kukwiyitsa Mulungu ndi la kugonjera ku zisonkhezero za dziko. Ndipo makolo amene amakonda Yehova ndi mtima wonse adzayesayesa kutsanzira umunthu wake wachikondi, wololera, ndi wachikatikati. (Aefeso 5:1; Yakobo 3:17) Ngati makolo achita zimenezo, ana awo sadzaona kulambira Yehova kukhala chinthu cholanda ufulu kapena monga njira ya moyo wopanda kuseŵera kapena kuseka, imene amafuna kuthaŵamo mofulumira. M’malo mwake, adzaona kuti kulambira Mulungu ndiko njira ya moyo yachimwemwe koposa, ndi yokhutiritsa.

27. Kodi banja lingalake motani dziko?

27 Mabanja amene amakhala ogwirizana muutumiki wachimwemwe ndi wachikatikati kwa Mulungu, akumayesa ndi mtima wonse kukhala “opanda banga ndi opanda chilema” cha zisonkhezero za dzikoli, amakondweretsa Yehova. (2 Petro 3:14; Miyambo 27:11) Mabanja oterowo amalondola mapazi a Yesu Kristu, amene anakaniza zoyesayesa za dziko la Satana za kumuipitsa. Chakumapeto kwa moyo wake monga munthu, Yesu anakhoza kunena kuti: “Ndalilaka dziko lapansi ine.” (Yohane 16:33) Lolani kuti banja lanu lilake dziko ndi kusangalala ndi moyo wosatha!

a Ponena za nkhani ya maphunziro owonjezera, onani brosha lakuti Mboni za Yehova ndi Maphunziro, lofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, masamba 4-7.

b Liwu lachihebri pano lotembenuzidwa “kuseka” m’mitundu ina, lingatembenuzidwe “kuseŵera,” “kuseketsa,” “kusekerera,” kapena ngakhale “kukondwera.”

c Zofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

KODI MAPULINSIPULO A BAIBULO AŴA ANGATHANDIZE MOTANI . . . KUTETEZERA BANJA LANU?

Chidziŵitso chimapatsa nzeru, imene ingasunge moyo wa munthu.—Mlaliki 7:12.

“Nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu.”—1 Akorinto 3:19.

Mayanjano oipa ayenera kupeŵedwa.—1 Akorinto 15:33.

Pamene kuli kwakuti zosangulutsa zili ndi malo ake, ziyenera kulamuliridwa.—Mlaliki 3:4.

SANAMVE KUKHALA WOMANIDWA

Makolo achikristu Paul ndi mkazi wake, Lu-Ann, amakonza macheza panyumba pawo nthaŵi ndi nthaŵi. Iwo amatsimikiza kuti machezawo amayang’aniridwa bwino ndipo ali a ukulu wosavuta kusamalira. Iwo ali ndi chifukwa chabwino chokhulupirira kuti ana awo amapindula ndi zimenezi.

Lu-Ann akusimba kuti: “Mayi wa mwana wina wa m’kalasi imodzi ndi mwana wanga wamwamuna wazaka zisanu ndi chimodzi, Eric, anandifikira ndi kunena kuti anachitira chifundo Eric chifukwa amakhala payekha ndipo samachitako mapwando a kalasi a tsiku la kubadwa. Ndinati kwa iye: ‘Ndiyamikira kwambiri kuti mumadera nkhaŵa mwana wanga motero. Zimasonyezadi kuti ndinu munthu wokoma mtima kwabasi. Koma mwinamwake palibe chimene ndinganene chimene chingakukhutiritseni kuti Eric samamva kuti akumanidwa.’ Anavomereza zimenezo. Choncho ndinati: ‘Chabwino, musavutike mtima kwambiri, tangomfunsani nokha Eric za mmene amamvera.’ Pamene ine kunalibe, anafunsa Eric kuti, ‘Kodi sumamva kuti ukumanidwa pamene sutengamo mbali m’mapwando abwino ameneŵa a tsiku la kubadwa?’ Iye anampenya kunkhope modabwa, ndi kunena kuti: ‘Kodi muganiza kuti mphindi khumi zokha, timakeke toŵerengeka, ndi nyimbo ndizo phwando? Mukabwere kunyumba kwathu mudzaone phwando lenileni!’” Chisangalalo chenicheni cha mnyamatayo chinapereka yankho lokwanira—samamva kukhala womanidwa kapena kutaya mwaŵi!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena