Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 9/14 tsamba 12-13
  • Zimene Mungachite Kuti Mupewe Matenda a Shuga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Mungachite Kuti Mupewe Matenda a Shuga
  • Galamukani!—2014
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Matenda a Shuga N’chiyani?
  • Vuto la Chithandizo Chake
    Galamukani!—2003
  • Matenda a Shuga “Amapha Mosadziŵika”
    Galamukani!—2003
  • Mmene Baibulo Lingathandizire Odwala Matendaŵa
    Galamukani!—2003
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2003
Onani Zambiri
Galamukani!—2014
g 9/14 tsamba 12-13
Mwamuna ndi mkazi wake akuthamanga kuti alimbitse thupi

Zimene Mungachite Kuti Mupewe Matenda a Shuga

CHIWERENGERO cha anthu odwala matenda a shuga chikuwonjezeka kwambiri moti matendawa angokhala mliri wa padziko lonse. Pali mitundu iwiri ikuluikulu ya matenda a shuga. Mtundu woyamba wa matendawa umagwira ana ndipo padakali pano madokotala sanapeze njira yowapewera. Mtundu wachiwiri ndiye wofala kwambiri ndipo anthu 90 pa 100 alionse amene amadwala matenda a shuga, amadwala mtundu umenewu. M’nkhaniyi tikambirana za mtundu wachiwiriwu.

Kale anthu ankaona kuti akuluakulu okha ndi amene amadwala matenda a shuga a mtunduwu. Koma masiku ano matendawa akumagwiranso ana. Madokotala odziwa bwino za matendawa amanena kuti n’zotheka kupewa mtundu wachiwiriwu. Choncho, kudziwa zambiri zokhudza matendawa kungakuthandizeni kudziwa mmene mungawapewere.a

Kodi Matenda a Shuga N’chiyani?

Anthu amene amadwala matenda a shuga amakhala kuti ali ndi shuga wam’magazi wochuluka kwambiri. Matendawa amapangitsa kuti shuga asamayende bwino kuchokera m’mitsempha kupita m’maselo amene amafunika shugayu kuti amugwiritse ntchito. Zimenezi zimachititsa kuti ziwalo zina zisamagwire bwino ntchito komanso kuti magazi asamayende bwino. Izi zingapangitse kuti zala kapena mapazi a munthu awonongeke kenako n’kudulidwa. Zingapangitsenso kuti munthu achite khungu komanso kuyamba kudwala matenda a impso. Anthu ambiri odwala matenda a shuga amamwalira ndi matenda a mtima kapena a kufa ziwalo.

Chinthu chachikulu chimene chimayambitsa matenda a shuga a mtundu wachiwiriwu ndi kunenepa kwambiri. Madokotala a matendawa amanena kuti munthu akakhala ndi mafuta ambiri pamimba ndi m’chiuno, akhoza kudwala matendawa. Komanso mafuta ambiri akakuta kapamba ndiponso chiwindi, zimapangitsa kuti shuga wa m’magazi asamayende bwino. Ndiye kodi mungatani kuti mupewe matendawa?

Zinthu Zitatu Zimene Zingakuthandizeni Kuti Mupewe Matendawa

1. Muzikayezetsa kuchuluka kwa shuga wam’magazi. Matenda a shuga akayamba, satheka kuwachiza chifukwa padakali pano palibe mankhwala ochiza matendawa. Munthu asanayambe kudwala matendawa, shuga wam’magazi ake amakwera pang’ono kuposa mlingo woyenera. Ichi chimakhala chizindikiro choti akhoza kudwala matendawa. Choncho, kuchuluka kwa shuga m’thupi si kwabwino pa thanzi la munthu. Komabe anthu amene shuga wachuluka pang’ono m’thupi mwawo, akhoza kuyesetsa kuchita zinthu zimene zingathandize kuti mlingo wa shuga ubwerere m’chimake. Ndi bwino kumakayezetsa kuchuluka kwa shuga wam’magazi chifukwa n’zovuta kudziwa ngati shuga wayamba kuchuluka m’thupi. Zili choncho popeza nthawi zambiri sipakhala zizindikiro zilizonse. Lipoti lina linasonyeza kuti padziko lonse, anthu 316 ali ndi vuto lokhala ndi shuga wam’magazi wochulukirapo kuposa mlingo woyenera, koma ambiri sadziwa zimenezi. Mwachitsanzo, United States kokha, anthu 90 pa 100 alionse omwe ali ndi vutoli, sadziwa.

Monga taonera, munthu akakhala ndi shuga wochulukirapo kuposa mlingo woyenera amatha kudwala matenda a shuga. Komatu munthu wotereyu akhoza kudwalanso matenda a maganizo. Ngati ndinu wonenepa kwambiri, simuchita masewera olimbitsa thupi komanso ngati anthu ena akwanu anadwalapo matenda a shuga, n’kutheka kuti muli kale ndi vuto lokhala ndi shuga wam’magazi wochulukirapo kuposa mlingo woyenera. Kuti mudziwe mlingo wa shuga amene ali m’magazi anu, mungachite bwino kukayezetsa.

2. Muzidya zakudya zoyenera. Mungachite bwino kuchita zinthu zotsatirazi ngati mungakwanitse. Musamadye kwambiri. M’malo momwa juwisi wotsekemera kwambiri kapena zakumwa zoziziritsa kukhosi, muzimwa madzi, tiyi kapena khofi. Muzikonda kudya buledi wabulauni, mpunga wabulauni ndi nsima ya mgaiwa. Musamakonde kudya buledi woyera, mpunga woyera kapena nsima yoyera chifukwa zinthu zofunika kwambiri m’thupi zimakhala zitachokamo. Muzidya nsomba, mtedza, nyemba komanso nyama yopanda mafuta ambiri.

1. Saladi; 2. Sikelo

3. Muzichita masewera olimbitsa thupi. Kuchita masewera olimbitsa thupi kungathandize kuti shuga wanu wam’magazi asachuluke komanso kuti musanenepe kwambiri. Katswiri wina ananena kuti, ndi bwino kuchepetsa nthawi imene mumaonera TV kuti muzipeza nthawi yochita masewera olimbitsa thupi.

Ngati ku mtundu kwanu kuli matenda a shuga, simungathe kusintha zimenezi. Komabe monga taonera m’nkhaniyi mungathe kuchita zinthu zimene zingathandize kuti inuyo musadwale matendawa. Kuchita zimenezi kungaoneke kovuta kwambiri, komatu n’kothandiza zedi.

a Magazini ya Galamukani! sisankhira anthu zochita pa nkhani ya zakudya kapena masewera olimbitsa thupi. Aliyense ayenera kusankha yekha. Komanso ndi bwino kufunsa dokotala wodziwa bwino za matendawa musanasankhe zochita pa nkhaniyi.

Anafotokoza Zimene Anachita Atamva Kuti Akhoza Kudwala Matenda a Shuga

Munadziwa bwanji kuti mukhoza kudwala matenda a shuga?

Nditapeza ntchito yatsopano, anapita nane kuchipatala kuti akandiyeze mmene m’thupi mwanga mulili. Dokotala anandiuza kuti ndikhoza kudwala matenda a shuga ngati nditapanda kusamala. Panali mavuto atatu amene akanapangitsa kuti ndidwale matendawa. (1) Ku mtundu kwathu komanso m’banja lathu munali anthu amene anadwalapo matenda a shuga, (2) ndinali wonenepa kwambiri komanso (3) sindinkachita masewera olimbitsa thupi. Popeza panalibe chimene ndikanachita kuti ndithetse vuto loyambalo, ndinaganiza zothetsa mavuto awiri omalizawo.

Ndiye munatani?

Ndinapita kwa dokotala wa matendawa ndipo anandifotokozera mmene chakudya chimene timadya, kusachita masewera olimbitsa thupi komanso kunenepa kwambiri, kungapangitsire munthu kudwala matenda a shuga. Atandiuza zimenezi, ndinasintha kadyedwe. Mwachitsanzo, ndinkayamba kaye ndadya ndiwo zamasamba zambiri ndisanadye chakudya. Zimenezi zinkandithandiza kuti ndisadye kwambiri zakudya zonenepetsa. Ndinayambanso kuchita masewera olimbitsa thupi.

Kodi zimenezi zinakuthandizani bwanji?

M’mene pankatha chaka chimodzi ndi hafu, ndinali nditachepa thupi kuyerekeza ndi mmene ndinalili poyamba ndipo sindinkalemedwanso ndi thupi langa. Matenda a shuga ndi oopsa kwambiri ndipo tiyenera kuchita chilichonse chimene tingathe kuti tiwapewe.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena