Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 10/13 tsamba 8-11
  • Zinthu Zitatu Zimene Sitingagule ndi Ndalama

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zinthu Zitatu Zimene Sitingagule ndi Ndalama
  • Galamukani!—2013
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mungatani Kuti Musakhale Wokonda Ndalama?
    Galamukani!—2015
  • Kodi Ndalama ndi Zimene Zimabweretsa Mavuto Onse?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Muzigwiritsa Ntchito Bwino Ndalama
    Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
  • Ndalama
    Galamukani!—2014
Onani Zambiri
Galamukani!—2013
g 10/13 tsamba 8-11
[Chithunzi patsamba 8]

NKHANI YA PACHIKUTO

Zinthu Zitatu Zimene Sitingagule ndi Ndalama

ANTHU ambiri masiku ano amakonda kugula zinthu. Ndipo n’zomvetsa chisoni kuti amachitabe zimenezi ngakhale kuti zingaike pangozi ntchito yawo komanso katundu wawo, kuphatikizapo nyumba.

Amalonda amakopa anthu ngati amenewa ndipo akamatsatsa malonda awo, amafuna kuti anthu aziona kuti ayenera kukhala ndi nyumba yaikulu, galimoto komanso zovala zapamwamba. Ndipo ngati alibe ndalama, amalondawo amawalimbikitsa kuti akhoza kugula zinthuzo pa ngongole. Anthu ambiri amalolera kuchita zimenezi n’cholinga choti azioneka ngati olemera, ngakhale atakhala kuti ali kale ndi ngongole zambiri.

Koma kenako amayamba kukumana ndi mavuto. Buku lina linanena kuti: “Munthu amene amagula katundu wapamwamba pa ngongole n’cholinga choti azioneka ngati wolemera, amafanana ndi munthu amene akusuta chamba n’cholinga choti asangalale. N’zoona kuti pogulapo akhoza kumaona ngati wagula zinthuzo motchipa komanso akhoza kuonekadi kuti ndi wolemera. Koma zimenezi sizichitika kwa nthawi yaitali chifukwa pamapeto pake amakhala wopanda ndalama komanso wosasangalala.”—The Narcissism Epidemic.

Baibulo limasonyeza kuti n’kupanda nzeru “kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake.” (1 Yohane 2:16) Munthu akamakonda kwambiri kugula katundu, amalephera kupeza zinthu zomwe ndi zofunika kwambiri pa moyo wake, ndipo zinthu zimenezi ndi zoti sangagule ndi ndalama. Tiyeni tione zinthu zitatu zimene sitingagule ndi ndalama.

1. BANJA LOGWIRIZANA

Mtsikana wina wa ku United States, dzina lake Brianne,a ananena kuti bambo ake amaona kuti ntchito yawo komanso ndalama zimene amapeza ndi zinthu zofunika kwambiri kuposa chilichonse. Iye anati: “Tili ndi chilichonse chimene timafunikira pa moyo wathu koma bambo anga sakhala pakhomo, amangokhalira kuyendayenda. Ndikudziwa kuti amachita zimenezi chifukwa cha ntchito yawo, komabe ndimaona kuti ayeneranso kumapeza nthawi yokhala ndi banja lawo.”

[Chithunzi patsamba 8]

Zoti muganizire: Kodi mukuganiza kuti ndi zinthu ziti zimene zingadzachititse kuti bambo a Brianne adzanong’oneze bondo? Kodi kukonda kwambiri ndalama kungakhudze bwanji ubwenzi wawo ndi mwana wawoyo? Kodi bambowa angamachite chiyani kuti banja lawo lizisangalala?

Mfundo za m’Baibulo zofunika kuziganizira:

  • “Kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse, ndipo pokulitsa chikondi chimenechi, ena . . . adzibweretsera zopweteka zambiri pathupi lawo.”—1 Timoteyo 6:10.

  • “Ndi bwino kudya zamasamba koma pali chikondi, kusiyana ndi kudya nyama ya ng’ombe yamphongo yodyetsedwa bwino pali chidani.”—Miyambo 15:17.

Mfundo yofunika: Ndalama sizingapangitse kuti banja likhale logwirizana. Banja lingakhale logwirizana ngati onse m’banjamo amapeza nthawi yochezera limodzi komanso ngati amakondana.—Akolose 3:18-21.

2. CHITETEZO CHENICHENI

Mtsikana wina wazaka 17, dzina lake Sarah ananena kuti: “Mayi anga amandiuza kuti ndidzakwatiwe ndi mwamuna wolemera komanso ndidzapeze ntchito yapamwamba kuti ndidzathe kudzisamalira kwa moyo wanga wonse. Nthawi zonse amangoganizira za mmene angapezere ndalama basi.”

[Chithunzi patsamba 8]

Zoti muganizire: Mukamaganizira za tsogolo lanu, kodi ndi zinthu ziti zomwe zimakudetsani nkhawa kwambiri? Nanga munthu angadziwe bwanji kuti wayamba kudera nkhawa kwambiri za tsogolo lake? Kodi zimene mayi ake a Sarah ananena zinalidi zothandiza kwa mwana wawoyo?

Mfundo za m’Baibulo zofunika kuziganizira:

  • “Lekani kudziunjikira chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zimawononga, ndiponso pamene mbala zimathyola ndi kuba.”—Mateyu 6:19.

  • “Simukudziwa kuti moyo wanu udzakhala wotani mawa.”—Yakobo 4:14.

Mfundo yofunika: Ndalama sizingapangitse kuti tikhale otetezeka chifukwa zikhoza kubedwa. Komanso sizingatiteteze ku matenda kapena imfa. (Mlaliki 7:12) Baibulo limasonyeza kuti munthu amakhala wotetezeka ngati amadziwa Mulungu komanso chifuniro chake.—Yohane 17:3.

3. KUKHALA WOKHUTIRA

Mtsikana wina wazaka 24, dzina lake Tanya, ananena kuti: “Makolo anga anandiphunzitsa kukhala ndi moyo wosafuna zinthu zambiri. Nthawi zambiri ineyo ndi mkulu wanga tinkangokhala ndi zinthu monga zovala, zakudya ndi pogona, komabe tinkasangalala.”

[Chithunzi patsamba 8]

Zoti muganizire: N’chifukwa chiyani zingakhale zovuta kuti munthu amene ali ndi zofunika pamoyo zokha akhale wokhutira? Kodi inuyo mumapereka chitsanzo chotani kwa banja lanu pa nkhani ya ndalama?

Mfundo za m’Baibulo zofunika kuziganizira:

  • “Pokhala ndi chakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutira ndi zinthu zimenezi.”—1 Timoteyo 6:8.

  • “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”—Mateyu 5:3.

Zoti muganizire: Tikhoza kukhala okhutira ngakhale titakhala kuti tilibe ndalama kapena katundu. Ndipotu Baibulo limati: “Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.” (Luka 12:15) Munthu angakhalenso wokhutira ngati atadziwa mayankho a mafunso ofunika otsatirawa:

  • N’chifukwa chiyani tili ndi moyo?

  • Kodi ndi zinthu zabwino ziti zimene zichitike kutsogoloku?

  • Kodi ndingatani kuti ndithetse njala yanga yauzimu?

A Mboni za Yehova, omwe amafalitsa magaziniyi, akhoza kukuthandizani kupeza mayankho a mafunso amenewa.

a Tasintha mayina m’nkhaniyi.

Kodi Ndalama Zingakuthandizeni Kuti Muzisangalala?

Buku lina linanena kuti: “Anthu ambiri okonda ndalama samakhala osangalala komanso amavutika maganizo. Ngakhale anthu amene alibe ndalama koma amangolakalaka atakhala ndi ndalama zambiri, amavutikabe maganizo komanso amavutika ndi matenda ngati zilonda za pakhosi, msana, mutu ndipo nthawi zambiri amamwa kwambiri mowa kapena mankhwala osokoneza bongo. Zimenezi zikusonyeza kuti kuyesetsa kuti ukhale ndi ndalama zambiri kumabweretsa mavuto ambiri.”—The Narcissism Epidemic.

“Anthu Asintha Kaonedwe ka Zinthu”

Buku lina linanena kuti: “Ophunzira a m’zaka za m’ma 1960 ndi kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1970 atafunsidwa chifukwa chimene ankapitira kukoleji, ambiri ankayankha kuti akufuna ‘kudzakhala munthu wophunzira kwambiri’ kapena ‘kukaphunzira mmene zinthu zimayendera pa moyo.’ Ndi ochepa amene ankanena kuti cholinga chawo chinali choti azidzapeza ndalama zambiri akadzamaliza maphunziro awo. Koma kungoyambira cha mma 1990, ophunzira ambiri amanena kuti cholinga chawo chachikulu chopitira kukoleji n’choti azidzapeza ndalama zambiri. . . . Zimenezi zachitika pa nthawi imenenso chiwerengero cha achinyamata amene amadzipha komanso amavutika maganizo chawonjezereka kwambiri.”—The Price of Privilege, lolembedwa ndi Dr. Madeline Levine.

Anthu Amangogula Zinthu Kuti Asangalale

Buku lina linanena kuti anthu amene amakonda kugula zinthu ndi amene mabanja awo sakuyenda bwino, amene m’dera lawo zinthu sizikuyenda bwino komanso amene akhumudwa ndi zimene zikuchitika m’matchalitchi mwawo. Iwo amangogula zinthu kuti asangalale ndipo amamva bwino akachita zimenezi. Linanenanso kuti: “Kugula zinthu kumatipangitsa kumva kuti tili ndi mphamvu yoyendetsa zinthu. Timaona kuti tikamagula zinthu ndiye kuti tikulamulira wogulitsayo. Koma zimenezi si zoona . . . Amene ali ndi mphamvu yolamulira ndi makampani akuluakulu komanso anthu amene amawatsatsira malonda, omwe amalipidwa n’cholinga choti azinamiza anthu kuti akagula katundu winawake akhala osangalala.”—The Price of Privilege, lolembedwa ndi Dr. Madeline Levine.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena