Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g02 8/8 tsamba 12-13
  • Kodi Mulungu Amachiona Bwanji Chiwawa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mulungu Amachiona Bwanji Chiwawa?
  • Galamukani!—2002
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chiwawa Chinayamba Kalekale
  • Kutsanzira Ziwanda
  • Mulungu Amadana ndi Chiwawa
  • Kodi Chiwawa Chidzatha N’komwe?
  • Chiwawa
    Galamukani!—2015
  • Kodi Zachiwawa Zidzatha Padzikoli?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Muzichitira Ena Zimene Mulungu Amafuna
    Muzikumbukira Tsiku la Yehova Nthawi Zonse
  • Zachiwawa Zili Paliponse
    Galamukani!—2012
Onani Zambiri
Galamukani!—2002
g02 8/8 tsamba 12-13

Lingaliro la Baibulo

Kodi Mulungu Amachiona Bwanji Chiwawa?

CHIWAWA n’chofala kwambiri ndipo n’chosiyanasiyana. Kupatulapo chiwawa cha kunkhondo, palinso chiwawa chokhudzana ndi maseŵera olimbitsa thupi, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, magulu a achinyamata osokoneza, kusukulu ndiponso kuntchito, komanso chiwawa chochitika panthaŵi ya chisangalalo. Ngakhalenso m’mabanja ambiri mukuoneka kuti mukuchitika chiwawa. Mwachitsanzo, atafufuza posachedwapa zinaoneka kuti ku Canada azibambo ndi azimayi oposa miliyoni anachitidwa chiwawa ndi amuna kapena akazi awo kamodzi kapena kuposapo pazaka zisanu zimene zangopitazi. Ofufuza ena nawo atafufuza anati pafupifupi theka la azibambo omenya akazi awo amazunzanso ana awo mwankhanza.

Inde, pali anthu enanso ambiri amene monga inuyo amaonanso kuti zochitika zachiwawa zoterezi n’zodandaulitsa kwambiri. Komabe masiku ano, chiwawa chasanduka mbali yofunika kwambiri ya zinthu zosangalatsa. Anthu akutengeka mtima ndi chiwawa chongoyerekezera chimene amachionetsa m’mafilimu komanso pa zochitika zenizeni zankhanza zimene amazionetsa pa TV. Anthu m’mayiko ambiri akukonda kwambiri maseŵera a nkhonya ndiponso maseŵera ena achiwawa. Koma kodi Mulungu amachiona bwanji chiwawa?

Chiwawa Chinayamba Kalekale

Chiwawa chinayamba kale kwambiri. M’Baibulo, nkhani yoyamba imene munthu anachitapo chiwawa anaifotokoza pa Genesis 4:2-15. Kaini, mwana woyamba wa Adamu ndi Hava anachitira kaduka mchimwene wake Abele n’kumupha mwadala. Kodi zitatero Mulungu anatani? Baibulo limafotokoza kuti Yehova Mulungu anam’langa kwambiri Kaini chifukwa chakupha mchimwene wakeyo.

Pa Genesis 6:11, timaŵerenga kuti patatha zaka zoposa 1,500 chichitikireni zimenezo, dziko lapansi “linadzala ndi chiwawa.” Kodi apanso zitatero Mulungu anatani? Iye analamula Nowa wolungamayo kumanga chingalawa choti chipulumutse iye pamodzi ndi banja lake panthaŵi imene Yehovayo ankabweretsa chigumula padzikoli, ‘powononga’ anthu achiwawawo. (Genesis 6:12-14, 17) Koma kodi n’chiyani chimene chinachititsa anthu kuti azikakamira kuchita zachiwawa?

Kutsanzira Ziwanda

Nkhani yopezeka m’buku la Genesis imanena poyera kuti ana aamuna a Mulungu, angelo osamvera anavala matupi a anthu n’kukwatira akazi kenaka n’kubereka ana. (Genesis 6:1-4) Ana amene anaberekawo otchedwa Anefili, anali anthu ojintcha mopitirira muyeso ndiponso otchuka. Chifukwa cha ziwanda zomwe zinali abambo awo, iwo anasanduka anthu achiwawa chosaneneka. Madzi a chigumula atakwera n’kudzaza dziko lapansili, anthu oipa ankhanzaŵa anatheratu. Koma zikuoneka kuti ziwandazo zinasandukanso anthu auzimu n’kubwerera kudziko la mizimu.

Baibulo limanena momveka kuti kuyambira nthaŵi imeneyo, angelo opandukaŵa akhala akulamulira maganizo a anthu mwamphamvu kwambiri. (Aefeso 6:12) Mtsogoleri wawo Satana, amatchedwa “wambanda” woyambirira. (Yohane 8:44) Choncho n’kulondola ndithu kunena kuti chiwawa chimene chimachitika padzikoli ndi chauchiwanda kapena kuti chausatana.

Baibulo limatichenjeza kuti chiwawa chili ndi mphamvu yokopa. Pa Miyambo 16:29, ilo limati: “Munthu wa chiwawa akopa mnzake, namuyendetsa m’njira yosakhala bwino.” Anthu ambiri masiku ano akhala akukopeka ndi makhalidwe achiwawa n’kumawaona ngati abwino, n’kumawalimbikitsa kapena kuwachita kumene. Ndiponso anthu mamiliyoni ambiri akhala akukopeka ndi zinthu zosangalatsa zimene zimatama chiwawa. Mawu a pa Salmo 73:6 tingawagwiritse ntchito molondola pofotokoza khalidwe la anthu amasiku ano. Wamasalmoyo anati: “Kudzikuza kunga unyolo pakhosi pawo; achivala chiwawa ngati malaya.”

Mulungu Amadana ndi Chiwawa

Kodi Akristu ayenera kukhala ndi khalidwe lotani m’dziko lachiwawali? Nkhani ya m’Baibulo yonena za ana aamuna a Yakobo, Simeoni ndi Levi imatipatsa malangizo abwino. Mchemwali wawo Dina anayamba dala kugwirizana ndi anthu amakhalidwe oipa a ku Sekemu. Zimenezi zinapangitsa kuti iye agonedwe mokakamizidwa ndi munthu wa ku Sekemuko. Pobwezera, Simeoni ndi Levi anapha amuna onse a ku Sekemu mopanda chisoni. Kenaka Yakobo atauzidwa ndi Mulungu, anatemberera mkwiyo wopitirira muyeso wa ana akewo ndi mawu akuti: “Simeoni ndi Levi ndiwo abale; zida za mphulupulu ndizo malupanga awo. Mtima wangawe, usaloŵe mu chiungwe chawo; ulemerero wanga, usadziphatike pa masonkhano awo.”—Genesis 49:5, 6.

Mogwirizana ndi mawu ameneŵa, Akristu amapeŵa kugwirizana ndi anthu amene amalimbikitsa kapena amene amachita zachiwawa. N’zoonekeratu kuti Mulungu amadana ndi anthu amene amalimbikitsa zachiwawa. Baibulo limanena kuti: “Yehova ayesa wolungama mtima: koma moyo wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa.” (Salmo 11:5) Akristu amalimbikitsidwa kupeŵa mtundu wina uliwonse wa kukwiya mopitirira muyeso, ngakhale kulankhula mawu okhadzula.—Agalatiya 5:19-21; Aefeso 4:31.

Kodi Chiwawa Chidzatha N’komwe?

Mneneri wakale Habakuku anafunsa Yehova Mulungu kuti: ‘Ndidzafuula mpaka liti . .  . za chiwawa?’ (Habakuku 1:2) Mwinatu inunso munafunsapo funso lotere. Mulungu anam’yankha Habakuku polonjeza kuti adzachotsa “woipa.” (Habakuku 3:13) Buku laulosi la Yesaya nalonso limatilimbitsa mtima. M’buku limenelo Mulungu amalonjeza kuti: “Chiwawa sichidzamvekanso m’dziko mwako, kupululutsa pena kupasula m’malire ako.”—Yesaya 60:18.

Mboni za Yehova sizikayika ngakhale pang’ono kuti posachedwa pompa Mulungu adzachotsa padzikoli mtundu wina uliwonse wa chiwawa ndiponso anthu amene amalimbikitsa chiwawacho. Panthaŵi imeneyo, mmalo modzaza chiwawa, “dziko lapansi lidzadzazidwa ndi chidziŵitso cha ulemerero wa Yehova, monga madzi aphimba pansi pa nyanja.”—Habakuku 2:14.

[Chithunzi patsamba 12]

Chiwawa chinayamba pamene Kaini anapha Abele

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena