Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ypq funso 7 tsamba 21-23
  • Kodi Ndingatani Ngati Wina Akundikakamiza Kuti Ndigone Naye?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndingatani Ngati Wina Akundikakamiza Kuti Ndigone Naye?
  • Mayankho a Mafunso 10 Omwe Achinyamata Amadzifunsa
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Kugonana Tili Pachibwenzi Kungachititse Kuti Tizikondana Kwambiri?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
  • Kodi Kugonana Tili Pachibwenzi Kungachititse Kuti Tizikondana Kwambiri?
    Galamukani!—2010
  • Ndingatani Ngati Anzanga Akundikakamiza Kugonana?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Kodi Ndingafotokoze Bwanji Zimene Ndimakhulupirira pa Nkhani ya Kugonana?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
Onani Zambiri
Mayankho a Mafunso 10 Omwe Achinyamata Amadzifunsa
ypq funso 7 tsamba 21-23
Mtsikana akukana kwamtuwagalu zoti agone ndi mnyamata

7

Kodi Ndingatani Ngati Wina Akundikakamiza Kuti Ndigone Naye?

KODI YANKHO LA FUNSOLI LINGAKUTHANDIZENI BWANJI?

Zimene mungasankhe pa nkhaniyi zingakhudze moyo wanu wonse.

KODI MUKANAKHALA INUYO MUKANATANI?

Tiyerekeze kuti patangodutsa miyezi iwiri kuchokera pamene Hilda anadziwana ndi Mike, anayamba kucheza kwambiri ngati anadziwana kalekale. Ankatumizirana mameseji pafupipafupi ndiponso kucheza pa foni kwa nthawi yaitali. Eniakewo ankangoona kuti zonse zili bwino. Pa miyezi iwiriyo, iwo ankangogwirana manja kapena kukisana pang’ono.

Koma tsiku lina, Mike anayamba kusonyeza kuti akufuna kucheza kwawo kutafika pena. Hilda sankafuna kuchita zimene Mike ankafunazo koma ankaopa kuti akakana chibwenzi chawo chitha. Iye ankamukonda kwambiri Mike chifukwa zimene ankamuchitira zinkamupangitsa kudziona kuti ndi wokongola komanso wofunika. Mumtima mwake ankadziuza kuti, ‘Ine ndi Mike timakondana kwambiri.’

Kodi inuyo mukanakhala Hilda ndipo muli pa msinkhu woti mutha kukhala ndi chibwenzi, mukanatani?

MFUNDO YOFUNIKA KUIGANIZIRA

Akugwiritsa ntchito malaya poyeretsa

Kugonana ndi mphatso imene Mulungu anapereka kwa anthu okwatirana. Koma anthu akagonana asanalowe m’banja amakhala kuti akugwiritsa ntchito mphatsoyi molakwika. Zili ngati akutenga malaya okongola amene munthu wina anawapatsa n’kumayeretsera m’nyumba

Munthu akapanda kutsatira lamulo linalake amakumana ndi mavuto. N’zimenenso zingachitike ngati mutapanda kutsatira lamulo la m’Baibulo lakuti: “Mukhale oyera mwa kupewa dama.”—1 Atesalonika 4:3.

Koma kodi munthu amene sangatsatire lamulo limeneli angakumane ndi mavuto otani? Baibulo limanena kuti: “Amene amachita dama amachimwira thupi lake.” (1 Akorinto 6:18) Kodi zimenezi ndi zoona?

Kafukufuku amasonyeza kuti achinyamata ambiri amene amayamba zogonana asanalowe m’banja amakumana ndi mavuto otsatirawa:

  • KUVUTIKA MAGANIZO. Amadziimba mlandu pambuyo pake.

  • KUSAKHULUPIRIRANA. Amayamba kudzifunsa kuti, ‘Kodi amene ndagona nayeyu wagona ndi anthu angati?’

  • KUKHUMUDWA. Atsikana ambiri amafuna mnyamata amene angawateteze, osati kuwadyera masuku pamutu. Anyamata ambiri akagona ndi mtsikana sakopeka nayenso ndipo amayamba kumuona ngati wopanda ntchito.

  • Dziwani izi: Thupi lanu ndi lamtengo wapatali kwambiri. Choncho, mukagona ndi munthu musanalowe m’banja mumakhala kuti mwadzitchipitsa.—Aroma 1:24.

Sonyezani kuti ndinu olimba mtima ndipo mukhoza “kupewa dama.” (1 Atesalonika 4:3) Mukadzalowa m’banja mudzakhala ndi mwayi wogonana popanda kuda nkhawa kapena kudziimba mlandu ngati mmene zimakhalira ndi amene amagonana asanalowe m’banja.—Miyambo 7:22, 23; 1 Akorinto 7:3.

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

  • Kodi munthu amene amakukondanidi angachite zinthu zimene zingakubweretsereni mavuto?

  • Kodi munthu amene amakukondani angakuuzeni kuti muchite zinthu zomwe zingasokoneze ubwenzi wanu ndi Mulungu?—Aheberi 13:4.

MALANGIZO KWA ATSIKANA

Mtsikana wakhala pansi n’kumaganiza

Anyamata ambiri amanena kuti sangakwatire mtsikana amene anagonapo naye. Koma n’chifukwa chiyani amanena zimenezi? Chifukwa chakuti amafuna kukwatira mkazi woti sanagonepo ndi mwamuna.

Kodi zimenezi zikukudabwitsani mwinanso kukukhumudwitsani? Dziwani kuti anthu opanga mafilimu komanso mapulogalamu a pa TV amachititsa achinyamata kuti aziona ngati kugonana asanalowe m’banja n’kosangalatsa, kulibe vuto lililonse komanso ndi njira yosonyezera chikondi.

Koma musapusitsike. Dziwani kuti munthu amene amakunyengererani kuti mugone naye, ndi wodzikonda.—1 Akorinto 13:4, 5.

MALANGIZO KWA ANYAMATA

Mtsikana wakhala pansi n’kumaganiza

Ngati muli ndi chibwenzi, dzifunseni kuti, ‘Kodi mtsikanayu ndimamukondadi?’ Ngati mumamukonda, mungasonyeze zimenezi poyesetsa kutsatira malamulo a Mulungu, popewa kukhala pamalo amene mukhoza kuyesedwa komanso pochita zinthu zosonyeza kuti mumamuganizira.

Mukamachita zimenezi, mtsikanayo azikuonani ngati mmene Msulami ankaonera chibwenzi chake. Iye anati: “Wachikondi wanga ndi wanga, ndipo ine ndine wake.” (Nyimbo ya Solomo 2:16) Mwachidule tingati adzakukondani kwambiri.

MFUNDO YOTHANDIZA

Ngati munthu wina atakunyengererani kuti mugone naye pokuuzani kuti, “Ngati umandikondadi, ulola,” muyankheni molimba mtima kuti, “Ukanakhala kuti iweyo umandikondadi sukanandiuza kuti tichite zimenezi.”

Mukakhala ndi munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi mnzanu, muzitsatira mfundo iyi: Ngati zimene mukufuna kuchita simungazichite pamaso pa makolo anu, ndiye kuti simuyenera kuzichita.

ZOTI NDICHITE

  • Munthu wina akadzakuuzani kuti mugone naye, kodi mudzachita chiyani?

  • Kodi ndi zinthu ziti zimene zingapangitse kuti zikuvuteni kukana wina atakuuzani kuti mugone naye?

  • Pofuna kupewa zimenezi, mungachite zotani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena