Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 8/12 tsamba 14-15
  • Kodi Mulungu Amamva Mapemphero Pokhapokha Ngati Muli Pamalo Enaake?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mulungu Amamva Mapemphero Pokhapokha Ngati Muli Pamalo Enaake?
  • Galamukani!—2012
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mulungu Sakhala M’nyumba Zopangidwa Ndi Manja
  • Atumiki a Mulungu Amakondana Ngati Ana a Banja Limodzi
  • Osaleka Kusonkhana Pamodzi
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kodi Akristu Ayenera Kupita ku Tchalitchi?
    Galamukani!—2001
  • Yesu Atiphunzitsa Ife Kupemphera
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • 5 Kodi Tiyenera Kupemphera Pamalo Ati, Nanga Nthawi Yanji?
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Galamukani!—2012
g 8/12 tsamba 14-15

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Mulungu Amamva Mapemphero Pokhapokha Ngati Muli Pamalo Enaake?

ANTHU ambiri amakonda kupita kutchalitchi, kukachisi kapena kumalo enaake kukapemphera. Ena amayenda ulendo wautali kupita kukangoona malo awo apadera opempherera. Kodi inuyo mumaona kuti muyenera kupita kukachisi, kutchalitchi kapena kumalo enaake kuti mukapemphere? Kapena mumaona kuti mukhoza kupemphera kwa Mulungu nthawi iliyonse komanso pamalo alionse? Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhaniyi?

Adamu ndi Hava atangolengedwa kumene, kunalibe nyumba yopempherera. Iwo ankakhala m’munda wokongola kwambiri wotchedwa Edeni. (Genesis 2:8) Ankatha kulankhulana ndi Mulungu ali m’munda umenewu. Kenako anthu anayamba kuchulukana ndipo anthu ena olungama monga Nowa “anayenda ndi Mulungu woona,” ngakhale kuti kunalibe malo opempherera. (Genesis 6:9) Anthu olungamawa ankakonda kwambiri Mulungu komanso kupemphera ndipo Yehova ankawakonda ngakhale kuti sankapempherera m’tchalitchi kapena malo enaake apadera.

Mulungu Sakhala M’nyumba Zopangidwa Ndi Manja

Atumiki ena a Mulungu ankadziwa kuti Mulungu, yemwe analenga dziko lapansi komanso zinthu za m’mlengalenga, sakhala m’nyumba zomangidwa ndi anthu. Mfumu Solomo anafunsa kuti: “Kodi Mulungu angakhaledi ndi anthu padziko lapansi? Taonani! Kumwamba, ngakhale kumwambamwamba, simungakwaneko.” (2 Mbiri 6:18) Poyamba Aisiraeli ankasonkhana m’chihema ndipo kenako anayamba kusonkhana m’kachisi chaka chilichonse kuti azichita zikondwerero mogwirizana ndi Chilamulo. (Ekisodo 23:14-17) Ngakhale kuti iwo anali ndi malo olambirira, ankatha kupemphera kwa Mulungu nthawi iliyonse, kaya polima, podyetsera ziweto, pamene ali okha kapena pocheza ndi banja lawo.—Salimo 65:2; Mateyu 6:6.

Nafenso tikhoza kupemphera kwa Mulungu kwina kulikonse komanso nthawi ina iliyonse. Yesu anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri chifukwa ankakonda kupita kwayekha kukapemphera. (Maliko 1:35) Mwachitsanzo, nthawi ina “anapita kuphiri kukapemphera, ndipo anachezera kupemphera kwa Mulungu usiku wonse.”—Luka 6:12.

Mofanana ndi Ayuda onse, Yesu ankapita kukachisi wa ku Yerusalemu kukachita nawo zikondwerero. (Yohane 2:13, 14) Komabe iye nthawi ina analosera kuti idzafika nthawi imene anthu sazidzalambiranso m’kachisi. Iye ananena zimenezi pamene ankalankhula ndi mayi wachisamariya pafupi ndi phiri lina pomwe panali kachisi wa anthu a ku Samariya. Yesu anauza mayiyo kuti: “Nthawi idzafika pamene anthu inu simudzalambira Atate m’phiri ili kapena ku Yerusalemu.” Kenako anamuuza kuti nthawi idzafika pomwe: “Olambira oona adzalambira Atate motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi.”—Yohane 4:21, 23.

Mfundo imeneyi ikusonyeza kuti Yesu ankaona kuti kulambira Mulungu mochokera pansi pa mtima ndi kumene kuli kofunika kwambiri kuposa nyumba zomangidwa ndi anthu. Koma kodi Yesu ankatanthauza kuti Akhristu sazidzagwiritsa ntchito nyumba zomangidwa ndi anthu polambira Mulungu? (Machitidwe 11:26) Ayi, ndipo pali chifukwa chake tikunena choncho.

Atumiki a Mulungu Amakondana Ngati Ana a Banja Limodzi

Atumiki a Mulungu amakhala ngati anthu a banja limodzi. (Luka 8:21) Anthu a m’banja limodzi amachitira zinthu limodzi monga kudyera limodzi ndipo zimenezi zimathandiza kuti banjalo likhale logwirizana. N’chimodzimodzinso polambira Mulungu. Misonkhano yachikhristu ndi phwando la chakudya chimene chimalimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova komanso Akhristu anzathu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane.”—Aheberi 10:24, 25.

Choncho atumiki a Yehova amadziwa kuti kusonkhana ndi kofunika chifukwa kumathandiza Mkhristu aliyense kuti akhale ndi makhalidwe achikhristu omwe sangakhale nawo ngati atamangopemphera kwayekha. Ena mwa makhalidwe amenewa ndi chikondi, kukhululukira ena, chifundo, kufatsa komanso kuchita zinthu mwamtendere.—2 Akorinto 2:7; Agalatiya 5:19-23.

Ndiyeno kodi Akhristu oyambirira ankasonkhana kuti? Nthawi zambiri ankasonkhana m’nyumba za anthu. (Aroma 16:5; Akolose 4:15) Mwachitsanzo, mtumwi Paulo analembera kalata Filimoni ndipo ananenanso kuti kalatayo ipite ku “mpingo umene umasonkhana m’nyumba”a mwa Filimoniyo.—Filimoni 1, 2.

Mofanana ndi nthawi imeneyo, Akhristu masiku ano safunikira nyumba zomangidwa mogometsa zopemphereramo. M’malomwake amangofunikira malo abwino okwanira anthu onse amene angabwere. A Mboni za Yehova ali ndi malo oterewa omwe amawatchula kuti Nyumba ya Ufumu. N’kutheka kuti kumene mumakhala kulinso Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova. Nyumba zimenezi sizimakhala zomangidwa mogometsa ndipo pa misonkhano imene imachitikira kumeneko amaimba nyimbo, kupemphera komanso kuphunzira Baibulo.

Kuwonjezera pamenepa, a Mboni za Yehova amapempheranso m’mabanja mwawo komanso aliyense payekha. Zimenezi n’zogwirizana ndi lemba la Yakobo 4:8 lomwe limati: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”

[Mawu a M’munsi]

a Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “mpingo” pa lembali amamasuliridwanso kuti “tchalitchi” m’maBaibulo ena.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● Kodi Mulungu amakhala m’nyumba zomangidwa ndi anthu?—2 Mbiri 6:18.

● Kodi nthawi ina Yesu anapita kuti komwe anakachezera kupemphera?—Luka 6:12.

● N’chifukwa chiyani Akhristu amasonkhana kuti azilambira pamodzi?—Aheberi 10:24, 25.

[Mawu Otsindika patsamba 15]

Kodi inuyo mumaona kuti Mulungu angamve mapemphero anu pokhapokha ngati muli pamalo enaake?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena