Kodi Zinangochitika Zokha?
Mano Odzinola Okha a Kanyama Kam’nyanja
● Pogwiritsa ntchito mano ake asanu, kanyama kameneka kamabowola mwala n’kupanga phanga loti kazibisalamo. Ngakhale kuti kamagwiritsa ntchito mano pobowola phangalo, manowo amakhalabe akuthwa. Pulofesa Pupa Gilbert, yemwe amaphunzitsa payunivesite ya Wisconsin–Madison, m’dziko la United States, anati: “Zimenezi sizingachitike ndi chipangizo chilichonse chodulira kapena kupalira zinthu chimene anthu akuchidziwa kapena chimene amagwiritsa ntchito.” Kodi chinsinsi cha kanyama kameneka chagona pati?
Taganizirani izi: Mano a kanyama kameneka amakhala ndi tinthu ting’onoting’ono timene timachititsa kuti manowa akhale olimba. Komabe, malinga ndi zimene Gilbert ananena, “dzino lililonse lili ndi malo ake amene limabenthukira.” Tinthu tosalimba timene timakhala pamalo amenewa timachititsa kuti dzinolo lizibenthuka mosavuta, ndipo mbali yotsalayo imakhalanso yakuthwa. Dzinoli silibuntha chifukwa chakuti limakhalabe likukula mbali imodzi ndipo mbali ina limadzinola lokha. Gilbert ananena kuti dzino la kanyama kameneka ndi “chimodzi mwa zinthu zochepa kwambiri m’chilengedwechi zimene zimadzinola zokha.”
Akatswiri amene amagwiritsa ntchito zipangizo zosiyanasiyana amachita chidwi ndi mmene dzino la kanyamaka limagwirira ntchito. Akuti kudziwa bwinobwino mmene limagwirira ntchito kungathandize kuti apange zipangizo zotha kudzinola zokha. Gilbert anati: “Kudziwa mmene dzino la kanyamaka limagwirira ntchito n’kothandiza kwambiri.”
Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti kanyama kameneka kakhale ndi dzino lotha kudzinola lokha, kapena zimenezi ndi umboni wakuti pali winawake wanzeru amene analenga kanyamaka?
[Chithunzi patsamba 16]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Dzino likumera
Mbali yokhala ngati fupa
Dzino lakuthwa
[Chithunzi patsamba 16]
Kanyamaka
[Chithunzi patsamba 16]
Mano asanu
[Mawu a Chithunzi patsamba 16]
Both photos: Courtesy of Pupa Gilbert/University of Wisconsin-Madison