-
Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Ukwati wa Amuna Kapena Akazi Okhaokha?Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
-
-
Mlengi wathu anapereka malamulo okhudza ukwati kale kwambiri, maboma a anthu asanayambe n’komwe kuika malamulo okhudza ukwati. Buku loyambirira m’Baibulo limatiuza kuti: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Malinga ndi buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo, mawu achiheberi amene anawamasulira kuti “mkazi” palembali, “amatanthauza munthu yemwe si mwamuna.” (Vine’s Expository Dictionary of Biblical Words) Yesu nayenso ananena kuti anthu okwatirana ayenera kukhala “mwamuna ndi mkazi.”—Mateyu 19:4.
Choncho, cholinga cha Mulungu chinali chakuti anthu okwatiranawo azikhala mwamuna ndi mkazi ndipo banja lisamathe. Amuna ndi akazi analengedwa moyenererana kuti azitha kukwatirana n’kumathandizana m’njira zosiyanasiyana, ndiponso kumasangalala ndi kugonana komanso kumabereka ana.
-
-
Kodi Baibulo Limaletsa Kugonana?Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
-
-
Baibulo sililetsa kugonana koma limasonyeza kuti kugonanako ndi mphatso yochokera kwa Mulungu imene anthu okwatirana ayenera kusangalala nayo. Mulungu analenga “mwamuna ndi mkazi” ndipo anaona kuti zonse zimene analenga zinali “zabwino kwambiri.” (Genesis 1:27, 31) Pa nthawi imene Mulungu ankapereka Hava kwa Adamu kuti akhale mkazi wake, ananena kuti “iwo adzakhala thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Umenewu unali ukwati woyambirira ndipo Adamu ndi mkazi wake anafunika kumakondana kwambiri komanso kumasangalala ndi mphatso ya kugonana.
-
-
Kodi Munthu Angasonyeze Bwanji Kuti ‘Amalemekeza Bambo Ake ndi Mayi Ake’?Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
-
-
Zoona zake: Baibulo limaphunzitsa kuti mgwirizano wa mwamuna ndi mkazi okwatirana ndi wofunika kwambiri kuposa mgwirizano wawo ndi abale awo. Lemba la Genesis 2:24 limati: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake.” (Mateyu 19:4, 5) N’zoona kuti mwamuna ndi mkazi wake akhoza kupindula ndi malangizo ochokera kwa makolo awo kapena apongozi awo. (Miyambo 23:22) Komabe, mwamuna ndi mkazi sangalakwitse ngati atasankha kuti achibale awo asamalowerere kwambiri nkhani za m’banja mwawo.—Mateyu 19:6.
-