Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gm mutu 11 tsamba 149-161
  • Kugwirizana kwa Baibulo Lonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugwirizana kwa Baibulo Lonse
  • Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndani Amene Ali Chinjoka?
  • Mbewu ya Chinjoka
  • Kodi Ndani Amene Ali Mbewu ya Mkazi?
  • Chovutacho Chathetsedwa
  • Nangano, Ndani Amene, Ali Mkaziyo?
  • Tanthuzo Lake kwa Ife
  • Mbewu ya Njoka—Yavumbulidwa Motani?
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Mfundo Yaikulu ya M’Baibulo
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Iye Amene Aneneri Onse Anamuchitira Umboni
    Lambirani Mulungu Woona Yekha
  • Kuvundukula Chinjokacho
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
gm mutu 11 tsamba 149-161

Mutu 11

Kugwirizana kwa Baibulo Lonse

Tayekezerani nkhokwe ya mabukhu 66 olembedwa ndi pafupifupi anthu osiyanasiyana 40 mkati mwa nyengo yanthaŵi ya zaka 1 600. Zinenero zitatu zinagwiritsiridwa ntchito ndi olemba amene anakhala ndi moyo m’maiko angapo. Olemba onse anali ndi maumunthu osiyana, maluso, ndi ziyambi. Koma pamene mabukhu amene anawalembera potsirizira pake anasonkhanitsidwa pamodzi, zinachitika kuti, kwenikweni, iwo anapanga bukhu limodzi lokha lalikulu lomatsatira mutu umodzi waukulu kuyambira pachiyambi kufikira kumapeto. Zimenezo nzovuta kuziyerekezera, kodi sichoncho? Komabe, Baibulo ndilo nkhokwe ya mabukhu yoteroyo.

1. (Phatikizamoni mawu oyamba.) Kodi ndikugwirizana kwapadera kotani kumene kumatsimikizira chenicheni chakuti Baibulo liridi louziridwa ndi Mulungu?

PALIBE wophunzira wowona mtima amene angalephere kugwidwa mtima ndi chenicheni chakuti Baibulo, ngakhale kuli kwakuti ndiro kusonkhanitsidwa pamodzi kwa mabukhu osiyanasiyana, liri chinthu chimodzi chogwirizanitsidwa. Iro liri logwirizanitsidwa m’chakuti, kuyambira pachiyambi kukafikira kumapeto, limapititsa patsogolo kulambiridwa kwa Mulungu mmodzi yekha amene mikhalidwe yake siimasintha konse, ndipo mabukhu ake onse amafotokoza mutu umodzi waukulu. Kugwirizana kwa lonse lathunthu kumeneku ndiko umboni wamphamvu wakuti Baibulo liri, ndithudi, Mawu a Mulungu.

2, 3. Kodi ndiulosi wotani wonenedwa mu Edene umene unapereka maziko a chiyembekezo, ndipo kodi ndimikhalidwe yotani imene inatsogolera kukunenedwa kwa ulosiwo?

2 Mutu waukulu wa Baibulo ukusonyezedwa m’mitu yoyambirira ya bukhu lake loyambirira lenilenilo, Genesis. Mmenemo, timaŵerenga kuti makolo athu oyambirira, Adamu ndi Hava, analengedwa ali angwiro naikidwa m’munda wa paradaiso, Edene. Komabe, Hava, anafikiridwa ndi njoka, imene inatsutsa kuyenerera kwa malamulo a Mulungu nimnyenga ndi mabodza a machenjera kuloŵa m’njira yauchimo. Adamu anamtsatira ndipo nayenso sanamvere Mulungu. Nchotulukapo chotani? Onse aŵiri anathamangitsidwa m’Edene ndipo anatsutsidwira kuimfa. Ife lerolino tikuvutika ndi zotulukapo za chipanduko choyambirira chimenecho. Ife tonse timalandira uchimo ndi imfa kuchokera kwa makolo athu oyambirira.—Genesis 3:1-7, 19, 24; Aroma 5:12.

3 Komabe, panthaŵi yovuta imeneyo, Mulungu anapereka ulosi umene unapereka maziko a chiyembekezo. Ulosiwo unanenedwa kwa chinjoka, koma unaperekedwa Adamu ndi Hava akumva kotero kuti iwo akanatha kuusimbira kwa ana awo. Nazi zimene Mulungu ananena: “Ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake. Iye adzakuzunzunda iwe mutu ndi iwe udzamzunzunda chitende.”—Genesis 3:15, NW; Aroma 8:20, 21.

4. Kodi ndianthu ati amene anatchulidwa muulosi wa Yehova mu Edene, ndipo kodi ndimotani mmene iwo akachitira mkati mwa zaka mazana ochuluka?

4 Wonani zinthu zinayi zimene zikutchulidwa m’vesi la mutu wa nkhani limeneli: chinjoka ndi mbewu yake kudzanso mkazi ndi mbewu yake. Zinthu zimenezi zikakhala zochitika zofunika m’zochitika kwa zaka zikwi zochuluka zirinkudza. Udani wosalekeza unayenera kukhalapo pakati pa mkazi ndi mbewu yake kumbali imodzi ndi chinjoka ndi mbewu yake kumbali ina. Udani umenewu ukaphatikizapo kulimbana kosalekeza pakati pa kulambira kowona ndi konyenga, khalidwe loyenera ndi kuipa. Panthaŵi ina, chinjoka chikapeza chowonekera kukhala phindu pamene chikazunzunda chitende cha mbewu ya mkazi. Komabe, potsirizira pake, mbewu yamkazi ikaphwanya mutu wa chinjoka, ndipo Mulungu iye mwini akatamandidwa pamene zodziŵikitsa zonse za chipanduko choyambirira chimenecho zikachotsedwa.

5. Kodi tikudziŵa motani kuti Hava sanali mkazi wa muulosi umenewo?

5 Kodi ndani amene ali mkaziyo ndi chinjoka? Ndipo kodi ndani amene ali mbewu zawo? Pamene Hava anabala mwana wake wamwamuna wachisamba, Kaini, iye ananena kuti: “Ndabala munthu mwa chithandizo cha Yehova.” (Genesis 4:1, NW) Mwinamwake iye analingalira kuti iye anali mkazi wa muulosi uja ndi kuti mwana wawo wamwamuna ameneyu akatsimikizira kukhala mbewu. Komabe, Kaini, anali ndi mzimu woipa wofanana ndi wa chinjoka. Iye anasanduka wambanda, akumapha m’ngono wake wa iye mwini Abele. (Genesis 4:8) Mwachiwonekere, ulosiwo unali ndi tanthauzo lozama, lophiphiritsira limene Mulungu yekha akanatha kulifotokoza. Ndipo zimenezi iye anazichita, mwapang’ono panthaŵi imodzi. Mabukhu onse 66 a Baibulo amathandizira mwanjira zosiyanasiyana kuvumbulutsidwa kwa tanthauzo la umenewu, ulosi woyambirira m’Baibulo.

Kodi Ndani Amene Ali Chinjoka?

6-8. Kodi ndimawu otani a Yesu amene amatithandiza kudziŵa mphamvu kutseri kwa chinjoka? Fotokozani.

6 Choyamba, kodi ndani amene ali chinjoka chotchulidwa m’Genesis 3:15? Cholembedwacho chikunena kuti njoka yeniyeni inafikira Hava mu Edene, koma njoka zenizeni sizingathe kulankhula. Payenera kukhala panali mphamvu ina kutseri kwa njokayo yomaichititsa kuchita monga mmene inachitiramo. Kodi mphamvu imeneyo inali chiyani? Mphamvuyo siinadziŵike bwino lomwe kufikira m’zaka za zana loyamba la Nyengo ya Onse, pamene Yesu anali kuchita utumiki wake padziko lapansi pano.

7 Pachochitika china, Yesu anali kulankhula ndi atsogoleri achipembedzo Achiyuda odzilunganitsa amene monyada ananena kuti iwo anali ana a Abrahamu. Komabe, iwo anatsutsa kwantu wagalu chowonadi cholalikidwa ndi Yesu. Chotero Yesu anati kwa iwo: “Inu muli ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo mufuna kuchita zolakalaka za atate wanu. Ameneyo anali wakupha munthu pamene iye anayamba, ndipo sanaima mwamphamvu m’chowonadi, chifukwa chakuti chowonadi sichiri mwa iye. Pamene iye alankhula bodza, iye amalankhula mogwirizana ndi chifuniro chake cha iye mwini, chifukwa chakuti iye ali wabodza ndi atate wabodza.”—Yohane 8:44, NW.

8 Mawu a Yesu anali amphamvu koma olunjikadi. Iye anafotokoza Mdyerekezi monga “wakupha munthu” ndi “atate wabodza.” Tsopano, mabodza oyambirira kulembedwa anali awo onenedwa ndi njoka mu Edene. Aliyense amene ananena mabodza amenewo analidi “atate wabodza.” Ndiponso, mabodza amenewo anachititsa imfa ya Adamu ndi Hava, akumapangitsa kuti wabodza wamakedzanayo akhale wambanda. Chotero mwachiwonekere, mphamvu imene inali kutseri kwa chinjoka mu Edene inali Satana Mdyerekezi, ndipo Yehova analidi kulankhula kwenikweni ndi Satana mu ulosi wamakedzana umenewo.

9. Kodi Satana anakhalako motani?

9 Ena afunsa kuti: Ngati Mulungu ali wabwino, kodi nchifukwa ninji iye analenga cholengedwa choterocho chonga Mdyerekezi? Mawu a Yesu amatithandiza kuyankha funso limenelo. Ponena za Satana Yesu anati: “[Iye] anali wakupha munthu kuyambira pachiyambi.” Chotero pamene Satana ananamiza Hava, ndipo pamene iye anayamba kukhala Satana—kuchokera ku liwu Lachihebri limene limatanthauza “wotsutsa.” Mulungu sanalenge Satana. Mngelo wokhulupirika papitapoyo analola chikhumbo cholakwa kukula mumtima mwake kotero kuti anakhala Satana.—Deuteronomo 32:4; yerekezerani ndi Yobu 1:6-12; 2:1-10; Yakobo 1:13-15.

Mbewu ya Chinjoka

10, 11. Kodi ndimotani mmene Yesu ndi mtumwi Yohane akutithandizira kudziŵa mbewu ya Chinjoka?

10 Komabe, bwanji ponena za ‘mbewu [kapena mbadwa] ya chinjoka’? Mawu a Yesu amatithandizanso kuthetsa mbali imeneyi ya vutolo. Iye kwa atsogoleri achipembedzo Achiyuda anati: “Inu muli ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo inu mufuna kuchita zikhumbo za atate wanu.” Ayuda ameneŵa anali mbadwa za Abrahamu, monga momwedi monyada ananenera. Koma khalidwe lawo loipa linawapanga iwo kukhala ana auzimu a Satana, woyambitsa uchimo.

11 Mtumwi Yohane, akulemba chakumapeto kwa zaka za zana loyamba, akufotokoza momvekera bwino amene anali a mbewu ya Chinjoka, Satana. Iye akulemba kuti: “Iye wochita tchimo ali wochokera mwa Mdyerekezi, chifukwa Mdyerekezi amachimwa kuyambira pachiyambi. . . . Mmenemo awoneka ana a Mulungu, ndi ana a Mdyerekezi: yense wosachita chilungamo siali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake.” (1 Yohane 3:8, 10) Mwachiwonekere, a mbewu ya Chinjoka akhala okangalika kwambiri m’mbiri yonse ya anthu!

Kodi Ndani Amene Ali Mbewu ya Mkazi?

12, 13. (a) Kodi ndimotani mmene Yehova anavumbulira kwa Abrahamu kuti mbewu ya mkazi ikawonekera pakati pa mbadwa zake? (b) Kodi ndani amene analandira mwacholoŵa lonjezo lonena za Mbewu?

12 Pamenepa, kodi ndani amene ali ‘mbewu [kapena mbadwa] ya mkazi’? Limeneli liri limodzi la mafunso ofunika kopambana amene anafunsidwapo, pakuti ndiyo mbewu ya mkaziyo imene potsirizira pake idzaphwanya mutu wa Satana ndi kuthetsa ziyambukiro zoipa za chipanduko choyambiriracho. Kalero m’zaka za zana la 20 B.C.E., Mulungu anavumbula chisonyezero chachikulu chodziŵira ponena za kudziŵika kwa ameneyu kwa munthu wokhulupirika Abrahamu. Chifukwa cha chikhulupiriro chachikulu cha Abrahamu, Mulungu anapanga mpambo wa malonjezo kwa iye wonena za mbadwa imene ikabadwa kwa iye. Limodzi la ameneŵa linakupangitsa kukhala kowonekera bwino kuti ‘mbewu ya mkazi’ imene ‘ikaphwanya mutu wachinjoka’ ikawonekera pakati pa ana a Abrahamu. Mulungu anamuuza kuti: “Mbewu zako zidzagonjetsa chipata cha adani awo. M’mbewu zako mitundu yonse yadziko idzadalitsidwa chifukwa wamvera mawu anga.”—Genesis 22:17, 18.

13 Pamene zaka zinali kupita, lonjezo la Yehova kwa Abrahamu linabwerezedwa kwa mwana wamwamuna wa Abrahamu Isake ndi kwa mdzukulu wake Yakobo. (Genesis 26:3-5; 28:10-15) Potsirizira pake, mbadwa za Yakobo zinakhala mafuko 12, ndipo limodzi la mafuko amenewo, Yuda, linalandira lonjezo lapadera: “Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.” (Genesis 49:10) Mwachiwonekere, Mbewu inayenera kuwoneka m’fuko la Yuda.

14. Kodi ndimtundu wotani umene unalinganizidwa kuti ukonzekere kaamba ka kudza kwa Mbewu?

14 Pamapeto a zaka za zana la 16 B.C.E., mafuko 12 a Israyeli analinganizidwa kukhala mtundu monga anthu apadera a Mulungu. Ndi cholinga chimenechi, Mulungu anapanga pangano la lumbiro ndi iwo nawapatsa mpambo wa malamulo. Chifukwa chachikulu chochitira zimenezi chinali kukonzekeretsa mtundu kaamba ka kudza kwa Mbewu. (Eksodo 19:5, 6; Agalatiya 3:24) Kuyambira panthaŵi imeneyo kumkabe mtsogolo, udani wa Satana kwa Mbewu ya mkazi unawonekera mu udani wamitundu ku anthu osankhidwa a Mulungu.

15. Kodi nchisonyezero chotsirizira chotani chimene chinaperekedwa ponena za kuti ndi banja liti pakati pa mbadwa za Abrahamu limene likatulutsa Mbewu?

15 Chisonyezero chotsirizira chonena za kuti ndibanja liti limene likatulutsa Mbewu chinaperekedwa m’zaka za zana la 11 B.C.E. Panthaŵi imeneyo, Mulungu analankhula ndi mfumu yachiŵiri ya Israyeli, Davide, namlonjeza kuti Mbewu ikachokerapo pakati pa mbadwa zake ndi kuti mpando wachifumu wa ameneyu “ukakhazikitsidwa mwamphamvu kunthaŵi yonse.” (2 Samueli 7:11-16, NW) Kuyambira pamenepopo kumkabe mtsogolo, Mbewuyo moyenerera imasonyezedwa kukhala mwana wa Davide.—Mateyu 22:42-45.

16, 17. Kodi ndimotani mmene Yesaya anafotokozera madalitso amene Mbewu ikadzetsa?

16 M’zaka zotsatirapo, Mulungu anadzutsa aneneri kupereka chidziŵitso chouziridwa chowonjezereka chonena za Mbewu irinkudza. Mwachitsanzo, m’zaka za zana lachisanu ndi chitatu B.C.E., Yesaya analemba kuti: “Kwa ife kwabadwa mwana, mwana wamwamuna waperekedwa kwa ife; ndipo ulamuliro waukalonga udzakhala pamapeŵa pake. Ndipo dzina lake lidzatchedwa Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa Mtendere. Kuchuluka kwa ulamuliro wake waukalonga ndi mtendere sikudzatha, pampando wachifumu wa Davide ndi paufumu wake.”—Yesaya 9:6, 7, NW.

17 Yesaya kenako analosera ponena za Mbewu imeneyi kuti: “Ndi chilungamo iye ayenera kulamula ofatsa, ndipo ndi chilungamo iye ayenera kupereka chidzudzulo mmalo mwa ofatsa a dziko lapansi. . . . Ndipo mbulu udzakhala pamodzi kwakanthaŵi ndi nkhosa yamphongo, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi, ndipo mwana wang’ombe ndi mwana wa mkango ndi choŵeta chonenepa pamodzi . . . Sizidzachititsa chivulazo chirichonse kapena kuchititsa kuipitsa kulikonse m’phiri langa lopatulika; chifukwa chakuti dziko lapansi lizadzadzadi ndi kudziŵa Yehova monga momwe madzi amadzadzira nyanja.” (Yesaya 11:4-9, NW) Ha ndimadalitso aakulu chotani nanga amene mbewu imeneyi inali kuzadzetsa!

18. Kodi ndichidziŵitso chowonjezereka chotani chonena za Mbewu chimene Danieli analemba?

18 M’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi Nyengo Yathu Yofala ino isanakhale, Danieli analemba umboni wina wowonjezereka ponena za Mbewu. Iye ananeneratu za nthaŵi pamene wina wonga mwana wamunthu akawonekera kumwamba, nanena kuti “ndipo kwa iye kunapatsidwa ulamuliro ndi ulemu ndi ufumu, kuti mitundu ya anthu, timagulu ta anthu ndi a zinenero ayenera onse kumtumikira iye.” (Danieli 7:13, 14, NW) Chotero Mbewu inalinkudzayo ikalandira choloŵa cha ufumu wakumwamba, ndipo ulamuliro wake wachifumu ukafutukukira padziko lonse lapansi.

Chovutacho Chathetsedwa

19. Kodi ndimbali yotani, monga momwe yavumbulutsidwira ndi mngelo, imene Mariya anayenera kuchita m’Mbewu imene inali nkudza?

19 Kudziŵika kwa Mbewu potsirizira pake kunavumbulidwa pa kuyambika kwa Nyengo Yathu Yofala ino. M’chaka cha 2 B.C.E., mngelo anawonekera kwa namwali Wachiyuda wotchedwa Mariya, amene anali mbadwa ya Davide. Mngeloyo anamuuza kuti akabala mwana wapadera kwambiri ndipo anati: “Ameneyo adzakhala wamkulu kwambiri ndipo adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwambayo; ndipo Yehova Mulungu adzampatsa iye mpando wachifumu wa Davide atate wake, ndipo adzalamulira monga mfumu panyumba yonse ya Yakobo kosatha, ndipo ufumu wake suudzatha.” (Luka 1:32, 33, NW) Chotero kuyembekezeredwa kwanthaŵi yaitali kwa “mbewu” potsirizira pake kunalinkufika kumapeto.

20. Kodi ndani amene ali Mbewu yolonjezedwayo, ndipo kodi ndiuthenga wotani umene iye analalikira mu Israyeli?

20 M’chaka cha 29 C.E. (chaka chonenedweratu kalekale pasadakhale ndi Danieli), Yesu anabatizidwa. Pamenepo mzimu woyera unatsikira pa iye, ndipo Mulungu anamvomereza iye kukhala Mwana wake. (Danieli 9:24-27; Mateyu 3:16, 17) Kwazaka zitatu ndi theka pambuyo pake, Yesu anachitira umboni kwa Ayuda, akumalengeza kuti: “Ufumu wakumwamba wasendera pafupi.” (Mateyu 4:17, NW) Mkati mwa nthaŵi imeneyo, iye anakwaniritsa maulosi ochuluka kwambiri ochokera m’Malemba Achihebri kwakuti panalibenso mpata wa chikaikiro ponena zakuti iye analidi Mbewu yolonjezedwayo.

21. Kodi nchiyani chimene Akristu oyambirira anamvetsa ponena za kudziŵika kwa Mbewu?

21 Akristu oyambirira anamvetsetsa zimenezi bwino lomwe. Paulo anafotokoza kwa Akristu m’Galatiya kuti: “Tsopano malonjezowo anaperekedwa kwa Abrahamu ndi kumbewu yake. Likunena, osati: ‘Ndi kwa mbewu zake,’ monga ngati akunena zambiri, koma ndi kunena imodzi: ‘Ndi kwa mbewu yako,’ imene iri Kristu.” (Agalatiya 3:16, NW) Chotero Yesu anali kudzakhala “Kalonga wa Mtendere” padziko lonse lapansi wonenedweratu ndi Yesaya. Pamene iye potsirizira pake akaloŵa Muufumu wake, chiweruzo cholungama ndi chilungamo zikakhazikitsidwa padziko lonse.

Nangano, Ndani Amene, Ali Mkaziyo?

22. Kodi ndani amene ali mkazi wotchulidwa muulosi wa Yehova mu Edene?

22 Ngati Yesu ali Mbewu, ndani amene ali mkazi amene anatchulidwa kalero mu Edene? Popeza kuti mphamvu imene inali kutseri kwa chinjoka inali cholengedwa cha mzimu, sitiyenera kudabwa kuti mkaziyo nayenso ayenera kukhala mzimu ndipo osati munthu. Mtumwi Paulo analankhula za “mkazi” wakumwamba pamene iye anati: “Koma Yerusalemu wakumwamba ali waufulu, ndipo iye ndiye amayi ŵathu.” (Agalatiya 4:26, NW) Malemba ena amasonyeza kuti “Yerusalemu wakumwamba” ameneyu wakhalapo kale kwa zaka zikwi zochuluka. Iye ndiye gulu lakumwamba la Yehova la zolengedwa zauzimu, kuchokera m’limene Yesu anatsika kudzakwaniritsa ntchito ya ‘mbewu ya mkazi.’ Kokha mtundu wa “mkazi” ameneyu ukanatha kupirira udani wa “chinjoka chakalecho” kwa zaka zikwizikwi.—Chivumbulutso 12:9; Yesaya 54:1, 13; 62:2-6.

23. Kodi nchifukwa ninji kuvumbulutsidwa kopita patsogolo kwa tanthauzo la ulosi wa Yehova wa pa Edene kuli kwapadera kwambiri?

23 Kupenda kwachidule kwa chochitika cha ulosi wamakedzana umenewo mu Genesis 3:15 kuli umboni wamphamvu wa kugwirizana kwakukulu kwa Baibulo. Kuli kwapadera kwenikweni kuti ulosi ungathe kumvedwa kokha pamene tisonkhanitsa pamodzi zochitika ndi zonenedwa zochokera m’zaka za zana la 20, la 11, la 8, ndi la 6 B.C.E. limodzi ndi zonena ndi zochitika zochokera m’zaka za zana loyamba la Nyengo Yathu ya Onse ino. Zimenezi sizingakhale zitangochitika mwamwaŵi. Payenera kukhala panali dzanja lotsogoza kutseri kwa zonsezi.—Yesaya 46:9, 10.

Tanthuzo Lake kwa Ife

24. Kodi kudziŵika kwa Mbewu kumatanthauzanji kwa ife?

24 Kodi zonsezi zikutanthauzanji kwa ife? Eya, Yesu ali wamkulu wa ‘mbewu ya mkaziyo.’ Ulosi wamakedzana umenewo mu Genesis 3:15 udaneneratu kuti chitende chake ‘chikazunzundidwa’ ndi Chinjoka, ndipo zimenezi zinachitika pamene Yesu anafa pamtengo wozunzirapo. Kuzunzundidwa sikumakhala kosatha. Chotero, chowonekera ngati chipambano cha Chinjoka mwamsanga chinachititsidwa kukhala kugonja pamene Yesu anaukitsidwa. (Monga momwe tinawonera m’Mutu 6, pali umboni wamphamvu wakuti zimenezi zinachitikadi.) Imfa ya Yesu inakhala maziko kaamba ka chipulumutso cha mtundu wa anthu owongoka mtima, chotero Mbewu inayamba kukhala dalitso, monga momwe Mulungu anali atalonjezera Abrahamu. Koma bwanji ponena za maulosi akuti Yesu akayenera kulamulira kuchokera Muufumu wakumwamba pachigawo chake chonse cholamulidwa cha padziko lapansi?

25, 26. Kodi ndi nkhani yotani imene inali yophatikizidwa ponena za udani umene uli pakati pa mbewu ya mkazi ndi Chinjoka, umene walongosoledwa m’Chivumbulutso?

25 M’masomphenya olongosola molosera m’Chivumbulutso mutu 12, chiyambi cha Ufumu umenewo chikuphiphiritsiridwa ndi kubadwa kwa mwana wamwamuna kumwamba. Mu Ufumu umenewu, Mbewu yolonjezedwayo ikutenga ulamuliro pansi pa dzina la ulemu lakuti Mikaeli, kutanthauza “Ndani Afanana ndi Mulungu?” Iye akusonyeza kuti palibe aliyense amene moyenera angathe kutsutsa ulamuliro wa Yehova, pamene iye athamangitsa “chinjoka choyambiriracho” kumwamba kwanthaŵi yonse. Timaŵerenga kuti: “Chotero chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulucho, chinjoka chakalecho, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, amene akusokeretsa dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu; anaponyeredwa pansi kudziko lapansi.”—Chivumbulutso 12:7-9, NW.

26 Chotulukapo ndicho mpumulo kaamba ka miyamba koma nsautso padziko lapansi. “Tsopano zafika chipulumutso ndi mphamvu ndi ufumu za Mulungu wathu ndi ulamuliro wa Kristu wake,” inadza motero mfuu yachipambano. Ndiponso timaŵerenga kuti: “Chifukwa chake kondwerani, miyamba inu ndi inu amene mumakhalamo! Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo mkwiyo waukulu, podziŵa kuti ali ndi nyengo ya nthaŵi yaifupi.”—Chivumbulutso 12:10, 12, NW.

27. Kodi ndiliti pamene ulosi wonena za kuthamangitsidwa kwa Satana kuchokera kumwamba unakwaniritsidwa? Kodi tidziŵa bwanji?

27 Kodi tingathe kunena kuti ndiliti pamene ulosi umenewu ukakwaniritsidwa? Kwenikweni, limeneli linali funso limene linadzutsidwa ndi ophunzira pamene iwo anafunsa Yesu ponena za ‘chizindikiro cha kukhalapo kwake ndi cha mathedwe a dongosolo la zinthu’—monga momwe tafotokozera m’Mutu 10. (Mateyu 24:3) Monga momwe tinawonera, umboni ulipo wochuluka wakuti kukhalapo kwa Yesu m’mphamvu ya Ufumu wakumwamba kunayamba mu 1914. Kuyambira panthaŵi imeneyo, tawonadi “tsoka padziko lapansi”!

28, 29. Kodi ndimasinthidwe aakulu otani pa zochitika za padziko lapansi amene akali mtsogolo, ndipo kodi tikudziŵa motani kuti iwo adzachitika msanga?

28 Koma tawonani: Kuti mfuu yakumwamba imeneyo inalengeza kuti Satana ali ndi “nyengo yanthaŵi yaifupi” chabe. Chotero ulosi woyambirira umenewo m’Genesis 3:15 ukuyenda kumka kuchimake chosalakwika. Chinjoka, mbewu yake, mkazi, ndi mbewu yake zonsezo zadziŵikitsidwa. Mbewuyo ‘inazunzundidwa chitende,’ koma inachira. Posachedwapa, kuphwanyidwa kwa Satana (ndi mbewu yake) kudzayamba pansi pa Mfumu ya Mulungu imene iri tsopano linoyo pampando wachifumu, Kristu Yesu.

29 Kumeneku kudzaloŵetsamo masinthidwe aakulu pa zochitika za padziko lapansi. Limodzi ndi Satana, awo amene adzitsimikizira iwo eni kukhala mbewu yake adzachotsedwa. Monga momwe wamasalmo analoserera: “Katsala kanthaŵi, ndipo oipa sadzakhalakonso; ndipo iwe ndithudi udzayang’ana pamalo ake, ndipo iye adzakhala palibe.” (Salmo 37:10, NW) Ha ndikusintha kwakukulu chotani nanga mmene kumeneko kudzakhalira! Pamenepo, mawu owonjezerapo a wamasalmo adzakwaniritsidwa akuti: “Koma ofatsa iwo eniwo adzalandira dziko lapansi, ndipo ndithudi adzapeza chikondwerero chawo chochuluka m’kuchuluka kwa mtendere.”—Salmo 37:11, NW.

30. Kodi nchifukwa ninji okaikira amene amaika chikaikiro pa kuuziridwa kwa Baibulo ndipo ngakhale pakukhalapo kwa Mulungu iwo eniwo ali okaikitsa?

30 Mwanjira imeneyi, “Kalonga wa Mtendere” potsirizira pake azadzetsa mtendere kwa mtundu wa anthu. Iritu ndilo lonjezo la Baibulo monga momwe tinawonera pa Yesaya 9:6, 7. M’nyengo ino yokaikira, ambiri amapeza lonjezo loterolo kukhala lokaikiritsa. Koma kodi ndichinthu china chotani chimene munthu amapereka? Palibe! Kumbali ina, lonjezo limeneli lalongosoledwa momvekera bwino m’Baibulo, ndipo Baibulo ndilo Mawu osalephera a Mulungu. Kwenikweni ndiwo okaikirawo amene ali okaikiritsa. (Yesaya 55:8, 11) Iwo amanyalanyaza Mulungu, amene anauzira Baibulo ndi amene ali weniweni wamkulu koposa onse.

[Chithunzi patsamba 151]

Ulosi woyambirira wa Baibulo unapatsa anthu akugwawo maziko achiyembekezo

[Chithunzi patsamba 154]

M’zaka za zana la 20 B.C.E., Yehova anauza Abrahamu kuti Mbewu yolonjezedwayo ikachokera pakati pa mbadwa zake

[Chithunzi patsamba 155]

M’zaka za zana la 11 B.C.E., Mfumu Davide anamva kuti Mbewuyo ikadzera mu mzera wake wachifumu

[Chithunzi patsamba 156]

M’zaka za zana la chisanu ndi chitatu B.C.E., Yesaya ananeneratu za madalitso amene Mbewuyo ikadzetsa

[Chithunzi patsamba 157]

M’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E., Danieli ananeneratu kuti Mbewu ikalamulira mu ufumu wakumwamba

[Chithunzi patsamba 159]

Chapafupi ndi chiyambi cha zaka za zana loyamba C.E., Mariya anauzidwa kuti Yesu, khanda limene iye akabala, likakula kukhala Mbewu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena