Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Ngakhale Kuti Anafa, Iye Akulankhulabe”
    Nsanja ya Olonda—2013 | January 1
    • Ngati iye ankaganizadi zimenezi ndiye kuti ankalakwitsa. Komanso ngati iye ndi mwamuna wake ankauza Kaini zimenezi, ndiye kuti anachititsa Kainiyo kukhala ndi maganizo olakwika. Kenako Hava anaberekanso mwana wina ndipo pa nthawiyi sananene mawu osonyeza kuti ananyadira. Mwana wachiwiriyu, anamutchula kuti Abele, dzina lomwe mwina limatanthauza “Mpweya wotuluka m’mphuno” kapena “Zachabechabe.” (Genesis 4:2) N’kutheka kuti anamutchula dzina limeneli posonyeza kuti ankadalira kwambiri Kaini kusiyana ndi Abeleyo.

  • “Ngakhale Kuti Anafa, Iye Akulankhulabe”
    Nsanja ya Olonda—2013 | January 1
    • N’zodziwikiratu kuti pamene anyamatawa ankakula, Adamu ankawaphunzitsa ntchito. Kaini anali mlimi ndipo Abele anali m’busa.

  • “Ngakhale Kuti Anafa, Iye Akulankhulabe”
    Nsanja ya Olonda—2013 | January 1
    • Abele ankaganizira kwambiri za Yehova. Yerekezani kuti mukumuona ali kuubusa akuweta nkhosa zake. Abusa ankayenda kwambiri ndipo nthawi zambiri ankayenda ndi nkhosa zawo m’malo amapiri, m’zigwa komanso m’mbali mwa mitsinje kufunafuna msipu wobiriwira, akasupe a madzi komanso malo abwino oti nkhosazo zipume. Pa zolengedwa zonse, nkhosa zinkaoneka kuti sizingayende zokha koma zinkafunika munthu woti azizitsogolera komanso kuziteteza. Abele ankaona kuti nayenso ankafunika kuti Mulungu, yemwe ndi wamphamvu kuposa anthu, azimutsogolera, kumuteteza komanso kumusamalira. N’zosakayikitsa kuti iye ankanena zimenezi akamapemphera ndipo izi zinathandiza kuti chikhulupiriro chake chipitirize kulimba.

      Chilengedwe chinathandiza Abele kukhulupirira kwambiri Mlengi

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena