“Momwemo Anachita”
“Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake.”—1 YOHANE 5:3.
1. Kodi chinganenedwe nchiyani ponena za ukulu wa chikondi cha Mulungu?
“MULUNGU NDIYE CHIKONDI.” Onse amene amayamba kumdziŵa Mulungu ndi kumvera malamulo ake amamvetsetsa kuya kwake kwa chikondicho. “Umo muli chikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiwombolo chifukwa cha machimo athu.” Pamene tisonyeza chikhulupiriro m’nsembe ya dipo ya Yesu yamtengo wapatali, ‘timakhala m’chikondi cha Mulungu.’ (1 Yohane 4:8-10, 16) Motero tingapeze madalitso ochuluka auzimu tsopano ndipo m’dongosolo latsopano la zinthu likudzalo, moyo wosatha.—Yohane 17:3; 1 Yohane 2:15, 17.
2. Kodi kusunga malamulo a Mulungu kwawapindulitsa motani atumiki ake?
2 Mbiri ya Baibulo yadzala ndi zitsanzo za anthu amene anasunga malamulo a Mulungu ndipo anadalitsidwa kwambiri chifukwa cha zimenezo. Iwo akuphatikizapo mboni zokhalako Chikristu chisanakhale, amene mtumwi Paulo analemba ponena za ena a iwo motere: “Iwo onse adamwalira m’chikhulupiriro, osalandira malonjezano, komatu adaona ndi kuwalankhula kutali, navomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko.” (Ahebri 11:13) Pambuyo pake, atumiki Achikristu odzipereka a Mulungu anapindula ndi “chisomo ndi choonadi [zimene] zinadza mwa Yesu Kristu.” (Yohane 1:17) M’zaka zonse pafupifupi 6,000 za mbiri ya munthu, Yehova wapereka mphotho kwa mboni zake zokhulupirika zimene zamvera malamulo ake, amene “saali olemetsa” ayi.—1 Yohane 5:2, 3.
Mu Masiku a Nowa
3. Kodi Nowa anachita “momwemo” m’njira zotani?
3 Mbiri ya Baibulo imati: “Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndipo pochita mantha, anamanga chingalaŵa cha kupulumutsiramo iwo a m’nyumba yake; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala woloŵa nyumba wa chilungamo chili monga mwa chikhulupiriro.” Pokhala “mlaliki wa chilungamo,” Nowa anamvera Mulungu kotheratu, nachenjeza dziko lachiwawa lokhalako Chigumula chisanadze za chiweruzo cha Mulungu chomwe chinali pafupi. (Ahebri 11:7; 2 Petro 2:5) Pomanga chingalaŵa, anatsatira mosamala mapulani amene Mulungu anampatsa. Ndiyeno analoŵetsamo zinyama zimene anauzidwa ndi zakudya. “Anachita Nowa, monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita.”—Genesis 6:22.
4, 5. (a) Kodi chisonkhezero choipa chawakhudza motani anthu kufikira lerolino? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuchita “momwemo” pomvera malangizo a Mulungu?
4 Nowa ndi banja lake analimbana ndi chisonkhezero choipa cha angelo opanduka. Ana a Mulungu ameneŵa anavala matupi a anthu nakhala pamodzi ndi akazi, nabala ana achilendo, zimphona zimene zinavutitsa anthu. “Dziko lapansi linavunda pamaso pa Mulungu, dziko lapansi ndipo linadzala ndi chiwawa.” Yehova anatumiza Chigumula kudzaseseratu mbadwo woipa umenewo. (Genesis 6:4, 11-17; 7:1) Chiyambire tsiku la Nowa angelo auchiŵanda sanaloledwe kuvala matupi a anthu. Komatu, ‘dziko lonse lapansi lipitiriza kugona mwa woipayo,’ Satana Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19; Chivumbulutso 12:9) Mu ulosi wake, Yesu anayerekezera mbadwo wopandukawo wa m’tsiku la Nowa ndi mbadwo wa anthu umene wamkana iye chiyambire pamene chizindikiro cha “kukhalapo” kwake chinayamba kuonekera mu 1914.—Mateyu 24:3, 34, 37-39; Luka 17:26, 27.
5 Lerolino, monga m’tsiku la Nowa, Satana akuyesa kuwononga anthu ndi pulaneti lathuli. (Chivumbulutso 11:15-18) Chifukwa chake tiyenera kufulumira kulabadira lamulo louziridwali lakuti: “Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchirimika pokana machenjerero a Mdyerekezi.” (Aefeso 6:11) Pankhaniyi, timalimbitsidwa mwa kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kuwatsatira m’moyo wathu. Ndiponso, tili ndi gulu la Yehova lotisamalira, limodzi ndi “kapolo [wake] wokhulupirika ndi wanzeru” ndi akulu ake achikondi, otitsogolera moleza mtima m’njira imene tiyenera kuyendamo. Tili ndi ntchito yolalikira padziko lonse yoti tichite. (Mateyu 24:14, 45-47) Monga Nowa, amene anatsatira malangizo a Mulungu mosamalitsa, tiyenitu nthaŵi zonse tichite “momwemo.”
Mose—Wofatsa Woposa Anthu Onse
6, 7. (a) Kodi ndi chosankha chiti chopereka mphotho chimene Mose anapanga? (b) Kodi ndi chitsanzo cha kulimba mtima chotani chimene Mose anatisiyira?
6 Talingalirani munthu winanso wachikhulupiriro—Mose. Akanasangalala ndi moyo wa mwana alirenji pakati pa zokondweretsa za Igupto. Koma anasankha “kuchitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, kosati kukhala nazo zokondweretsa za zoipa za nthaŵi.” Monga mtumiki wotumidwa ndi Yehova, “anapenyerera chobwezera cha mphotho [napirira] molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo.”—Ahebri 11:23-28.
7 Pa Numeri 12:3, timaŵerenga kuti: “Munthuyu Mose ndiye wofatsa woposa anthu onse a pa dziko lapansi.” Mosiyana ndi ameneyo, Farao wa Igupto anachita ngati munthu wonyada woposa anthu onse. Pamene Yehova analamula Mose ndi Aroni kukalengeza chiweruzo chake kwa Farao, kodi iwo anatani? Tikuuzidwa kuti: “Mose ndi Aroni anachita monga Yehova anawalamulira, momwemo anachita.” (Eksodo 7:4-7) Ha, iwo ali chitsanzo cha kulimba mtima chotani nanga kwa ife olengeza ziweruzo za Mulungu lerolino!
8. Kodi ndi motani mmene Aisrayeli anafunikira kuchita “momwemo,” ndipo chikondwerero chotulukapo chidzafanana motani ndi chimene chidzachitika patsogolopa?
8 Kodi Aisrayeli anamchirikiza Mose mokhulupirika? Yehova atakantha Igupto ndi miliri isanu ndi inayi ya miliri khumi, anapatsa Israyeli malangizo onse ochitira Paskha. “Ndipo anthu anaŵerama, nalambira. Ndipo ana a Israyeli anamuka nachita monga Yehova adalamulira Mose ndi Aroni; anachita momwemo.” (Eksodo 12:27, 28) Tsiku lapadera limenelo la Nisani 14, 1513 B.C.E., pakati pa usiku, mngelo wa Mulungu anapha ana onse oyamba kubadwa a Aaigupto koma anapitirira nyumba za Aisrayeli. Nchifukwa ninji ana oyamba kubadwa a Aisrayeli anapulumuka? Chifukwa chakuti mwazi wa mwana wa nkhosa wa Paskha, wopaka pa mphuthu zawo, unawatetezera. Iwo anachita monga momwedi Yehova analamulira Mose ndi Aroni. Inde, “momwemo anachita.” (Eksodo 12:50, 51) Pa Nyanja Yofiira, Yehova anachita chozizwitsa china kupulumutsa anthu ake omvera ndi kuwononga Farao ndi magulu ake ankhondo amphamvu. Aisrayeli anakondwa chotani nanga! Momwemonso lerolino, ambiri amene amvera malamulo a Yehova adzakondwa kukhala mboni zoona ndi maso za kudzitsimikiziritsa kwake pa Armagedo.—Eksodo 15:1, 2; Chivumbulutso 15:3, 4.
9. Kodi ndi mwaŵi wotani wamakano umene ukuchitiridwa chithunzi ndi kuchita “momwemo” kwa Aisrayeli kulinga ku chihema?
9 Pamene Yehova analamula Israyeli kupereka chopereka ndi kumanga chihema m’chipululu, anthu mooloŵa manja anachirikiza zimenezo. Ndiyeno, Mose ndi antchito anzake ofunitsitsa anatsatira mapulani onse omangira omwe Yehova anawapatsa osasiyapo kali konse. “Potero anatsiriza ntchito yonse ya kachisi wa chihema chokomanako; ndipo ana a Israyeli adachita monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, anachita momwemo.” Momwemonso, pa kupatulidwa kwa ansembe, “anatero Mose; monga mwa zonse Yehova adamuuza, momwemo anachita.” (Eksodo 39:32; 40:16) Masiku ano, tili ndi mwaŵi wa kuchirikiza ndi mtima wonse ntchito yolalikira ndi maprogramu ofutukula za Ufumu. Chotero ndi mwaŵi wathu kugwirizana kuchita “momwemo.”
Yoswa—Wolimba Mtima ndi Wamphamvu
10, 11. (a) Kodi chinakonzekeretsa Yoswa kukometsa njira zake nchiyani? (b) Kodi nchiyani chingatilimbitse polimbana ndi mayeso amakono?
10 Pamene Mose anasankha Yoswa kuti atsogolere Israyeli kuloŵa m’dziko la lonjezano, mwachionekere panali Mawu a Yehova ouziridwa olembedwa kokha m’mabuku asanu a Mose, salmo limodzi kapena aŵiri, ndi buku la Yobu. Mose anauza Yoswa kusonkhanitsa anthuwo atafika m’Dziko Lolonjezedwa ndi ‘kulalikira chilamulo ichi pamaso pa Israyeli wonse, m’makutu mwawo.’ (Deuteronomo 31:10-12) Ndiponso, Yehova iye yekha analamula Yoswa kuti: “Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru.”—Yoswa 1:8.
11 Kuŵerenga “buku” la Yehova masiku onse kunamkonzekeretsa Yoswa kuyang’anizana ndi mayeso amtsogolo, monga momwedi kuŵerenga Mawu a Yehova, Baibulo, masiku onse kumalimbitsira Mboni Zake zamakono kulimbana ndi mayeso a “masiku otsiriza” ameneŵa ovuta. (2 Timoteo 3:1) Popeza tazingidwa ndi dziko lachiwawa, tiyeninso tilabadire chilangizo cha Mulungu kwa Yoswa: “Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usawope, kapena kutenga nkhaŵa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kuli konse umukako.” (Yoswa 1:9) Atagonjetsa Kanani, mafuko a Israyeli anafupidwa kwambiri pokhala m’choloŵa chawo. “Monga Yehova analamulira Mose, momwemo ana a Israyeli anachita.” (Yoswa 14:5) Mphotho yonga imeneyo ikutiyembekezera tonsefe amene timaŵerenga Mawu a Mulungu ndi kuwatsatira m’moyo wathu, tikumachita “momwemo” momvera.
Mafumu—Okhulupirika ndi Osamvera
12. (a) Kodi mafumu m’Israyeli anapatsidwa lamulo lotani? (b) Nanga kulephera kumvera kwa mafumuwo kunakhala ndi chotulukapo chotani?
12 Bwanji nanga za mafumu m’Israyeli? Yehova anafuna zotsatirazi kwa mfumu: “Kudzali, pakukhala iye pa mpando wachifumu wa ufumu wake, adzilemberere chofanana cha chilamulo ichi m’buku, achitenge pa ichi chili pamaso pa ansembe Alevi; ndipo azikhala nacho, naŵerengemo masiku onse a moyo wake; kuti aphunzire kuwopa Yehova Mulungu wake, kusunga mawu onse a chilamulo ichi ndi malemba aŵa, kuwachita.” (Deuteronomo 17:18, 19) Kodi mafumu a Israyeli anamvera lamulolo? Ambiri analephera kowopsa, kwakuti anawadzera matemberero onenedweratu pa Deuteronomo 28:15-68. Potsirizira pake, Israyeli anabalalika “kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero a dziko lapansi.”
13. Mofanana ndi Davide, kodi tingapindule motani mwa kusonyeza chikondi pa Mawu a Yehova?
13 Komabe, Davide—mfumu yaumunthu yoyamba yokhulupirika m’Israyeli—anasonyeza kudzipereka kwambiri kwa Yehova. Anakhaladi ‘mwana wa mkango m’Yuda,’ akumachitira chithunzi Kristu Yesu, “mkango wochokera m’fuko la Yuda, muzu wa Davide” wolakikayo. (Genesis 49:8, 9; Chivumbulutso 5:5) Kodi Davide anaipeza kuti nyonga yake? Iye anali ndi chiyamikiro chozama cha Mawu olembedwa a Yehova ndipo anawatsatira. M’Salmo 19, “salmo la Davide,” timaŵerenga kuti: “Malamulo a Yehova ali angwiro.” Atatchula zikumbutso, malangizo, lamulo, ndi ziweruzo za Yehova, Davide akupitiriza kuti: “Ndizo zofunika koposa golidi, inde, golidi wambiri woyengetsa: zizuna koposa uchi ndi zakukha za zisa zake. Ndiponso kapolo wanu achenjezedwa nazo: m’kuzisunga izo muli mphotho yaikulu.” (Salmo 19:7-11) Ngati kuŵerenga Mawu a Yehova masiku onse ndi kuwasinkhasinkha kunali ndi mphotho zaka 3,000 zapitazo, ziyenera kuposapo chotani nanga lerolino!—Salmo 1:1-3; 13:6; 119:72, 97, 111.
14. Kodi njira imene Solomo anatenga imasonyeza motani kuti pamafunika zinthu zina zoposa chidziŵitso chabe?
14 Komabe, si kokwanira kungopeza chidziŵitso. Atumiki a Mulungu afunikanso kugwiritsira ntchito chidziŵitsocho, kuchitsatira malinga ndi chifuniro cha Mulungu—inde, kuchita “momwemo.” Tingagwiritsire ntchito monga chitsanzo nkhani ya Solomo mwana wa Davide, amene Yehova anasankha “akhale pa mpando wachifumu wa ufumu wa Yehova kuweruza Israyeli.” Solomo analandira ntchito yomanga kachisi, mwa kugwiritsira ntchito mapulani amene Davide analandira “mouziridwa.” (1 Mbiri 28:5, 11-13) Kodi Solomo akanaichita motani ntchito yaikuluyo? Poyankha pemphero lake, Yehova anampatsa nzeru ndi chidziŵitso. Ndi zinthu zimenezi, ndipo mwa kutsatira mosamalitsa mapulani omwe Mulungu anapereka, Solomo anamanga nyumba yaikuluyo, imene inadzazidwa ndi ulemerero wa Yehova. (2 Mbiri 7:2, 3) Komabe, m’kupita kwa nthaŵi, Solomo anadzalephera. Pambali iti? Chilamulo cha Yehova chinati ponena za mfumu m’Israyeli: “Asadzichulukitsire akazi, kuti ungapatuke mtima wake.” (Deuteronomo 17:17) Koma Solomo “anali nawo akazi mazana asanu ndi aŵiri, ana aakazi a mfumu, ndi akazi achabe mazana atatu; ndipo akazi ake . . . anapambutsa mtima wake atsate milungu ina.” Atakalamba, Solomo analeka kuchita “momwemo.”—1 Mafumu 11:3, 4; Nehemiya 13:26.
15. Kodi ndi motani mmene Yosiya anachitira “momwemo”?
15 Mu Yuda munali mafumu angapo omvera, womaliza anali Yosiya. M’chaka cha 648 B.C.E., iye anayamba kuchotsa mafano m’dziko ndi kukonza kachisi wa Yehova. Ndiko kumene mkulu wa ansembe anapezako “buku la chilamulo la Yehova mwa dzanja la Mose.” Kodi Yosiya anachita chiyani pamenepo? “Nikwera mfumu ku nyumba ya Yehova ndi amuna onse a m’Yuda, ndi okhala m’Yerusalemu, ndi ansembe ndi Alevi, ndi anthu onse akulu ndi ang’ono; naŵerenga iye m’makutu mwawo mawu onse a buku la chipangano adalipeza m’nyumba ya Yehova. Ndipo mfumu inaimirira pokhala pake, nichita pangano pamaso pa Yehova, kuti adzayenda chotsata Yehova, ndi kusunga malamulo ake, ndi mboni zake, ndi malemba ake, ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse, kuchita mawu a chipangano olembedwa m’bukumu.” (2 Mbiri 34:14, 30, 31) Inde, Yosiya “anachita momwemo.” Chifukwa cha kukhulupirika kwake, chiweruzo cha Yehova pa Yuda wosakhulupirika sichinaperekedwe kufikira m’masiku a ana ake opulupudza.
Kutsatira Mawu a Mulungu
16, 17. (a) Kodi ndi m’mbali ziti zimene tiyenera kutsatira mapazi a Yesu? (b) Kodi ndi atumiki ena ati okhulupirika a Mulungu amene akupereka zitsanzo kwa ife?
16 Pa anthu onse amene anakhalako, Ambuye Yesu Kristu ndiye chitsanzo chabwino koposa pakusinkhasinkha Mawu a Mulungu ndi kuwatsatira. Mawu a Mulungu anali ngati chakudya kwa iye. (Yohane 4:34) Anauza omvetsera ake kuti: “Sakhoza Mwana kuchita kanthu pa yekha, koma chimene aona Atate achichita, ndicho. Pakuti zimene iye azichita, zomwezo Mwanayo azichita momwemo.” (Yohane 5:19, 30; 7:28; 8:28, 42) Yesu “anachita momwemo,” akumati: “Ndinatsika kumwamba, si kuti ndichite chifuniro changa, koma chifuniro cha iye amene anandituma ine.” (Yohane 6:38) Ife amene tili Mboni zodzipatulira za Yehova tifunikira kuchita “momwemo” mwa kutsatira mapazi a Yesu.—Luka 9:23; 14:27; 1 Petro 2:21.
17 Kuchita chifuniro cha Mulungu kunali patsogolo nthaŵi zonse m’maganizo a Yesu. Iye anali kuwadziŵa bwino lomwe Mawu a Mulungu choncho anali wokonzeka kupereka mayankho a m’Malemba. (Mateyu 4:1-11; 12:24-31) Mwa kusamalira Mawu a Mulungu nthaŵi zonse, nafenso tingakhale ‘oyenera, okonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.’ (2 Timoteo 3:16, 17) Tiyeni titsanzire chitsanzo cha atumiki a Yehova okhulupirika akale ndipo koposa zonse chija cha Ambuye wathu, Yesu Kristu, yemwe anati: “Kuti dziko lapansi lizindikire kuti ndikonda Atate, ndi kuti ndichita monga momwe Atate wandilamulira.” (Yohane 14:31) Ifenso tisonyezetu chikondi chathu pa Mulungu mwa kupitiriza kuchita “momwemo.”—Marko 12:29-31.
18. Kodi nchiyani chiyenera kutisonkhezera ‘kukhala akuchita mawu,’ nanga nkhani yotsatira idzafotokoza chiyani?
18 Pamene tisinkhasinkha pa kumvera kwa atumiki a Mulungu a m’nthaŵi za Baibulo, kodi sitikulimbikitsidwa kuchita utumiki mokhulupirika m’masiku omalizira a dongosolo loipa la Satana? (Aroma 15:4-6) Inde, tiyenera kusonkhezeredwa ‘kukhala akuchitadi mawu’ m’zinthu zonse monga momwe nkhani yotsatira idzafotokozera.—Yakobo 1:22.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi “chikondi cha Mulungu” chiyenera kutanthauzanji kwa ife?
◻ Kodi zitsanzo za Nowa, Mose, ndi Yoswa zikutiphunzitsanji?
◻ Kodi mafumu m’Israyeli anamvera “mawu” a Mulungu pamlingo wotani?
◻ Kodi Yesu ali Wotipatsa Chitsanzo motani pakuchita “momwemo”?
[Zithunzi patsamba 15]
Nowa, Mose, ndi Yoswa “anachita momwemo”