Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 2/1 tsamba 31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Nkhani Yofanana
  • “Ndiwe Mkazi Wokongola”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Yehova Anamutchula Kuti “Mfumukazi”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Abrahamu ndi Sara Mungatsanzire Chikhulupiriro Chawo!
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Anakhala Ndi Mwana Atakalamba
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 2/1 tsamba 31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi Farao anakwatiradi Sara, mkazi wa Abrahamu, monga momwe zimawonekera m’kumasuliridwa kwa Genesis 12:19 m’matembenuzidwe a Mabaibulo ena?

Ayi, Farao anachinjirizidwa kutenga Sara (Sarai) kukhala mkazi wake. Chifukwa chake, ulemu ndi khalidwe la Sara sizinanyazitsidwe.

Timathandizidwa kuwona zimenezi mwakusanthula nkhaniyo m’mawu ake apatsogolo ndi apambuyo. Njala inamkakamiza Abrahamu (Abramu) kuthaŵira ku Igupto kwakanthaŵi. Anawopa kuti moyo wake ukakhala pachiswe kumeneko chifukwa cha mkazi wake wokongola, Sara. Abrahamu anali asanabale mwana mwa Sara, choncho ngati akakumana ndi imfa ku Igupto, mzera wa Mbewu ukasweka, Mbewu kupyolera mwa imene mabanja onse a padziko lapansi akadalitsidwa. (Genesis 12:1-3) Choncho Abrahamu anauza Sara kunena kuti ndimlongo wake, pakutitu analidi mlongo wake wa mimba ina.​—Genesis 12:10-13; 20:12.

Kuwopa kwake sikunali kopanda maziko. Katswiri August Knobel anafotokoza kuti: “Abramu anapempha Sarai kudzisonyeza monga mlongo wake ku Igupto kotero kuti asaphedwe. Ngati mkaziyo akanawonedwa monga wokwatiwa, Mwigupto akanamlanda kokha mwakupha mwamuna wake mwiniyo; ngati akawonedwa monga mlongo wake, panali kuthekera kwa kumkopa mwakunyengerera mbale wake mwamtendere.

Komabe, akalonga a Igupto sanakambitsirane ndi Abrahamu za kufuna kwa Farao kukwatira Sara. Anangobweretsa Sara wokongolayo m’nyumba ya Farao, ndipo wolamulira wa Igupto ameneyo anapatsa mphatso wotengedwa kukhala mbale wakeyo, Abrahamu. Koma pambuyo pa zimenezo, Yehova anakantha banja la Farao ndi miliri. Pamene chowona chinavumbulidwa kwa Farao mwanjira yosatchulidwa, iye anati kwa Abrahamu: ‘Chifukwa chanji unati, Ndiye mlongo wanga? [kotero kuti ndinatsala pang’ono kumtenga kuti akhale mkazi wanga, “NW”]; tsopano suyu mkazi wako; mtenge nuchoke.’​—Genesis 12:14-19.

The New English Bible ndi matembenuzidwe ena Abaibulo amamasulira mawu akanyenye alipamwambapa a vesilo motere “kotero kuti ndinamtenga monga mkazi wanga” kapena mawu ofananako. Pamene kuli kwakuti sikumasulira kolakwa kwenikweni, mawu oterowo angapereke lingaliro lakuti Farao anakwatiradi Sara, kuti ukwati unali chochitika chenicheni. Onani kuti pa Genesis 12:19 mneni Wachihebri womasuliridwa “kutenga” ali m’kaimidwe kosonyeza ntchito imene sinamalizidwebe. New World Translation imamasulira mneni Wachihebri ameneyu mogwirizana ndi mawu apatsogolo ndi apambuyo a nkhaniyo ndi mwanjira imene imasonyeza bwino lomwe kaimidwe ka mneniyo​—“kotero kuti ndinatsala pang’ono kumtenga kuti akhale mkazi wanga.”a Ngakhale kuti Farao ‘anatsala pang’ono kumtenga’ Sara kuti akhale mkazi wake, anali asanachitebe mwambo uliwonse kapena dzoma loloŵetsedwamo.

Kaŵirikaŵiri Abrahamu wasulizidwa chifukwa cha njira imene anasamalirira nkhaniyo, koma anachita motero chifukwa cha Mbewu yolonjezedwa ndipo motero chifukwa cha anthu onse.​—Genesis 3:15; 22:17, 18; Agalatiya 3:16.

Panthaŵi yofanana imene mwachiwonekere inalinso yaupandu, Isake anauza mkazi wake, Rebeka, kupeŵa kutchula kuti anali wokwatiwa. Panthaŵiyo mwana wawo Yakobo, amene mzera wa Mbewu ukadzera mwa iye, anali atabadwa kale ndipo mwachiwonekere anali mnyamata. (Genesis 25:20-27; 26:1-11) Chikhalirechobe, cholinga cha kachitidwe kolungama kameneka chingakhale chinali chimodzimodzi ndi cha Abrahamu. M’nthaŵi yanjala Isake ndi banja lake anali kukhala m’dziko la mfumu ya Afilisiti yotchedwa Abimeleke. Ngati akanazindikira kuti Rebeka anali wokwatiwa kwa Isake, Abimeleke akanafuna njira yambanda yophera banja lonse la Isake, zimene zikanatanthauza imfa kwa Yakobo. M’chochitika ichinso, Yehova analoŵererapo kutetezera atumiki ake ndi mzera wa Mbewuyo.

[Mawu a M’munsi]

a Matembenuzidwe a J. B. Rotherham amati: “Chifukwa ninji unati, Iye ndimlongo wanga; ndipo chotero ndinali pafupi kumtenga akhale mkazi wanga?”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena