-
Moyo Wawo Unali Wovuta Koma “Anamanga Nyumba ya Isiraeli”Nsanja ya Olonda—2007 | October 1
-
-
Ana a Rakele
Nthawi imeneyo, munthu akakhala wosabereka ankaonedwa ngati wotembereredwa. Mulungu analonjeza Abulahamu, Isake, ndi Yakobo kuti banja lawo ndi limene lidzabereka “mbewu” ndipo kudzera mwa mbewuyo mabanja onse adzadalitsidwa. (Genesis 26:4; 28:14) Rakele analibe mwana. Koma Yakobo ankadziwa kuti ndi Mulungu yekha amene angapatse Rakele ana kuti madalitsowo adzerenso mwa iye. Rakele sanathe kudikira. Iye anati: “Taonani mdzakazi wanga Biliha, mulowe kwa iye; ndipo iye adzabala pa maondo anga, kuti inenso ndionerepo ana pa iye.”—Genesis 30:2, 3.
Mwina ife sitingamvetse zimene Rakele anachita. Koma mapangano akale onena za ukwati, omwe anapezedwa ku Near East, amasonyeza kuti zinali zofala kuti mkazi wosabereka apatse mwamuna wake mdzakazi kuti am’berekere mwana.a (Genesis 16:1-3) Ndipo nthawi zina, ana a mdzakaziyo ankatengedwa kuti ndi a mkazi wosaberekayo.
Pamene Biliha anabereka mwana wamwamuna, Rakele ananena mosangalala kuti: “Mulungu wandiweruzira ine, namva mawu anga, nandipatsa ine mwana.” Mwanayo anam’patsa dzina lakuti Dani, limene limatanthauza kuti “Woweruza.” Rakele nayenso anali atapemphera za vuto lake. Pamene Biliha anabereka mwana wake wachiwiri dzina lake Nafitali, limene limatanthauza “Ndalimbana,” Rakele anati: “Ndi malimbano a Mulungu ndalimbana naye mkulu wanga, ndipo ndapambana.” Maina a anawa amasonyeza kuti panali kupikisana pakati pa akazi awiriwa.—Genesis 30:5-8.
Mwina Rakele ankaganiza kuti akuchita zogwirizana ndi mapemphero ake popereka Biliha kwa Yakobo. Komatu, imeneyi siinali njira ya Mulungu yom’patsira ana. Zimenezi zikutiphunzitsa kuti tikapemphera kwa Yehova, tizimudikira kuti ayankhe. Iye angayankhe mapemphero athu m’njira yosayembekezereka ndiponso panthawi yomwe sitikuyembekezera.
-
-
Moyo Wawo Unali Wovuta Koma “Anamanga Nyumba ya Isiraeli”Nsanja ya Olonda—2007 | October 1
-
-
a Pangano lina limene linapezedwa ku Nuzi, m’dziko la Iraq linati: “Kelim-ninu tam’pereka kwa Shennima kuti akhale mkazi wake. . . . Ngati Kelim-ninu sadzabereka [ana], Kelim-ninu adzakatenge mkazi [mdzakazi] ku dera la Lullu kuti akhale mkazi wa Shennima.”
-