-
Moyo Wawo Unali Wovuta Koma “Anamanga Nyumba ya Isiraeli”Nsanja ya Olonda—2007 | October 1
-
-
Zimene zinachitika pamene mwana wa Leya, Rubeni, anapeza zipatso zomwe iwo ankakhulupirira kuti ndi mankhwala othandiza kubereka, zimasonyeza bwino kusagwirizana komwe kunalipo pakati pa Rakele ndi Leya. Rakele anapempha zipatsozo koma Leya anayankha mokwiya kuti: “Kodi m’pachabe kuti iwe wachotsa mwamuna wanga? Kodi ufuna kuchotsanso mankhwala a mwana wanga?” Ena amati mawu amenewa amasonyeza kuti Yakobo ankakhala kwambiri ndi Rakele kuposa Leya. Mwina Rakele anamvetsa kudandaula kwa Leya, chifukwa anayankha kuti: “Chifukwa chake iye adzagona nawe usiku uno chifukwa cha mankhwala a mwana wako.” Choncho, Yakobo atabwera kunyumba madzulo, Leya anamuuza kuti: “Ulowe kwa ine chifukwa ndakulipirira iwe ndi mankhwala a mwana wanga.”—Genesis 30:15, 16.
-
-
Moyo Wawo Unali Wovuta Koma “Anamanga Nyumba ya Isiraeli”Nsanja ya Olonda—2007 | October 1
-
-
Zipatso zija sizinathandize. Patapita zaka 6 ali m’banja, Rakele anabereka Yosefe chifukwa choti Yehova ‘anam’kumbukira’ ndipo anayankha mapemphero ake. Apa m’pamene iye anatha kunena kuti: “Mulungu wachotsa manyazi anga.”—Genesis 30:22-24.
-