Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yehova Ndiye Chitsanzo Chachikulu Pankhani Yosonyeza Ubwino
    Nsanja ya Olonda—2002 | January 15
    • 12 M’maŵa wake, ukoma wa Yehova unadutsa pamaso pa Mose pa Phiri la Sinai. Panthaŵi imeneyo, Mose anaona mwachimbuuzi ulemerero wa Mulungu ndipo anamva mawu akuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza [“wosakwiya msanga,” NW], ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi; wakusungira anthu osaŵerengeka chifundo [“kukoma mtima,” NW], wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula; wakulangira ana ndi zidzukulu chifukwa cha mphulupulu ya atate awo, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinayi.” (Eksodo 34:6, 7) Mawu ameneŵa akusonyeza kuti ubwino wa Yehova ndi wogwirizana ndi kukoma mtima kwake pamodzinso ndi makhalidwe ake ena. Kupenda zimenezi kutithandiza kuchita zabwino. Tiyeni choyamba tipende khalidwe limene alitchula kaŵiri m’mawu ochititsa chidwi a Mulungu ameneŵa.

  • Yehova Ndiye Chitsanzo Chachikulu Pankhani Yosonyeza Ubwino
    Nsanja ya Olonda—2002 | January 15
    • 13. Kodi ndi khalidwe liti limene alitchula kaŵiri m’mawu onena za ubwino wa Mulungu, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi n’zoyenerera?

      13 “Yehova [ndi] Mulungu . . . wa ukoma mtima wochuluka . . . wakusungira anthu osaŵerengeka chifundo [“kukoma mtima,” NW].” Liwu la Chihebri limene analimasulira kuti “ukoma mtima” limatanthauzanso “chikondi chokhulupirika.” Ndi khalidwe lokhali limene alitchula kaŵiri m’mawu amene Mulungu anamuuza Mose. Zimenezi n’zoyenereratu kwambiri popeza khalidwe lalikulu la Yehova ndilo chikondi. (1 Yohane 4:8) Mawu odziŵika bwino otamanda Yehova akuti, “pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo [“kukoma mtima,”NW] chake chikhala chikhalire,” akutsindika khalidwe limeneli.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena