Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Angelo Ndi Ndani, Nanga Amachita Chiyani?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • Zinthu zosiyanasiyana zokhudza ufiti komanso kukhulupirira zamizimu, monga thabwa la zamatsenga, mipira yagalasi, buku la mavampaya makadi, zidole, zofukiza komanso zithumwa.

      5. Muzipewa zamizimu

      Satana ndi ziwanda ndi adani a Yehova komanso a anthufe. Werengani Luka 9:38-42, kenako mukambirane funso ili:

      • Kodi ziwanda zimawachitira zotani anthu?

      Sitifuna kumachita zinthu zomwe zingapangitse kuti ziwanda zizitivutitsa. Werengani Deuteronomo 18:10-12, kenako mukambirane mafunso awa:

      • Kodi ziwanda zimafuna kumalankhula nafe komanso kutipusitsa pogwiritsa ntchito njira ziti? Kodi ndi zinthu ziti zomwe zimakonda kuchitika komwe mumakhala?

      • Kodi mukuona kuti ndi zomveka Yehova akamatiletsa kuchita zamizimu? N’chifukwa chiyani mukutero?

      Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

      VIDIYO: “Tsutsani Mdyerekezi” (5:02)

      • Kodi mukuganiza kuti khoza limene Palesa anamveka mwana wake linali loopsa? N’chifukwa chiyani mukutero?

      • Kodi Palesa anafunika kuchita chiyani kuti asamavutitsidwe ndi ziwanda?

      Akhristu enieni salola kuti ziwanda ziziwavutitsa. Werengani Machitidwe 19:19 ndi 1 Akorinto 10:21, kenako mukambirane funso ili:

      • Ngati muli ndi zinthu zokhudzana ndi zamizimu, n’chifukwa chiyani muyenera kuziwotcha kapena kuzitaya?

      Mayi akuwotcha zinthu zosiyanasiyana zokhudzana ndi zamizimu.
  • N’chiyani Chimachitikira Munthu Amene Wamwalira?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • 2. Kodi kudziwa zenizeni zimene zimachitika munthu akamwalira n’kothandiza bwanji?

      Anthu ambiri amachita mantha ndi imfa ngakhalenso ndi anthu amene anamwalira. Koma mukaphunzira zimene Baibulo limanena zokhudza imfa mulimbikitsidwa kwambiri. Yesu anati: “Choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti pali chinachake chimene chimapitiriza kukhala ndi moyo munthu akamwalira. Koma Baibulo siliphunzitsa zimenezi. Choncho munthu akamwalira savutika kapena kumva kupweteka. Komanso akufa sangativulaze chifukwa sadziwa chilichonse. Choncho, sitiyenera kuchita chilichonse chosonyeza kuti tikulambira kapena kulemekeza akufa poopa kuti angativulaze.

      Anthu ena amanena kuti angathe kulankhula ndi amene anamwalira. Koma zimenezi sizingatheke. Monga mmene taphunzirira, anthu amene anamwalira, “sadziwa chilichonse.” Amene amaganiza kuti akulankhulana ndi achibale awo amene anamwalira, amakhala akulankhulana ndi ziwanda zimene zimayerekezera kukhala munthu womwalirayo. Choncho kudziwa zenizeni zimene zimachitika munthu akamwalira, kumatiteteza kuti tisamavutitsidwe ndi ziwanda. Yehova amatichenjeza kuti tisayese kulankhulana ndi anthu amene anamwalira chifukwa amadziwa kuti kulankhulana ndi ziwanda kungatibweretsere mavuto aakulu.​—Werengani Deuteronomo 18:​10-12.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena