-
Mmene Moyo wa Mose UmakukhudziraniGalamukani!—2004 | April 8
-
-
Mneneri Wangati Mose
Tikukhala m’nthaŵi zosautsa. Ndithu, anthu akufunikira mtsogoleri wangati Mose; mtsogoleri amene ali ndi mphamvu zotha kuchita zinthu, kulamulira anthu, komanso wakhalidwe labwino, wolimba mtima, wachifundo, ndiponso wokondadi chilungamo ndi mtima wake wonse. Mose atamwalira, Aisrayeli ayenera kuti ankadzifunsa kuti, ‘Kodi padziko pano padzapezekanso munthu wina wangati ameneyu?’ Mose mwini anali atayankha kale funso limeneli.
Zimene Mose analemba zimafotokoza mmene matenda ndi imfa zinabwerera komanso chifukwa chimene Mulungu analolera kuti zoipa zipitirire. (Genesis 3:1-19; Yobu chaputala 1, 2) Pa Genesis 3:15, pali ulosi woyambirira wa Mulungu ndipo umalonjeza kuti zoipa zidzathetsedwa! Kodi zidzathetsedwa motani? Ulosiwo unasonyeza kuti kudzabadwa munthu amene adzadzetse chipulumutso. Lonjezo limeneli ndilo linayambitsa chiyembekezo chakuti kudzabwera Mesiya ndipo adzapulumutsa anthu. Koma kodi ndani adzakhale Mesiyayo? Mose anatithandiza kum’dziŵa mosakayikira.
Kutatsala nthaŵi yochepa kuti afe, Mose ananena mawu olosera akuti: “Yehova Mulungu wanu adzakuukitsirani mneneri wa pakati panu, wa abale anu, wonga ine; muzimvera iye.” (Deuteronomo 18:15) M’tsogolo mwake mtumwi Petro ananena mawu ameneŵa polongosola za Yesu.—Machitidwe 3:20-26.
Akatswri ambiri achiyuda otsata nkhani zoterezi amatsutsa kwambiri zakuti lembali limayerekezera Mose ndi Yesu. Iwo amati mawu a mlembali angagwirizane ndi mneneri aliyense woona amene anakhalapo Mose atafa. Komabe malingana ndi Baibulo lotchedwa Tanakh—The Holy Scriptures lofalitsidwa ndi bungwe lachiyuda lofalitsa mabuku lotchedwa Jewish Publication Society, lemba la Deuteronomo 34:10 limati: “Sipanakhalekonso mneneri wina ku Israyeli wangati Mose, amene AMBUYE anam’sankha, pamasom’pamaso.”—Deuteronomo 34:10.
Inde, Mose atamwalira kunabwera aneneri ambiri okhulupirika, monga Yesaya ndi Yeremiya. Koma palibe amene anagwirizanako ndi Mulungu ngati Mose, moti n’kumachita kulankhulana naye “pamasom’pamaso.” Motero lonjezo la Mose lakuti kudzabwera ‘mneneri wangati iyeyo’ silimanena za munthu wina ayi, koma Mesiya basi! N’zochititsa chidwi kuti umu ndi mmene anthu ophunzira achiyuda ankaonera nkhaniyi Chikristu chisanayambe ndiponso Akristu asanayambe kuzunzidwa ndi Akristu onyenga. Mfundo zoyandikira ku mfundo imeneyi zimapezeka mu mabuku angapo achiyuda, monga m’buku la Midrash Rabbah, limene limafotokoza kuti Mose ndiye anatsogola pokonzekera kubwera kwa “Momboli wam’tsogolo,” kapena kuti Mesiya.
Palibe angatsutse zakuti Yesu anali ngati Mose m’njira zambiri. (Onani bokosi lakuti “Yesu Anali Mneneri Wangati Mose.”) Yesu anali ndi mphamvu zotha kuchita zinthu ndiponso anali ndi ulamuliro. (Mateyu 28:19) Yesu ndi munthu “wofatsa ndi wodzichepetsa mtima.” (Mateyu 11:29) Yesu amadana ndi kuchita zoipa ndiponso kusoŵa chilungamo. (Ahebri 1:9) Motero Yesu angathe kukwanitsa utsogoleri wangati umene tikuufuna kwambiriwu! Ndi iyeyo amene posachedwapa adzathetse zoipa zonse ndi kukonza dzikoli kuti likhale ngati Paradaiso amene amatchulidwa m’Baibulo.b
-
-
Mmene Moyo wa Mose UmakukhudziraniGalamukani!—2004 | April 8
-
-
[Bokosi patsamba 29]
Yesu Anali Mneneri Wangati Mose
Yesu anali ngati Mose m’njira zina izi:
▲ Mose ndiponso Yesu ali makanda anapulumuka pamene atsogoleri a panthaŵi yawo analamula kuti makanda onse aamuna aphedwe.—Eksodo 1:22; 2:1-10; Mateyu 2:13-18.
▲ Mose anaitanidwa kuchoka ku Aigupto pamodzi ndi mtundu wa Israyeli womwe unali ‘mwana woyamba’ wa Yehova. Yesu anaitanidwa kuchoka ku Aigupto monga mwana woyamba wa Mulungu.—Eksodo 4:22, 23; Hoseya 11:1; Mateyu 2:15, 19-21.
▲ Mose ndiponso Yesu anasala kudya kwa masiku 40 ali m’chipululu.—Eksodo 34:28; Mateyu 4:1, 2.
▲ Mose ndiponso Yesu anali ofatsa komanso odzichepetsa kwambiri.—Numeri 12:3; Mateyu 11:28-30.
▲ Mose ndiponso Yesu ankachita zozizwitsa.—Eksodo 14:21-31; Salmo 78:12-54; Mateyu 11:5; Marko 5:38-43; Luka 7:11-15, 18-23.
▲ Mose ndiponso Yesu anali amkhalapakati a mapangano a pakati pa Mulungu ndi anthu ake.—Eksodo 24:3-8; 1 Timoteo 2:5, 6; Ahebri 8:10-13; 12:24.
-