Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Anali “Mkazi Wabwino Kwambiri”
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
    • 7, 8. (a) Kodi Naomi anaona kuti zimene Boazi anachita zinali zochokera kwa ndani ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Kodi Rute anasonyeza apongozi ake chikondi chosatha m’njira ina iti?

      7 Kenako Naomi ndi Rute anayamba kucheza ndipo Rute anafotokoza zabwino zimene Boazi anamuchitira. Atachita chidwi ndi zimene Boazi anachitazo, Naomi ananena kuti: “Yehova amene sanaleke kusonyeza kukoma mtima kosatha kwa amoyo ndi akufa, am’dalitse munthu ameneyu.” (Rute 2:20) Iye anaona kuti zimene Boazi anachita, zinali zochokera kwa Yehova yemwe amachititsa atumiki ake kukhala owolowa manja. Yehova amalonjeza kuti adzadalitsa atumiki ake amene amakomera mtima anthu ena.a—Werengani Miyambo 19:17.

  • Anali “Mkazi Wabwino Kwambiri”
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
    • a Monga Naomi ananenera, Yehova amawasonyeza anthu kukoma mtima, ngakhalenso amene anamwalira. Mwamuna wa Naomi komanso ana ake awiri anali atamwalira. Ndipo mmodzi mwa ana a Naomi amene anamwalirawo, anali mwamuna wake wa Rute. N’zosakayikitsa kuti amuna atatu onsewa ankakonda kwambiri Naomi ndi Rute. Choncho kukomera mtima Naomi ndi Rute tingati kunalinso kukomera mtima amunawo, chifukwa iwo akanakonda kuti azimayiwa azisamalidwa.

      b Monga zinalili pa nkhani ya cholowa, mchimwene weniweni wa mwamuna womwalirayo ndi amene ankayenera kukwatira mkazi wamasiyeyo. Koma ngati palibe wotereyu, achibale ake ena a mwamunayo ankayenera kukwatira mkaziyo.—Num. 27:5-11.

  • Anali “Mkazi Wabwino Kwambiri”
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
    • 11, 12. (a) Pamene Naomi anatchula Boazi kuti anali ‘wowawombola,’ kodi ankanena za lamulo liti lomwe linali m’Chilamulo cha Mulungu? (b) Kodi Rute anatani apongozi ake atamuuza zoti achite?

      11 Pamene Rute anatchula za Boazi, Naomi ananena kuti: “Munthuyutu ndi wachibale wathu. Ndi mmodzi wa otiwombola.” (Rute 2:20) Kodi iye ankatanthauza chiyani? M’Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Aisiraeli, munali lamulo lothandiza mabanja ovutika chifukwa cha umphawi kapena umasiye. Mayi amene mwamuna wake wamwalira asanam’berekere mwana, ankakhala wachisoni kwambiri chifukwa ankaona kuti dzina la mwamuna wakeyo lifa ndipo lithera pomwepo. Choncho Chilamulo cha Mulungu chinkati mchimwene wake wa munthuyo ayenera kukwatira mkaziyo kuti amuberekere mwana woti atenge dzina la bambo ake komanso kusamalira chuma cha banjalo.b—Deut. 25:5-7.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena