-
“Wakumva Pemphero”Nsanja ya Olonda—2010 | October 1
-
-
KODI Yehova Mulungu amayankhadi mapemphero ochokera pansi pa mtima a anthu amene amadzipereka ndi mtima wonse pomulambira? Nkhani ya m’Baibulo ya munthu wina wosadziwika kwenikweni dzina lake Yabezi imasonyeza kuti Yehova ‘amamvadi pemphero’ (Salimo 65:2) Nkhani yachidule imeneyi imapezeka pa mndandanda wa mayina ofotokoza mibadwo ya anthu chakumayambiriro kwa buku la 1 Mbiri. Tiyeni tione 1 Mbiri 4:9, 10.
Nkhani yonse ya Yabezi imangopezeka m’mavesi awiri amenewa basi. Malinga ndi vesi 9, ‘mayi ake ndiwo anamutcha dzina lakuti Yabezi, chifukwa anati: “Ndam’bereka ndikumva ululu.”’a N’chifukwa chiyani anasankha dzina limeneli? Kodi iye anamva ululu kwambiri kuposa umene akazi amamva nthawi zonse pobereka? Kodi kapena anali wamasiye ndipo ankadandaula kuti mwamuna wake sanaone mwana wakeyu atabadwa? Baibulo silinena kalikonse pa nkhani imeneyi. Koma mayiyu sankadziwa kuti tsiku lina adzanyadira za mwana wakeyu. N’kutheka kuti abale ake a Yabezi anali anthu abwino koma ‘Yabezi anali wolemekezeka kwambiri kuposa abale akewo.’
-
-
“Wakumva Pemphero”Nsanja ya Olonda—2010 | October 1
-
-
a Dzina lakuti Yabezi ndi lochokera ku mawu amene amatanthauza “ululu.”
-