PHUNZIRO 04
Kodi Mulungu Ndi Ndani?
Kuyambira kalekale, anthu akhala akulambira milungu yosiyanasiyana. Koma Baibulo limanena kuti pali Mulungu mmodzi yemwe “ndi wamkulu kuposa milungu ina yonse.” (2 Mbiri 2:5) Kodi Mulungu ameneyu ndi ndani? Nanga n’chifukwa chiyani ndi wamkulu kuposa Milungu ina yonse imene anthu amalambira? M’phunziroli tiona zimene Mulungu wachita kuti mumudziwe bwino.
1. Kodi dzina la Mulungu ndi ndani, nanga tikudziwa bwanji kuti amafuna kuti tilidziwe?
Mulungu amafuna kuti timudziwe, ndipo amatiuza dzina lake m’Baibulo. Iye anati: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.” (Werengani Yesaya 42:5, 8.) Dzina lakuti “Yehova” analimasulira kuchokera ku dzina la Chiheberi ndipo zikusonyeza kuti limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhala.” Yehova amafuna kuti tidziwe dzina lake. (Ekisodo 3:15) Tikudziwa bwanji zimenezi? Iye anachititsa kuti dzina lake lilembedwe m’Baibulo maulendo oposa 7,000.a Dzina lakuti Yehova ndi la “Mulungu woona, kumwamba ndiponso padziko lapansi.”—Deuteronomo 4:39.
2. Kodi Baibulo limatiuza zotani zokhudza Yehova?
Baibulo limatiuza kuti pa milungu yonse imene anthu amailambira, Mulungu woona ndi Yehova yekha. N’chifukwa chiyani tikutero? Pali zifukwa zambiri. Yehova ndi wolamulira wamkulu, ndipo iye yekha ndi “Wam’mwambamwamba, woyenera kulamulira dziko lonse lapansi.” (Werengani Salimo 83:18.) Iye ndi “Wamphamvuyonse,” kutanthauza kuti ali ndi mphamvu zochitira chilichonse chimene wasankha. Iye ndi amene ‘analenga zinthu zonse,’ zakumwamba ndi zapadziko lapansi. (Chivumbulutso 4:8, 11) Mosiyana ndi wina aliyense, Yehova alibe chiyambi komanso alibe mapeto.—Salimo 90:2.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kusiyana pakati pa mayina audindo a Mulungu ndi dzina lake lenileni lomwe ndi lapadera. Kenako onani zimene Mulungu anachita kuti mudziwe dzina lake ndiponso chifukwa chake anatero.
3. Mulungu ali ndi mayina audindo ambiri, koma dzina lake lenileni ndi limodzi lokha
Kuti muone kusiyana kwa dzina la udindo ndi dzina lenileni, onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili.
Kodi dzina laudindo ngati lakuti “Ambuye,” ndi losiyana bwanji ndi dzina lenileni?
Baibulo limanena kuti anthu amalambira milungu ndi ambuye ambiri. Werengani Salimo 136:1-3, kenako mukambirane funso ili:
Kodi “Mulungu wa milungu” ndi “Mbuye wa ambuye” ndi ndani?
4. Yehova akufuna kuti mudziwe dzina lake n’kumaligwiritsira ntchito
N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova amafuna kuti mudziwe dzina lake? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:
Kodi inuyo mukuona kuti Yehova akufuna kuti anthu adziwe dzina lake? N’chifukwa chiyani mukutero?
Yehova akufuna kuti anthu azigwiritsa ntchito dzina lake. Werengani Aroma 10:13, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:
Kodi kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu lakuti Yehova n’kofunika bwanji?
Kodi inuyo mumamva bwanji munthu wina akakumbukira dzina lanu n’kulitchula?
Ndiye mukuganiza kuti Yehova amamva bwanji mukamagwiritsa ntchito dzina lake?
5. Yehova akufuna kuti inuyo mukhale mnzake
Mayi wina wa ku Cambodia dzina lake Soten ananena kuti palibe “chinthu chosangalatsa kwambiri” ngati kudziwa dzina la Mulungu. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:
Muvidiyoyi, kodi Soten anamva bwanji atadziwa dzina la Mulungu?
Munthu asanakhale mnzathu timayamba tadziwa kaye dzina lake. Werengani Yakobo 4:8a, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:
Kodi Yehova akufuna kuti inuyo muchite chiyani?
Kodi kudziwa dzina la Mulungu ndiponso kuligwiritsira ntchito kungakuthandizeni bwanji kuti muzimuona kuti ndi mnzanu?
ANTHU ENA AMANENA KUTI: “Mulungu alipo mmodzi yekha, ndiye zilibe kanthu kuti ukumutchula pogwiritsa ntchito dzina liti.”
Kodi inuyo mumakhulupirira kuti dzina la Mulungu ndi Yehova?
Kodi mukudziwa bwanji kuti Mulungu akufuna kuti tizigwiritsa ntchito dzina lake?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Dzina la Mulungu woona ndi Yehova. Iye amafuna kuti tidziwe dzinali ndiponso tiziligwiritsira ntchito n’cholinga choti akhale mnzathu.
Kubwereza
Kodi Yehova amasiyana bwanji ndi milungu ina yonse imene anthu amalambira?
N’chifukwa chiyani tiyenera kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu?
N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova amafuna kuti inuyo mukhale mnzake?
ONANI ZINANSO
Onani zifukwa 5 zotsimikizira kuti Mulungu alipo.
N’chifukwa chiyani ndi zomveka kukhulupirira kuti Mulungu wakhala alipo kuyambira kalekale?
“Kodi Ndani Analenga Mulungu?” (Nsanja ya Olonda, August 1, 2014)
Onani chifukwa chake tiyenera kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu, ngakhale kuti sitikudziwa mmene ankalitchulira kalekale.
Kodi kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu n’kofunika bwanji? Onani chifukwa chake tinganene kuti dzina lake lenileni ndi limodzi lokha.
“Kodi Mulungu Ali Ndi Mayina Angati?” (Nkhani yapawebusaiti)
a Kuti mumve zambiri pa nkhani ya tanthauzo la dzina la Mulungu komanso chifukwa chake anthu analichotsa m’Mabaibulo ena, onani Zakumapeto A4 mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika.