Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi pa Yobu 1:8 tiyenera kumvapo kuti m’nyengo imene Yobu anakhala ndi moyo, anali munthu yekha wokhulupirika kwa Yehova?
Ayi. Lingaliro limenelo silikulungamitsidwa ndi Yobu 1:8, amene amati:
“Ndipo Yehova anati kwa Satana, Kodi wawonerera mtumiki wanga Yobu? Pakuti palibe wina wonga iye m’dzikomo, munthu wangwiro ndi wowongoka, wakuwopa Mulungu ndi kupeŵa zoipa.” Mulungu anapereka malongosoledwe ofananawo pa Yobu 2:3, akumafunsa Satana kuti: “Kodi wawonerera mtumiki wanga Yobu? Pakuti palibe wina wonga iye m’dzikomo, munthu wangwiro ndi wowongoka, wakuwopa Mulungu, ndi kupeŵa zoipa.”
Bukhu la Yobu lenilenilo limasonyeza kuti Yobu sanali munthu yekha wamoyo amene Mulungu anavomereza monga wokhulupirika. Kuyambira Yobu m’chaputala 32, timaŵerenga za Elihu. Ngakhale kuti anali mnyamata, Elihu anawongolera kawonedwe ka zinthu kolakwa ka Yobu nalemekeza Mulungu wowona.—Yobu 32:6–33:6, 31-33; Yobu 35:1–36:2.
Ndiponso, mawu a Mulunguwo akuti ‘panalibe wina wonga Yobu m’dzikomo’ ayenera kutanthauza kuti Yobu kwakukulukulu anali wapadera monga munthu wolungama. Mwachiwonekere Yobu anakhalako m’nyengo yapakati pa imfa ya Yosefe m’Igupto ndi kuyamba kwa utumiki wa Mose monga mneneri wa Mulungu. M’nyengoyo namtindi wa Aisrayeli anali kukhala m’Igupto. Palibe chifukwa cholingalirira kuti onsewo anali osakhulupirika ndi osavomerezeka kwa Mulungu; mwinamwake panali ambiri amene anakhulupirira Yehova. (Eksodo 2:1-10; Ahebri 11:23) Komabe, palibe aliyense wa iwo amene anachita mbali yaikulu, yofanana ndi ya Yosefe, ndiponso olambira amenewo sanali apadera ponena za kulambira kowona, monga momwe Mose anakhalira potsogoza mtundu wa Israyeli kutuluka mu Igupto.
Komabe, kumalo ena kunali mwamuna waumphumphu wapadera. “Panali munthu m’dziko la Uzi, dzina lake ndiye Yobu; ndipo munthuyu anali wangwiro ndi wowongoka, wakuwopa Mulungu ndi kupeŵa zoipa.”—Yobu 1:1.
Chotero Yehova anakhoza kutchula Yobu monga chitsanzo chachiwonekere kapena chodziŵika bwino cha chikhulupiriro ndi kudzipereka. Mofananamo, olemba Baibulo Ezekieli ndi Yakobo polankhula za kale anasankha Yobu kukhala wopereka chitsanzo cha chilungamo ndi chipiriro.—Ezekieli 14:14; Yakobo 5:11.