Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mapeto Akudzawo a “Buku la Nkhondo za Yehova”
    Nsanja ya Olonda—1990 | July 1
    • 12. Kodi Melikizedeke anachitira chithunzi Nduna yaikulu iti ya Mulungu Wamkulukulu, ndipo kodi ndi salmo liti lolembedwa ndi Davide limene lalunjikitsidwa kwa ameneyu kukhala wansembe ndi munthu wankhondo?

      12 Pamene Abrahamu anagonjetsa Kedorelaomere ndi mafumu ake ogwirizana nawo, Melikizedeke anamdalitsa. Melikizedeke Mfumu ndi Wansembe mwaulosi anachitira chithunzi Yemwe akakhala Wansembe Wamkulu wa Mulungu Wamkulukulu ndiponso munthu wankhondo wamphamvu wochilikizidwa ndi Mulungu Wamkulu. Salmo 110, lolembedwa ndi Davide mfumu yankhondo pansi pa kuuziridwa, lalembedwera kwa wamkulu koposa Melikizedeke wa ku Salemu Ameneyu pamene limati: ‘Yehova adzatumiza ndodo ya mphamvu yanu kuchokera ku Ziyoni; Chitani ufumu pakati pa adani anu. Yehova walamulira, ndipo sadzasintha, Inu ndinu wansembe kosatha monga mwa chilongosoko cha Melikizedeke. Yehova pa dzanja lamanja lako adzaphwanya mafumu tsiku la mkwiyo wake.’​—Salmo 110:2, 4, 5.

      13. Mu Ahebri mitu 7 ndi 8, kodi Amene ali wamkulu kuposa Melikizedeke wakale wazindikiritsidwa kukhala yani, ndipo ndi mmalo okwezeka otani omwe Ameneyu anakalowa ndipo ndi nsembe ya mtundu wotani?

      13 Mlembi wouziridwa wa bukhu la Ahebri anavumbula chizindikiro cha Ameneyu kwa amene mawu amenewo analembedweradi pamene anati: ‘Mmene Yesu mtsogoleri analowamo chifukwa cha ife, atakhala mkulu wa ansembe nthaŵi yosatha monga mwa dongosolo la Melikizedeke.’ (Ahebri 6:20) M’mutu wotsatira wa Ahebri, ukulu wa Melikizedeke wakale walongosoledwa. Komabe, ukulu wake wansembe wapambanidwa ndi Yemwe anamuchitira chithunzi, Yesu Kristu wolemekezedwa, woukitsidwa, amene anakafika pamaso poyera pa Yehova Mulungu iyemwini ndi mtengo wa nsembe yoposadi chirichonse chimene Melikizedeke Mfumu ndi Wansembe wa ku Salemu anapereka.​—Ahebri 7:1–8:2.

  • Mapeto Akudzawo a “Buku la Nkhondo za Yehova”
    Nsanja ya Olonda—1990 | July 1
    • 17. Kodi Yehova adzatumiza yani kukamenyera m’dzina lake, ndipo chotero kodi adzaisonyezanji mitundu yonse ya lerolino?

      17 Panthaŵi yake, Yehova Mulungu adzatumiza Yesu Kristu, Melikizedeke Wamkulu, monga munthu wankhondo wamphamvu. Kupyolera mwa iye, Yehova adzadzitengera mbiri yoposa iriyonse ya kumbuyoko yofotokozedwa m’bukhu la Nkhondo za Yehova kapena m’Malemba Achihebri a Baibulo Loyera. M’mutu womalizira wa bukhu lachiŵiri ku lomalizira la Malemba Achihebri, kuwukira kwa mitundu yonse kolimbana ndi Yerusalemu kunanenedweratu. Kenaka, mogwirizana ndi Zekariya 14:3, ‘Yehova adzatuluka, nadzachita nkhondo ndi amitundu aja, monga anachitira nkhondo tsiku lakudumana.’ Mwanjirayi Mulungu wa Baibulo adzasonyeza mitundu yonse yamakono kuti iye adakali Mulungu wankhondo monga momwe analiri m’masiku a Israyeli wakale.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena