-
Tingatani Kuti Mulungu Azitiona Kuti Ndife Oyera?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
2. Kodi ndi makhalidwe ati amene tiyenera kupewa kuti tikhale oyera?
Baibulo limatilimbikitsa kuti “tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi ndi mzimu.” (2 Akorinto 7:1) Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kupewa chilichonse chimene chingaipitse thupi kapena maganizo athu. Zimene timaganiza ziyenera kusangalatsa Yehova. Choncho tiyenera kuyesetsa kupewa kuganiza zinthu zoipa. (Salimo 104:34) Tiyeneranso kuyesetsa kuti zolankhula zathu zizikhala zabwino.—Werengani Akolose 3:8.
Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene zingachititse kuti tisakhale oyera mwakuthupi komanso mwa makhalidwe? Pali zinthu zina zomwe zikhoza kuwononga thupi lathu. Choncho timapewa zinthu monga kusuta fodya, kusuta chamba, kutafuna mtedza wotchedwa betel, kutafuna masamba enaake otchedwa coca, kugwiritsa ntchito mankhwala oletsedwa komanso kugwiritsa ntchito mankhwala molakwika. Tikamapewa zinthu zimenezi timakhala anthu athanzi komanso timasonyeza kuti timalemekeza mphatso ya moyo. Tiyeneranso kuyesetsa kukhala oyera mwa makhalidwe popewa makhalidwe amene angachititse kuti tisakhale oyera monga, kudziseweretsa maliseche ndi kuonera zolaula. (Salimo 119:37; Aefeso 5:5) Si zophweka kusiya makhalidwe ngati amenewa komabe Yehova angatithandize kuti tiwasiye.—Werengani Yesaya 41:13.
-
-
Tingatani Kuti Mulungu Azitiona Kuti Ndife Oyera?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
5. Yesetsani kuti musiye kuganizira komanso kuchita zinthu zoipa
Werengani Akolose 3:5, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi tikudziwa bwanji kuti kuonera zolaula, kutumizira ena mauthenga kapena zinthu zina zolaula komanso kudziseweretsa maliseche Yehova amaona kuti ndi makhalidwe amene amadetsa munthu?
Kodi mukuganiza kuti n’zomveka kuti Yehova aziyembekezera kuti tizikhala ndi makhalidwe oyera? N’chifukwa chiyani mukutero?
Onani zimene mungachite kuti musamaganizire zinthu zoipa. Onerani VIDIYO.
Yesu anagwiritsa ntchito fanizo lomwe limasonyeza kuti tiyenera kuchita zonse zomwe tingathe kuti tikhalebe oyera. Werengani Mateyu 5:29, 30, kenako mukambirane funso ili:
Palembali Yesu sankanena kuti tiyenera kudzivulaza koma ankatanthauza kuti tiyenera kuchita zonse zomwe tingathe kuti tizichita zimene Mulungu amafuna. Kodi n’chiyani chimene munthu ayenera kuchita kuti asamaganizire zinthu zoipa?b
Yehova amayamikira kwambiri mukamayesetsa kuchita khama kuti musiye kuganizira zoipa. Werengani Salimo 103:13, 14, kenako mukambirane funso ili:
Ngati mukuyesetsa kulimbana ndi khalidwe linalake loipa, kodi lembali lingakuthandizeni bwanji kuti musafooke?
Musataye mtima
Zimakhala zosavuta kuganiza kuti, ‘Popeza ndachitanso khalidwe loipali, basi sindingakwanitse kulisiya.’ Koma taganizirani mfundo iyi: Munthu amene ali pampikisano wothamanga akapunthwa n’kugwa, sizitanthauza kuti sangapambane mpikisanowo. Sizitanthauzanso kuti akuyenera kubwerera n’kukayambiranso kuthamangako. N’zimene zingachitike ngati mwayambiranso kuchita khalidwe linalake loipa. Mukalephera ulendo umodzi wokha, sizitanthauza kuti mwalephera kulimbana ndi khalidwelo. Sizitanthauzanso kuti khama lonse limene munachita lija langopita pachabe. Zimachitika ndithu kuyambiranso khalidwe linalake loipa. Koma zikatero, musamataye mtima chifukwa sizitanthauza kuti ndinu wolephera. Yehova akhoza kukuthandizani kuti musiye khalidwe loipalo.
-