Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 9/1 tsamba 32
  • Nyali Yokutsogolerani Panjira ya Moyo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nyali Yokutsogolerani Panjira ya Moyo
  • Nsanja ya Olonda—1997
Nsanja ya Olonda—1997
w97 9/1 tsamba 32

Nyali Yokutsogolerani Panjira ya Moyo

“INU Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Mwa mawu amenewo mneneri Yeremiya anasonyeza kuti anthu sangayende bwino panjira ya moyo popanda chithandizo. Kodi chithandizo chimenecho chingapezeke kuti? Wamasalmo akuyankha mwa pemphero lake kwa Yehova Mulungu kuti: “Mawu anu ndiwo nyali ya kumapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.”​—Salmo 119:105.

Amene amaphunzira Mawu a Mulungu, Baibulo Loyera, ndi kugwiritsira ntchito zomwe limanena adzakhala ngati munthu amene wayamba ulendo m’mamaŵa. Poyamba, samatha kuona zambiri chifukwa kudakali mdima. Koma pamene dzuŵa liyamba kukwera, amaona zambiri. Potsirizira, dzuŵa limaŵala mwachindunji pamutu. Zonse amangoziona bwinobwino. Fanizo limenelo likutikumbutsa mwambi wa Baibulo wakuti: “Mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbanda kucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbe.”​—Miyambo 4:18.

Bwanji za aja amene amakana chitsogozo cha Mulungu? Baibulo limati: “Njira ya oipa ikunga mdima; sadziŵa chimene chiwapunthwitsa.” (Miyambo 4:19) Inde, oipa ali ngati munthu womapunthwa mumdima. Ngakhale amaoneka ngati zinthu zikuwayendera bwino, koma nzakanthaŵi chabe, pakuti “Kulibe nzeru ngakhale luntha ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.”​—Miyambo 21:30.

Chotero, tsatirani chitsogozo cha Mawu a Mulungu, Baibulo. Mutatero, mudzaona kuti mawu a Miyambo 3:5, 6 ngoona, akuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena