Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 4/8 tsamba 16-17
  • Kukongozana Ndalama ndi Mabwenzi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukongozana Ndalama ndi Mabwenzi
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mfundo Zoyenera Kuzilingalira
  • Wokongoza
  • Kodi Ndibwerekedi Ndalama?
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Kodi Ndipemphe Ngongole kwa Mbale?
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Kubwereketsa Ndalama kwa Akristu Anzathu
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Kuloŵa m’Ngongole Kumathandiza?
    Galamukani!—1995
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 4/8 tsamba 16-17

Lingaliro la Baibulo

Kukongozana Ndalama ndi Mabwenzi

“WOIPA AKONGOLA, WOSABWEZA: KOMA WOLUNGAMA ACHITIRA CHIFUNDO, NAPEREKA.”​—SALMO 37:⁠21.

WILLIAM Shakespeare, wolemba ndakatulo wa ku England, analemba kuti: “Usakongole ndalama, ndipo usakongoze; chifukwa nthaŵi zambiri ngongoleyo siibwera ndipo imasokoneza ubwenzi.” Pamene anatero, anali kubwereza mwambi wina wanzeru wakale kwambiri. N’zoona kuti nthaŵi zambiri chimene chimadanitsa anthu ndicho kukongozana ndalama. Ngakhale ngati munali mutalinganiza zinthu bwino kapena kuti munali ndi zolinga zabwino motani, zinthu siziyenda bwino nthaŵi zonse.​—⁠Mlaliki 9:​11, 12.

Mikhalidwe ingasinthe moti ingachititse wokongola ndalamayo kulephera kubweza kapenanso kumulepheretsa kukwanitsa pangano lake. Kapena wokongozayo angazifune mwadzidzidzi ndalama zomwe wakongoza zija. Pamene zoterezi zichitika, monga mmene Shakespeare ananenera, ubwenzi ndi maunansi angawonongeke.

N’zoona kuti munthu angakhale ndi chifukwa chomveka chokongolera ndalama. Atasoŵeratu ndalama mwina chifukwa choti anachita ngozi yaikulu kapena chifukwa choti anachotsedwa ntchito, angaone ngati kuti chimene angachite ndicho kuloŵa m’ngongole. Baibulo limalimbikitsa kuti ngati pali ena amene angathandize anzawo osoŵa ayenera kumawathandizadi ngati angathe. (Miyambo 3:27) Zimenezo zingatanthauzenso kukongozana ndalama. Komabe, kodi Akristu amene akongozana ndalama ayenera kumaiona bwanji ngongole yawo?

Mfundo Zoyenera Kuzilingalira

Baibulo si buku lolangiza pankhani zandalama. Silifotokoza njira zonse zokhudza kukongola ndalama kapena kukongoza. Zoti wokongolayo adzaikepo chiwongoladzanja kapena ayi, zimenezo ndi za anthu aŵiriwo.a Komabe, zimene Baibulo limapereka ndizo mfundo zomveka, zachikondi, zomwe ziyenera kuthandiza aliyense amene akufuna kukongoza kapena kukongola ndalama.

Talingalirani mfundo zimene zingagwire ntchito kwa wokongola. Mtumwi Paulo analangiza Akristu kuti ‘asakhale ndi mangawa ndi munthu aliyense, koma kukondana ndiko.’ (Aroma 13:⁠8) Ngakhale kuti Paulo anali kunena za mfundo imene ingagwire ntchito pankhani zambiri, uphungu wake tingautenge monga chenjezo loti tisaloŵe m’ngongole. Nthaŵi zina kuli bwino kukhala wopanda ndalama m’malo mokhala ndi mangawa ndi munthu wina. Chifukwa? Miyambo 22:7 imafotokoza kuti “wokongola ndiye kapolo wa wom’kongoletsa.” Wokongola ndalamayo ayenera kumazindikira kuti mangawa ake sadzatha kufikira atabweza ngongoleyo. Mwa mawu ena, ndalama zonse zimene ali nazo si zake ayi. Nthaŵi zonse ayenera kuganizira kwambiri zobweza ngongole yakeyo malinga ndi mmene anagwirizanira ndi wokongozayo, kupanda kutero angautse mikangano.

Mwachitsanzo, patati papita nthaŵi wokongolayo asanabweze, wokongozayo angakhumudwe. Zinthu zimene wokongola ndalamayo azichita, monga kugula zovala, kukadya kulesitilanti, kapena kupita kutchuthi, zingam’pangitse wokongozayo kuyamba kukayikira. Chidani chingayambike. Aŵiriwo angadane ndithu ndiponso mwina ndi mabanja awo omwe angakanganenso. Pamachitika zomvetsa chisoni zonga zimenezi ngati wokongola ndalamayo sasunga pangano.​—⁠Mateyu 5:⁠37.

Koma bwanji ngati wokongola ndalamayo walephera kusunga lonjezo lake chifukwa cha zochitika zimene iye sanakachitira mwina? Kodi zitatero ndiye kuti ngongoleyo ithera pompo? Kutha kwake sikukhala koteroko. Wamasalmo anati munthu wolungama “atalumbira kwa tsoka lake, sasintha ayi.” (Salmo 15:⁠4) Nkhani yake itakhala choncho, chinthu chachikondi ndi chanzeru chingakhale chakuti wokongola ndalamayo akam’fotokozere nthaŵi yomweyo wokongozayo mmene zinthu zilili. Ndiyeno mwina angagwirizanenso mwanjira ina. Atatero adzasungitsa mtendere, ndipo adzakondweretsa Yehova Mulungu.​—⁠Salmo 133:1; 2 Akorinto 13:⁠11.

Kunena zoona, munthu amadzisonyeza yekha za mmene alili mwa njira imene amachitira ndi ngongole zake. Ngati munthu amachita mphwayi, kungoiwaliratu zoti ali ndi ngongole, zimasonyeza kuti salingalira za anzake. Ndiponso, munthu wamaganizo oterowo n’ngodzikonda​—⁠amangoganizira kupeza zofuna iye choyamba. (Afilipi 2:⁠4) Mkristu amene amakana dala kubweza ngongole yake akudzipangitsa yekha kudedwa ndi Mulungu, ndipo zochita zake zimasonyeza kuti ndi waumbombo, ali ndi mtima woipa.​—⁠Salmo 37:⁠21.

Wokongoza

Ngakhale kuti mlandu waukulu umakhala ndi wokongolayo, palinso mfundo zina zogwira ntchito kwa wokongozayo. Baibulo limanena kuti ngati tingathe kuthandiza osauka, tiyenera kuwathandiza. (Yakobo 2:​14-16) Koma zimenezo sizikutanthauza kuti munthu akakamizike kukongoza ndalama chifukwa choti munthu yemwe akupempha ngongoleyo ndi mbale wake wauzimu. Baibulo limati: “Wochenjera aona zoipa, nabisala.”​—⁠Miyambo 22:⁠3.

Munthu wozindikira, wodziŵa bwino mavuto amene amabuka pankhani yokongoza ndi kukongola ndalama, adzaganiza bwino kwambiri asanakongoze aliyense ndalama zomwe akufuna. Kodi pempho lake n’lomveka? Kodi munthu amene akupempha ngongoleyo walingalira bwino nkhaniyi? Kodi munthu wofuna kukongola ndalamayo amachita zinthu molongosoka ndipo kodi ali ndi mbiri yabwino? Kodi akuvomereza kulemba dzina lake papepala limene mwalembapo mfundo za pangano lanu? (Yerekezerani ndi Yeremiya 32:​8-​14.) Kodi watsimikizadi kuti adzabweza?

Izi sizikutanthauza kuti Mkristu ayenera kukana kuthandiza wina wofuna thandizo yemwe akuoneka kuti adzalephera kubweza ngongole. Zinthu zabwino zimene Mkristu angachitire ena si zabizinesi zokhazokha ayi. Mtumwi Yohane anafunsa kuti: “Iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosoŵa ndi kutsekereza chifundo chake pom’mana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji?” Inde, Akristu ayenera ‘kukondana m’choonadi, osati ndi mawu kapena ndi lilime.’​—⁠1 Yohane 3:​17, 18.

Nthaŵi zina munthu angaganize zoti asakongoze ndalama mbale wake wosoŵa. Mwina angafune kungom’patsa mphatso kapena kum’thandiza mwa njira ina. Mofananamo, ngati pabuka mavuto ena, pamene anthu akongozana ndalama, wokongozayo mwina angam’chitire mnzakeyo chifundo. Poti mikhalidwe ya wokongolayo yasintha, mwina wokongozayo angafune kum’chitira chifundo ndi kum’patsa nthaŵi yaitali yobwezera ngongoleyo, mwina angachepetse ngongoleyo, kapena kungom’khululukira mangawa ake. Zimenezi n’zinthu zimene munthu aliyense angachite mongofuna yekha.

Akristu ayenera kumakumbukirabe kuti Mulungu amaona zonse ndipo adzatiimba mlandu wa khalidwe lathu ndiponso wa mmene timachitira ndi ndalama zathu. (Ahebri 4:​13) N’zoona kuti uphungu wa Baibulo wakuti “zanu zonse zichitike m’chikondi” umagwiranso ntchito pankhani yokongozana ndalama ndi mabwenzi.​—⁠1 Akorinto 16:⁠14.

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mudziŵe zambiri pankhani yolandira chiwongoladzanja pangongole, onani Nsanja ya Olonda ya October 15, 1991, masamba 25-8.

[Chithunzi patsamba 16]

“Munthu Wosinthitsa Ndalama ndi Mkazi Wake” (1514), chojambulidwa ndi Quentin Massys

[Mawu a Chithunzi]

Scala/Art Resource, NY

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena