Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Helo Ndimalo Amtundu Wotani?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
    • 6. (a) Kodi ndimotani mmene Baibulo limasonyezera kuti Sheol ndi Hade zimatanthauza chinthu chimodzi? (b) Kodi nchiyani chimene chikusonyezedwa ndi chenicheni chakuti Yesu anali m’Hade?

      6 Tisanayankhe funso limeneli, tiyeni timveketse kuti liwu Lachihebrilo Sheol ndi liwu Lachigirikilo Hade limatanthauza chinthu chimodzimodzicho. Zimenezi zikusonyezedwa mwa kuyang’ana pa Salmo 16:10 m’Malemba Achihebri ndi Machitidwe 2:31 m’Malemba Achikristu Achigiriki, mavesi amene mungawaone pa tsamba linalo. Wonani kuti m’kugwira mawu kuchokera m’Salmo 16:10 m’mene Sheol amapezeka, Machitidwe 2:31 amagwiritsira ntchito Hade. Wonaninso, kuti, Yesu Kristu anali m’Hade, kapena helo. Kodi tiyenera kukhulupirira kuti Mulungu anazunza Kristu m’helo wa moto? Ndithudi ayi! Yesu anali chabe m’manda mwake.

  • Kodi Helo Ndimalo Amtundu Wotani?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
    • [Bokosi patsamba 83]

      Liwu Lachihebrilo “Sheol” ndi liwu Lachigirikilo “Hade amatanthauza chinthu chimodzi

      American Standard Version

      Salmo 16:10

      10 Pakuti simudzasiya moyo wanga ku

      Shēʹōl;

      Ndiponso simudzalola

      woyera wanu awone chivundi.

      Machitidwe 2:31

      31 Iye powoneratu zimenezi analankhula za chiukiriro cha Kristu, kuti iye sanasiyidwe m’Hade, ngakhale thupi lake kuwona chivundi.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena