Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 4/8 tsamba 18-20
  • N’chifukwa Chiyani Sindikutha Kupeza Zinthu Zimene Ndimafuna?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • N’chifukwa Chiyani Sindikutha Kupeza Zinthu Zimene Ndimafuna?
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuona Zinthu Zakuthupi Moyenera
  • Pamene Mukufunadi Chinachake
  • Phunzirani Kukhutiritsidwa
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndizipeza Ndalama?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Zovala Zolembedwa Dzina la Ozipanga Kodi Nzanga?
    Galamukani!—1992
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndizisamala Ndalama?
    Galamukani!—2006
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndidziwane Bwino Ndi Makolo Anga?
    Galamukani!—2009
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 4/8 tsamba 18-20

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

N’chifukwa Chiyani Sindikutha Kupeza Zinthu Zimene Ndimafuna?

“Pali zinthu zina zabwinodi; ndipo ndimalakalaka nditakhala nazo, koma makolo anga sangazikwanitse.”—Mike.

KODI pali zinthu zimene mumafunadi koma simungazipeze? Mwina mukufunitsitsa mutapeza wailesi yapamwamba yatsopano ija, nsapato zimene achinyamata onse akuvala zija, kapena kokha jinzi yatsopano yokhala ndi chidindo cha woipanga. Anzanu ena ali nazo zinthu zimenezi—ndiponso amazionetsa monyadira. Choncho ngati mwauzidwa kuti makolo anu sangazikwanitse, mungakhumudwe.

Ngakhale kuli koyenera kufuna zinthu zinazake, achinyamata ambiri amafikira podzazidwa maganizo ndi chikhumbo chimenechi. Nthaŵi zambiri zimenezi zimachitika chifukwa cha zofalitsa nkhani zokopa. Kunenerera malonda kokopa pa TV, m’magazini, ndi pawailesi kumachititsa munthu kuganiza kuti ukapanda kuvala zovala zina zake kapena kugwiritsa ntchito zinthu zokhala ndi mayina ena ake, ndiwe munthu wolephera kotheratu. Inde, achinyamata amawononga ndalama zokwanira madola 100 biliyoni pachaka ku United States kokha!

Ndiye pali chisonkhezero chochokera kwa anzanu. “Pamoyo wongokhulupirira zilizonse wa achinyamata,” ikutero nkhani yolembedwa m’magazini ya Marketing Tools, “kuonedwa monga wotsalira ndi gulu limene umafuna kukhalamo sikumasonyeza chabe kuti sungakwanitse, kapenanso kuti anzako sakukufuna: komanso ndi chizindikiro cha Wolephera.” Ndi motani m’mene ungakhalire “wotsogola”? Ambiri amati mwa kukhala ndi zinthu zabwino kwambiri ndiponso zatsopano. Nanga ngati sungazikwanitse? “N’zosautsadi kwambiri,” akuvomereza mnyamata wina wachikristu. “Wapita kusukulu utavala zovala zosatchuka, ndiye aliyense akukuseka.” Mtsikana wina akuvomereza motere, “Nthaŵi zina ndimaona kuti anzanga sakundifuna.”

Achinyamata amene amakhala m’mayiko amene adakatukuka, kumene anthu amavutika kwa maola ambiri kuti angopeza zofunika pa moyo angapezenso mavuto ngati amenewa. Ngati banja lanu lili lotere, mwachibadwa mungafune moyo wabwinopo. Mutaonera makanena a pa TV ndi mafilimu a ku mayiko olemera, inunso mungakhale mutayamba kukhumba zovala zamtengo wapatalizo, nyumba, ndi galimoto zosonyezedwa m’makanema ndi mafilimuwo. Chifukwa chakuti zinthu zimenezi zingaoneke kukhala zovuta kwambiri kuzipeza, mungaipidwe kapenanso kupsinjika maganizo.

Kaya mumakhala m’dziko losauka kapena lolemera, kukhala wokwiya kapena wokhumudwa chifukwa chakuti simungapeze zinthu zina zake kungangokuvulazani. Kungachititsenso kukangana pafupipafupi ndi makolo anu. Funso ndi lakuti, Kodi mungathane nazo bwanji?

Kuona Zinthu Zakuthupi Moyenera

Choyamba zindikirani kuti sichikhumbo cha Yehova Mulungu kuti anthu ake akhale osauka kapena kuti akhale opanda zinthu zimene zili zofunikadi. Ndiponsotu, Mulungu sanaike Adamu ndi Hava kumalo otayako zinyalala, koma m’munda wokongola wodzaza ndi mitengo yokoma m’maso. (Genesis 2:9) Pambuyo pake, atumiki ena a Mulungu monga Abrahamu, Yobu, ndi Solomo, anali ndi chuma chambiri. (Genesis 13:2; Yobu 1:3) Inde, Solomo anali ndi golide wochuluka kwambiri kotero kuti siliva “anangoyesedwa opanda pake” m’nthaŵi ya ulamuliro wake!—1 Mafumu 10:21, 23.

Komabe, nthaŵi zambiri anthu a Mulungu ambiri akhala opeza mochepera. Yesu Kristu weniweniyo anali wosauka; analibe ngakhale “potsamira mutu wake.” (Mateyu 8:20) Ngakhalebe zinali choncho, simunaŵerengepo kuti Yesu anadandaula kuti ankalephera kugula zinthu zimene ankafuna. M’malo mwake iye anaphunzitsa kuti: “Musadere nkhaŵa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? kapena, Tidzamwa chiyani? kapena, Tidzavala chiyani? . . . Pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziŵa kuti musoŵa zonse zimenezo. Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.”—Mateyu 6:31-33.

Zimenezi sizikutanthauza kuti Mulungu ayenera kukwaniritsa chikhumbo cha munthu winawake cha zovala zotchuka kapena zipangizo zinazake zamagetsi. Mulungu amatipatsa zinthu zimene timasowa—osati kwenikweni zimene timazilakalaka. N’chifukwa chake Baibulo limatilimbikitsa kukhala wokhutira ndi “zakudya ndi zofunda” basi. (1 Timoteo 6:8) Koma tiyeni tinene zoona, kukhala wokhutira sikwapafupi ayi. “Nthaŵi zonse uyenera kumasiyanitsa pakati pa zimene umalakalaka ndi zimene umasowa,” akuvomereza wachinyamata wina wotchedwa Mike. Kuphatikiza pa zilakolako zathu, tiyeneranso kulimbana ndi chisonkhezero cha mdani wamkulu wa Mulungu, Satana Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19) Ndipo umodzi wa misampha yake yakale kwambiri ndiwo kuchititsa anthu kumva ngati kuti akuphonya chinachake. Motero Hava ananyengedwa kukhulupirira kuti anali kumanidwa kanthu kena—ngakhale kuti ankakhala m’paradaiso wangwiro!—Genesis 3:2-6.

Kodi mungapeŵe bwanji kugwera m’mbuna ya kusakhutira? Zingamveke ngati zongokambapo chabe, koma pali zifukwa zambiri zimene muyenera kuganizira za zinthu zabwino zomwe muli nazo. Osatitimira m’maganizo ovulaza a zinthu zimene mulibe. Ganizani mwanzeru ndipo kumbukirani zinthu zimene muli nazo. (Yerekezerani Afilipi 4:8.) Mike akunena zomwezi motere: “Pali zinthu zambiri zimene ndimazilakalakadi koma sindimaziika kumtima.”

Zimathandizanso kukhala wochenjera ndi malonda achinyengo amene amasokoneza malingaliro anu.a (Miyambo 14:15) Musanafulumire kunena kuti simungathe kukhala wopanda nsapato zatsopano zija kapena wailesi yapamwamba ya ma disc ija, yesetsani kuganiza modekha. Dzifunseni nokha kuti: ‘Kodi chinthu ichi n’chofunikiradi? Kodi chili ndi ntchito yeniyeni? Kapena zimene ndili nazo kale n’zokwanira?’ Samalani ndi zilengezo za malonda zimene zimalimbikitsa kuti mudzakhala wapamwamba mukagula zinthu zinazake. Mawu a mtumwi Yohane opezeka pa 1 Yohane 2:16 ndi amphamvu: “Chilichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi.”

Pamene Mukufunadi Chinachake

Nanga bwanji ngati palidi chinachake chimene mukuchifunadi pa zifukwa zabwino? Musanawauze makolo anu ganizani kaye panokha. Khalani wokonzeka kufotokoza chifukwa chimene mukufunira chinthucho, m’mene mudzachigwiritsire ntchito, ndi m’mene mukuonera kuti chingadzakhalire chaphindu kwa inu. Mwina makolo anu angapeze njira yochiikira pa bajeti ya pa banjapo. Koma nanga bwanji ngati pakali pano sangathe? Simungachitire mwina koma kudikira. (Mlaliki 7:8) Zino ndi “nthaŵi zoŵaŵitsa,” ndipo makolo ambiri sangakwanitse zinthu zonse zimene ana awo angapemphe. (2 Timoteo 3:1) Ngati mutapeŵa kupempha zinthu zopanda ntchito kwenikweni kwa makolo anu, mungapangitse ntchito yawo yovuta kukhala yofeŵerapo.

Komabe, mwina mungachitepo kanthu. Mwachitsanzo, kodi mumalandira ndalama zongokuthandizirani? Ndiye phunzirani kupanga bajeti ndi ndalama zanuzo mwanzeru kuti muzitha kusungapo zina mwezi uliwonse. Mungathe kutsegula buku ku banki yomwe muli nayo pafupi. (Yerekezerani ndi Luka 19:23.) N’zimene mtsikana wotchedwa Abigail anachita. Akunena kuti: “Ndimaika ndalama zanga m’miyulu iŵiri—umodzi ndi wa ku buku langa la ku banki ndipo winawo ndi wogwiritsa ntchito.” Ngati muli wosinkhukirapo, mungathe kuchita ganyu kapena kupeza ntchito ya maola ochepa.b Mulimonse, ngati makolo anu aona kuti mukufunadi kugula chinachake ndipo mwalingalira kuti musunge ndalama, angalimbikitsidwe kukuwonjezerani ndalamazo, ngati kuli kotheka.

Kusintha mmene mumagulira zinthu kungakuthandizeninso. Mwachitsanzo ngati chinthu chili pa mtengo wosafikirika, n’zotheka kunenelera kuti muchigule pa mtengo wotsikirapo. Ngati zimenezi zakanika dikirani n’kuyamba mwaona kaye ngati chinthucho chidzatsitsidwe mtengo. Onani m’masitolo ena kuti mudziŵe ngati mungapeze chinthu chomwecho pa mtengo wotsikirapo. Phunzirani kuona zinthu mosamala kuti mudziŵe ngati zili zapamwamba. Nthaŵi zina zinthu zosatchuka zimakhala zabwino kwambiri.c

Phunzirani Kukhutiritsidwa

Miyambo 27:20 amachenjeza kuti: “Kunsi kwa manda ndi kuchiwonongeko sikukhuta; ngakhale maso amunthu sakhuta ayi.” Inde, monga momwe manda alili ndi njala yosakhutitsika, anthu ena amafuna zinthu nthaŵi zonse—ngakhale atakhala kale ndi zina zochuluka bwanji. Pewani kuganiza koteroku. Pamapeto pake umbombo sumapindulitsa m’njira iliyonse koma umangogwiritsa mwala ndi kubweretsa chisoni. Wachinyamata wina wotchedwa Jonathan akuvomereza: “Ngati nthaŵi zonse chimwemwe chanu chimadalira pa kukhala ndi zinthu simudzakhala achimwemwe. Nthaŵi zonse padzapezeka chinachake chatsopano chimene mudzachifuna. Muyenera kuphunzira kukhala wosangalala ndi zimene muli nazo.”

Mukakhala wokhutira mungathe kukhala wosakhudzidwa ndi zimene anzanu akuchita. Wachinyamata wina wotchedwa Vincent akuti: “Sikuti ndikaona winawake ali ndi nsapato zatsopano ndiye kuti inenso ndikagule zanga ayi.” N’zoona kuti kaŵirikaŵiri, zingamakuwawenibe kuti simungathe kukhala ndi zinthu zimene mukufuna. Koma osaiŵala kuti Yehova amadziŵa zimene mumafuna. (Mateyu 6:32) Ndipo posachedwapa, ‘adzakwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo.’—Salmo 145:16.

[Mawu a M’munsi]

a Onani Galamukani! ya September 8, 1998 kuyambira pa nkhani yakuti “Kutengekatengeka ndi Zilengezo za Malonda Zochuluka.”

b Onani nkhani ya “Achinyamata Akufunsa Kuti . . . Ndingatani Kuti Ndizipeza Ndalama?,” m’kope lathu la September 8, 1998.

c Ngati mukufuna kudziŵa njira zambiri zothandiza, onani nkhani ya “Achichepere akufunsa . . . Kodi Ndingapeze Motani Zovala Zoyenera?,” m’kope lathu la February 8, 1995.

[Mawu Otsindika patsamba 19]

“Mukupita kusukulu mutavala zovala zosatchuka, ndipo aliyense akukusekani”

[Chithunzi patsamba 20]

Mungakhalebe wosangalala ngakhale mutapanda kukhala ndi zonse zimene mumafuna

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena