-
Mafunso Ochokera kwa OŵerengaNsanja ya Olonda—1991 | August 1
-
-
Bukhu la Miyambo liri ndi mavesi ambiri amene amaima paokha monga ndemanga zapadera za uphungu, koma Miyambo 27:23 ndimbali ya gulu la mavesi akuti: ‘Udziwitsitse zoweta zako ziri bwanji, Samalira magulu ako. Pakuti chuma sichiri chosatha; Kodi korona alipobe mpaka mibadwo mibadwo? Amatuta maudzu, msipu uoneka, Achera masamba a kumapiri. Ana a nkhosa akuveka, Atonde aombera munda; Mkaka wa mbuzi udzakukwanira kudya; Ndi a pa banja lako ndi adzakazi ako.’—Miyambo 27:23-27.
-
-
Mafunso Ochokera kwa OŵerengaNsanja ya Olonda—1991 | August 1
-
-
Mbusa wogwira ntchito zolimba ndi wosamala adali ndi magwero odalirika a chithandizo—Yehova. Motani? Eya, Mulungu amagaŵira nyengo ndi kuzungulira kwawo zimene mwamasiku onse zimatulukapo nsipu wokwanira kudyetsa nkhosa. (Salmo 145:16) Pamene nsipu uwuma ku malo akuchidikha chifukwa cha kusintha kwa nyengo, ungakhale wochuluka ku malo akumtunda, kumene mbusa watcheru angapititseko nyama zake.
-