-
Mafunso Ochokera kwa OŵerengaNsanja ya Olonda—1991 | August 1
-
-
Bukhu la Miyambo liri ndi mavesi ambiri amene amaima paokha monga ndemanga zapadera za uphungu, koma Miyambo 27:23 ndimbali ya gulu la mavesi akuti: ‘Udziwitsitse zoweta zako ziri bwanji, Samalira magulu ako. Pakuti chuma sichiri chosatha; Kodi korona alipobe mpaka mibadwo mibadwo? Amatuta maudzu, msipu uoneka, Achera masamba a kumapiri. Ana a nkhosa akuveka, Atonde aombera munda; Mkaka wa mbuzi udzakukwanira kudya; Ndi a pa banja lako ndi adzakazi ako.’—Miyambo 27:23-27.
-
-
Mafunso Ochokera kwa OŵerengaNsanja ya Olonda—1991 | August 1
-
-
Miyambo 27:26, 27 imatchula chotulukapo chimodzi cha ntchito yoteroyo—zakudya ndi zovala. Mosakaikira, malongosoledwewo samanena chakudya chokoma chopambanitsa kapena mitundumitundu ya zakudya ndi zakumwa zapadera, ndiponso simapatsa wogwira ntchitoyo chifukwa chakuyembekezera zovala za mafashoni atsopano koposa kapena zovala za nsalu zokongola koposa. Koma ngati anali wofunitsitsa kupanga kuyesayesa, mbusayo ndi banja lake akakhoza kupeza mkaka ku nkhosazo (ndiponso cheese), limodzinso ndi ubweya wosokera zovala zochindikala.
-