-
Dalirani YehovaNsanja ya Olonda—2003 | September 1
-
-
18, 19. Kodi Baibulo likutilimbikitsa kudalira Yehova ndi mawu otani, koma kodi ndi maganizo olakwika ati amene anthu ena amakhala nawo pankhani imeneyi?
18 Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.” (Miyambo 3:5, 6) Ameneŵatu ndi mawu osangalatsa ndiponso olimbikitsa kwambiri. Kunena zoona, palibe aliyense m’chilengedwe chonse amene ali wodalirika kuposa Atate wathu wokondedwa wakumwamba. Komabe, kuŵerenga mawu ameneŵa m’buku la Miyambo n’kosavuta kusiyana ndi kuwatsatira.
-
-
Dalirani YehovaNsanja ya Olonda—2003 | September 1
-
-
22, 23. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kudalira Yehova tikakumana ndi mavuto, ndipo tingachite bwanji zimenezo? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatirayi?
22 Komabe, pa Miyambo 3:6 pakusonyeza kuti tiyenera ‘kulemekeza Yehova m’njira zathu zonse,’ osati pamavuto pokhapokha ayi. Motero, zimene timasankha kuchita tsiku ndi tsiku ziyenera kusonyeza kuti timadalira Yehova. Pakabuka mavuto, sitiyenera kutaya mtima, kugwira njakata, kapena kukana malangizo a Yehova ofotokoza njira yabwino kwambiri yothetsera mavutowo. Tiyenera kuona ziyeso monga mipata yoti tikhalire kumbuyo ulamuliro wa Yehova, kuthandiza kutsimikizira kuti Satana ndi wabodza, ndiponso kukulitsa kumvera ndi makhalidwe ena amene amakondweretsa Yehova.—Ahebri 5:7, 8.
-