Kugula Chimwemwe Popanda Ndalama
MUTAGWIDWA ndi ludzu pambuyo pakuyenda mtunda pansi pa dzuŵa lotentha, inu mwafika pa mudzi waung’ono. Ku chisangalalo chanu inu muwona chizindikiro cholengeza kuti zakumwa zoziziritsa ziripo. Koma kenaka inu muzindikira kuti mulibe ndalama iriyonse ya kulipira kaamba ka zotsitsimulazo.
Akumawona kuvutika kwanu, mwini sitolo anena kuti, ‘Idzani, gulani zakumwa—izo sizidzakuwonongerani ndalama zirizonse.’ Mwamsanga, inu mudzimva woyamikira kwambiri kaamba ka chogawira chachifundochi. Komabe, inu mukufunsa, ‘Kodi zimenezo zingakhale tero motani? Kodi ndimotani mmene ndingagulire popanda ndalama?’
Kugula Popanda Ndalama
Ngakhale kuti ichi chingawoneke kukhala choyerekeza, onse aŵiriwo Karel ndi Julian, otchulidwa pa tsamba 17, anali ndi chokumana nacho choterocho. Iwo anakhulupirira kuti ndalama zikawabweretsera chimwemwe. Koma monga mmene Karel walongosolera: “Phunziro la Baibulo linasintha kawonedwe kanga ka ndalama. Iro linapereka chiyembekezo cha moyo wosatha m’paradaiso pa dziko lapansi, chinthu chinachake chophulapo kanthu kuposa chirichonse chimene ndalama ingagule.” Yemwe kale ankayembekezera kukhala mponda matiki Julian akulongosola kuti: “Ndinali bwino lomwe pa njira yanga ya kufikira chonulirapo changa pamene ndinaphunzira chowonadi kuchokera m’Baibulo.”
Mofananamo, yemwe kale anali kugulitsa m’sitolo Kiyoshi Tomomitsu wa ku Japan ankaika ntchito yake poyamba, pamene kuli kwakuti kusamalira banja lake kunali kokha “chikondwerero chachiŵiri.” Iye analingalira kuti: “Ndinalingalira kuti ndingapange banja langa kukhala lachimwemwe mwa kupereka zinthu zakuthupi zokwanira kaamba ka mtsogolo mwawo.” Pamene anafunsidwa chimene chinasintha kawonedwe kake ka ndalama ndi zinthu zakuthupi, Kiyoshi anayankha kuti: “Malemba kuchokera m’Baibulo, onga ngati Miyambo 23:23, yomwe imati, ‘Gula chowonadi ndipo usachigulitse (NW).’”
‘Koma,’ inu mungafunse, ‘kodi ndimotani mmene “ndingagulire chowonadi”?’
Zowonongedwa za Chimwemwe
Chidzakuwonongerani ina ya nthaŵi yanu. ‘Pezani nthaŵi,’ analangiza tero mtumwi Wachikristu Paulo, ‘popeza kuti masiku ali oipa.’ (Aefeso 5:15-17) Mboni za Yehova zomwe ziri kumalo anu okhala zidzakhala zosangalatsidwa kukonzekera kulankhula ndi inu ponena za chowonadi kuchokera m’Mawu a Mulungu, Baibulo, pa nthaŵi yoyenera kwa inu, ndipo ichi chidzakhala chaulere kotheratu ponena za kulipiritsa ndalama.
Kodi mukudzimva kukhala wosinkhasinkha ‘kuloŵetsedwamo’? Ngati mutero, kenaka mvetsetsani kuchokera ku mawu a Yesu: “Odala ali akumva njala ndi ludzu la chilungamo, chifukwa adzakhuta.” Akumakokera chisamaliro cha omvetsera ake ku zochititsa m’zimene akapezera chimwemwe, Yesu anati: “Odala ali osauka mumzimu, chifukwa uli wawo ufumu wa kumwamba.” (Mateyu 5:3, 6) Boma lakumwamba limeneli, Ufumu wa Mulungu, uli ulamuliro waukulu wokhoza kukupatsani inu “chiphaso chonkira ku chimwemwe.”
Kodi ndi mbali yotani, kenaka, imene ndalama ziyenera kuchita m’moyo wanu? Mosangalatsa, Baibulo limapereka zitsogozo zogwira ntchito pa chimenechi.
Kugwiritsira Ntchito Kwabwino kwa Ndalama Tsopano
“Lemekeza Yehova ndi chuma chako,” amalangiza tero Mawu a Mulungu. (Miyambo 3:9) Mwachiwonekere, awo omwe amayang’ana kwa Mulungu kaamba ka chimwemwe chowona amagwiritsira ntchito ndalama zawo m’njira imene imamkondweretsa iye. Iwo amalinganiza pa kusamalira mokhazikika kaamba ka zosowa zakuthupi za banja lawo. (1 Timoteo 5:8) Iwo amapanga mphatso yowona mtima kaamba ka ena omwe ali oyanjana nawo m’chikhulupiriro. Ndipo amapanganso zopereka zaufulu kuchirikiza ntchito ya kupereka chidziŵitso chomangirira mwauzimu mumkhalidwe wa maBaibulo ndi zofalitsidwa zozikidwa pa Baibulo, zonga ngati magazini ino.
Akudziŵa kuti Ufumu wa Mulungu udzachotsa m’chitaganya cha anthu zinthu zake zakuthupi, mbali za chuma zadyera, iwo amapeŵa kucheutsidwa m’kuika ndalama m’mbali zimene zafikiridwa kale ndi kulephera. (Danieli 2:44) “Pokhala ndi zakudya ndi zofunda,” iwo ali okwaniritsidwa ndi mkhalidwe wa moyo womwe umasamalira kaamba ka zofunika za moyo.—1 Timoteo 6:8.
Chimwemwe Tsopano—Chinthu Chenicheni
“Chimodzi cha zinthu zoyambirira zimene ndinawona pamene ndinakumana ndi Mboni za Yehova,” akusimba tero Sue kuchokera ku England, “chinali mmene awo okhalirira m’malamulo a Baibulo, omwe anali olowetsedwamo kotheratu m’kulambira kwawo, anawonekera kukhala ndi zinthu zomwe anazifuna.” Mwamuna wake, John, anawona chinthu chimodzimodzicho. Iye akulongosola kuti:
“Chiri kokha chifukwa cha kudziŵa chowonadi cha Baibulo ndi pamene ndikhoza kuwona chimene chikuchitika kwa anthu ambiri. Chimene akugwirirapo ntchito chiri chodalira pa ndalama kotheratu. Baibulo linandithandiza ine kuphunzira kuti chimwemwe sichimadza mwa njira imeneyo. Tsopano ndizindikira kuti chimwemwe chiri chipatso chapambali cha kuchita zinthu kaamba ka ena ndikuti sichiri polekezera mwa icho chokha.”
John ndi Sue ali kokha aŵiri pakati pa Mboni za Yehova zoposa mamiliyoni atatu omwe akuchitira umboni ku chowonadi cha lonjezo la Yesu lakuti pamene mufunafuna choyamba Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo chake, zofunika zonse zakuthupi “zidzawonjezereka kwa inu.”—Mateyu 6:33.
Kodi mukufunafuna kaamba ka madzi othetsa ludzu la chowonadi? Kaya muli olemera kapena osauka, chimwemwe chingakhale chanu mwa kulabadira chiitano cha ulosi cha Mulungu: “Inu nonse, inu akumva ludzu, idzani ku madzi; ndi osowa ndalama, idzani inu mugule . . . opanda ndalama ndi opanda mtengo.” (Yesaya 55:1) Chogaŵira chimenechi chikugwirabe ntchito. Tengani mwaŵi wa icho pamene mungakhoze.
[Zithunzi patsamba 24]
Chimwemwe chimatulukapo m’kugwiritsira ntchito ndalama kupereka kaamba ka mabanja athu ndi kuthandiza ena