Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kumvetsa Cholinga cha Kulanga
    Nsanja ya Olonda—2003 | October 1
    • Koma kulanga kumene Baibulo limafotokoza n’kosiyana ndi mmene anthuwo amaganizira. Mfumu ya nzeru Solomo inalemba kuti: “Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova.” (Miyambo 3:11) Mawu ameneŵa sakunena za mwambo, kapena kuti kulanga, kwawamba koma akunena za “mwambo wa Yehova,” kutanthauza kuti ndi kulanga kotsatira mfundo zapamwamba za Mulungu. Kulanga koteroko n’kumene kumapindulitsa mwauzimu, ndipo munthu angafune kulangidwa motero. Mosiyana ndi zimenezi, kulanga motsatira maganizo a anthu kumene kumatsutsana ndi mfundo zapamwamba za Yehova n’kolakwika ndipo kumapweteka ena. Zimenezi n’zimene zachititsa kuti anthu aziipidwa ndi kulanga.

      N’chifukwa chiyani timalimbikitsidwa kumvera kulanga kwa Yehova? Malemba amafotokoza kuti kulanga kwa Mulungu kumasonyeza kuti amakonda anthu amene anawalenga. Motero, Solomo anapitiriza kuti: “Yehova adzudzula omwe awakonda; monga atate mwana amene akondwera naye.”​—Miyambo 3:12.

      Kodi Kulanga ndi Kukhaulitsa N’zosiyana Bwanji?

      Kulanga kumene Baibulo limafotokoza kuli ndi mbali zosiyanasiyana monga kutsogolera, kulangiza, kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongolera, ngakhalenso chilango. Komabe, m’mbali zonsezo, chikondi n’chimene chimamulimbikitsa Yehova kuti alange munthu, ndipo cholinga chake chimakhala choti munthu wolangidwayo apindule. Yehova akamalanga munthu kuti amuwongolere sakhala n’cholinga chongokhaulitsa.

  • Kumvetsa Cholinga cha Kulanga
    Nsanja ya Olonda—2003 | October 1
    • Kodi chilango choterocho ‘chinaika chitsanzo cha kwa iwo akakhala osapembedza’ motani? Paulo, m’kalata imene analembera Atesalonika, ananena kuti nthaŵi imene tikukhala ino ndi nthaŵi imene Mulungu, kudzera mwa Yesu Kristu, ‘adzabwezera chilango kwa iwo osam’dziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino.’ Ndiyeno anapitiriza kuti: “Amene[ŵa] adzamva chilango, ndicho chiwonongeko chosatha.” (2 Atesalonika 1:8, 9) Mwachionekere, cholinga cha chilango choterocho si choti aphunzitse kapena awongolere anthu amene akuwapatsa chilangowo. Koma Yehova akamapempha anthu amene amamulambira kuti amvere kulanga kwake, satanthauza kuti awakhaulitsa monga mmene amachitira kwa anthu osalapa.

      N’zochititsa chidwi kuti Baibulo silifotokoza kuti khalidwe lalikulu la Yehova ndilo kupereka chilango. M’malo mwake, nthaŵi zambiri limati iye ndi mphunzitsi wachikondi ndiponso woleza mtima. (Yobu 36:22; Salmo 71:17; Yesaya 54:13) Inde, Mulungu akamalanga munthu n’cholinga chofuna kumuwongolera, nthaŵi zonse amatero mwachikondi ndiponso moleza mtima. Mwakumvetsa cholinga cha chilango, Akristu adzatha kuvomera kulangidwa ndi ena ndiponso adzatha kulanga ena ndi mtima wabwino.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena