Akatswiri Odumphadumpha m’Miyala ya m’Mapiri
M’MPHEPETE mwa nyanja ya Dead Sea, chakumadzulo kwake kunali mzinda wakale ndi chipululu cha En-gedi. Mipata ya pakati pa matanthwe ndi zigwengwe za kumaloko ndizo malo abwino okhala zinkhoma monga chomwe mukuchiona apachi.
Cholengedwa choyenda mosadodomachi ndi imodzi mwa nyama zodabwitsa. Tiyeni titsekule Baibulo kuti timvetsetse bwino nyama yochititsa chidwiyi.
“Mapiri Aatali Ndiwo Ayenera Zinkhoma”
Anaimba motero wamasalmo. (Salmo 104:18) Zinkhoma zinalengedwa mwakuti zizitha kukhala m’malo okwera kwambiri! Nzochenjera, zotha kuyenda pa malo amiyala mosaopa ndipo mwaliŵiro. Izi zili choncho pang’ono chifukwa cha mmene ziliri ziboda zake. Mpata wa pakati pa zigoba za kumapazi kwake umatheka kuwonjezeka kukula malinga ndi kulemera kwa chinkhomacho, zikumachipangitsa kutha kugwira pansi mwamphamvu chitaimirira kapena chikuyenda pa mwala wosongoka.
Zinkhoma sizichita chizungulire. Zikhoza kudumpha kuchokera patali ndi kukagwa pa kamalo kochepa kosakwana mapazi ake anayi. Katswiri wa biology Douglas Chadwick nthaŵi ina anaona chinkhoma koma chamtundu wina chikugwiritsira ntchito kupanda chizungulire kwake kudzibweza kuti chisapanikizike pa kamalo pamene sichikanatha kutembenuka. Iye akuti: “Chitaona mwala wina chapatali pafupifupi mamita 120 pansi, chinkhomacho chinaponda pansi mwamphamvu ndi miyendo yakutsogolo ndiye pang’onopang’ono chinagadabuka ngati kuchita pidigoli. Ndikumazizwa, chinkhomacho chinatembenuka kufikira miyendo yake inafika pansi mwakuti chinapenya komwe chimachokera.” (National Geographic) Nzosadabwitsa kuti zinkhoma zimatchedwa kuti “akatswiri adumphadumpha m’miyala ya m’mapiri.”
‘Kodi Mudziŵa Pamene Zinkhoma Zimaswa?’
Zinkhoma ndi zamanyazi kwambiri. Zimakonda kukhala kutali ndi anthu. Ndithudi, anthu amavutika kuti aziyandikire kwambiri kuti aone momwe zimakhalira kuthengo. Motero, Mwini “ng’ombe za pamapiri zikwi” moyenera anatha kufunsa munthuyo Yobu kuti: “Kodi udziŵa nyengo yakuswana zinkhoma?” Salmo 50:10; Yobu 39:1.
Nzeru yachibadwa ya chinkhoma imene Mulungu achipatsa imapangitsa chinkhoma chachikazi kuzindikira nthaŵi yakuswa. Chimafunafuna malo otetezereka ndi kuswerapo mwana mmodzi kapena aŵiri, kaŵirikaŵiri kumapeto kwa May kapena mu June. Ana obadwa kumenewo amayamba kuyenda mosadodoma pamasiku oŵerengeka chabe.
“Ngati Mbawala Yokonda ndi Chinkhoma”
Mfumu yanzeru Solomo inalimbikitsa amuna kuti: ‘Ukondwere ndi mkazi wokula naye. Ngati mbawala yokonda ndi chinkhoma’. (Miyambo 5:18, 19) Sananene izi ncholinga chopeputsa akazi. Mwachionekere, Solomo anali kuyerekezera kukongola, chifundo, ndi makhalidwe ena abwino a nyama zimenezi.
Chinkhoma ndi chimodzi mwa “zamoyo” zimene zimapereka umboni wa nzeru ya Mlengi. (Genesis 1:24, 25) Kodi sitili okondwa kuti Mulungu watipatsa zolengedwa zosangalatsa zimenezi?
[Mawu a Chithunzi patsamba 24]
Courtesy of Athens University