Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Yehova Apatsa Nzeru”
    Nsanja ya Olonda—1999 | November 15
    • M’mawu a atate wachikondi, mfumu yanzeru Solomo ya Israyeli wakale inanena kuti: “Mwananga, ukalandira mawu anga, ndi kusunga malamulo anga; kutcherera makutu ako kunzeru, kulozetsa mtima wako kukuzindikira; ukaitananso luntha, ndi kufuulira kuti ukazindikire; ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika; pompo udzazindikira kuopa Yehova ndi kum’dziŵadi Mulungu.”​—Miyambo 2:1-5.

      Kodi mukuona kuti kupeza nzeru ndi udindo wa yani? M’mavesi ameneŵa, mawu akuti “ukalandira,” “ukaitananso,” “ukaifunafuna,” akupezeka nthaŵi zitatu. Mwachionekere, ndi udindo wa aliyense wa ife kufunafuna nzeru ndi zonse zochirikiza nzeruyo, monga kuzindikira ndi luntha. Komabe, choyamba, tifunikira ‘kulandira’ ndiponso “kusunga” m’chikumbumtima mawu anzeru olembedwa m’Malemba. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kuphunzira Baibulo.

  • “Yehova Apatsa Nzeru”
    Nsanja ya Olonda—1999 | November 15
    • Mawuwo akuti “ukalandira,” “ukaitananso,” “ukaifunafuna” m’ndime yoyambirira ya chaputala chachiŵiri cha Miyambo akutsatana ndi mawu akuti ‘kusunga’, ‘kufuulira,’ ‘kuipwaira.’ N’chifukwa chiyani mlembiyo anagwiritsa ntchito mawu osonyeza mphamvu zowonjezereka ameneŵa? Buku lina limati: “Munthu wanzeruyu [pano] akunena motsindika za kufunika kwa khama pofunafuna nzeru.” Inde, tiyenera kulondola nzeru mwakhama ndi mikhalidwe ina yogwirizana nayo monga kuzindikira ndi luntha.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena