Kodi Zolankhula Zanu Zimapyoza Kapena Zimachiza?
M’NTHAŴI zino zoŵaŵitsa, nzosadabwitsa konse kuona kuti ambiri ali “a mtima wosweka” ndiponso “a mzimu wolapadi.” (Salmo 34:18) Choncho, malinga nkunena kwa mtumwi Paulo, nkofunika nthaŵi zonse ‘kulimbikitsa amantha mtima’ ndiponso ‘kuchirikiza ofooka.’ (1 Atesalonika 5:14) Koma kodi tingatani pamene munthu mnzathu atikhumudwitsa kapena atilakwira kwambiri? Zikatere, mwina tingaganize kuti ndi bwino kungomkhaulitsa munthuyo. Komabe, mpofunika kusamala. Uphungu, ngakhale utakhala wothandiza, ungakhale wovulaza ngati uperekedwa mwankhanza. Miyambo 12:18 imati: “Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga.”
Choncho, pamene tifuna kuwongolera winawake kapena kukambitsirana naye pacholakwa china, nkofunika kwambiri kukumbukira mbali yachiŵiri ya Miyambo 12:18 yomwe imati: “Lilime la anzeru lilamitsa.” Nthaŵi zonse dzifunseni kuti, ‘Ngati wina anafunikira kundiwongolera, kodi ineyo ndikanafuna kuti achite zimenezo motani?’ Ambirife timafuna kulimbikitsidwa osati kudzudzulidwa. Choncho tikhale okonda kuyamikira. Zimenezi nthaŵi zambiri zidzasonkhezera wolakwayo kuti awongolere, ndipo mosakayika konse adzayamikira chifukwa cha chithandizo chilichonse chomwe tidzapereka.
Nkothandiza chotani nanga kukamba mawu athu modekha! Mawu ochiza adzapangitsa womvetserayo kulingalira monga momwe analingalirira wamasalmo kuti: “Akandipanda munthu wolungama ndidzati nchifundo: akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu; mutu wanga usakane.”—Salmo 141:5.