Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mungatani Kuti Musasiye Kuphunzira Baibulo?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • Phunziro 12. Mayi ndi ana ake awiri akuphunzira Baibulo ndi wa Mboni za Yehova.

      PHUNZIRO 12

      Kodi Mungatani Kuti Musasiye Kuphunzira Baibulo?

      Kuphunzira Baibulo n’kothandiza kwambiri. Koma nthawi zina kuchita zimenezi kumakhala kovuta. Mwina mungamakayikire ngati mungakwanitse kupitiriza kuphunzira Baibulo. N’chifukwa chiyani mukuyenera kuchita khama kuti musasiye kuphunzira? N’chiyani chingakuthandizeni kuti musasiye kuphunzira ngakhale mutakumana ndi mavuto?

      1. N’chifukwa chiyani kuphunzira Baibulo n’kofunika kwambiri?

      Baibulo limati: “Mawu a Mulungu ndi amoyo komanso amphamvu.” (Aheberi 4:12) Baibulo ndi lothandiza kwambiri chifukwa limatiuza zimene Mulungu amaganiza komanso mmene amamvera akationa. Sikuti Baibulo limangokuthandizani kudziwa zinthu, koma lingakuthandizeninso kupeza nzeru zodalirika ndiponso kukhala ndi chiyembekezo chabwino. Koma chofunika kwambiri ndi choti Baibulo lingakuthandizeni kuti mukhale mnzake wa Yehova. Mukamaphunzira Baibulo mumakhala mukulola kuti mphamvu yake ikuthandizeni kusintha moyo wanu.

      2. N’chifukwa chiyani tiyenera kuona kuti choonadi cha m’Baibulo ndi chamtengo wapatali?

      Choonadi cha m’Baibulo chili ngati chuma chamtengo wapatali. N’chifukwa chake Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Gula choonadi ndipo usachigulitse.” (Miyambo 23:23) Tikamaganizira kufunika kwa choonadi cha m’Baibulo, timayesetsa mwakhama kupitiriza kuliphunzira ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto.​—Werengani Miyambo 2:4, 5.

      3. Kodi Yehova angakuthandizeni bwanji kuti musasiye kuphunzira?

      Popeza kuti Yehova ndi Mlengi wamphamvuyonse komanso Mnzanu, iye amakudziwani bwino ndipo amafuna kukuthandizani kuti mumudziwe. Mulungu angakupatseni “mtima wofuna kuchita zinthu zimene iye amakonda komanso mphamvu zochitira zinthuzo.” (Werengani Afilipi 2:13.) Choncho, ngati nthawi zina mungafunikire kulimbikitsidwa kuti mupitirize kuphunzira kapenanso kugwiritsa ntchito zimene mukuphunzira, iye angakuthandizeni. Ngati mukukumana ndi mavuto kapena kutsutsidwa, Mulungu angakupatseni mphamvu kuti mukwanitse kupirira. Muzipemphera kwa Yehova nthawi zonse kuti akuthandizeni kupitiriza kuphunzira Baibulo.​—1 Atesalonika 5:17.

      FUFUZANI MOZAMA

      Fufuzani kuti muone zimene mungachite kuti musasiye kuphunzira Baibulo ngakhale mumatanganidwa kapenanso mumatsutsidwa. Kenako ganizirani mmene Yehova angakuthandizireni kuti mupitirize kuphunzira.

      4. Muziona kuti kuphunzira Baibulo n’kofunika kwambiri

      Nthawi zina anthufe timatanganidwa kwambiri moti zingaoneke ngati n’zosatheka kupeza nthawi yophunzira Baibulo. Kodi n’chiyani chingatithandize? Werengani Afilipi 1:10, kenako mukambirane mafunso awa:

      • Kodi mumaona kuti ndi zinthu ziti zimene zili m’gulu la “zinthu zimene ndi zofunikadi kwambiri” pa moyo?

      • Kodi mungatani kuti muziona kuti kuphunzira Baibulo ndi chinthu chofunika kwambiri pa moyo wanu?

      A. Zithunzi: Zithunzi zosonyeza kuika miyala ndi mchenga m’chitini. 1. Mulu wa mchenga ndiponso wa miyala ikuluikulu. 2. Chitini chatsala pang’ono kudzadza ndi mchenga. 3. Miyala ikuluikulu ili pamwamba pa mchenga ndipo ina yagwera pansi. B. Zithunzi: 1. Mulu womwe uja wa mchenga komanso wa miyala. 2. Chitini chomwe chija chatsala pang’ono kudzaza ndi miyala ikuluikulu. 3. Mchenga wathiridwa m’chitini ndipo wadzaza kufika kukamwa. Mchenga wochepa uli pansi.
      1. Ngati mungayambe kuika mchenga m’chitini pambuyo pake n’kuika miyala, miyalayo singakwanemo yonse

      2. Ngati mungayambe kuika miyala m’chitinimo sizingavute kuti mchenga wambiri ulowemo. N’chimodzimodzinso ndi zimene zimachitika mukaika “zinthu zimene ndi zofunikadi kwambiri” pamalo oyamba m’moyo wanu. Mumatha kuzikwaniritsa komanso mumapeza nthawi yochitira zinthu zina

      Tikamaphunzira Baibulo timakhala tikudzidyetsa mwauzimu chifukwa chozindikira kuti tikufunikira kudziwa Mulungu ndi kumulambira. Werengani Mateyu 5:3, kenako mukambirane funso ili:

      • Kodi timapindula bwanji tikamayesetsa kupeza nthawi yophunzira Baibulo?

      5. Muzipirira mukamatsutsidwa

      Nthawi zina anthu ena angayese kukufooketsani kuti musiye kuphunzira Baibulo. Onani zimene zinachitikira Francesco. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

      VIDIYO: Anadalitsidwa Chifukwa Chosasiya Kuphunzira (5:22)

      Chithunzi cha muvidiyo yakuti, ‘Anadalitsidwa Chifukwa Chosasiya Kuphunzira.’ Francesco akusiyana ndi anzake pambuyo powafotokozera kuti sadzacheza nawonso.
      • Muvidiyoyi, kodi anzake a Francesco ndi mayi ake anachita chiyani iyeyo atawauza zimene akuphunzira?

      • Nanga anadalitsidwa bwanji chifukwa chakuti sanasiye kuphunzira?

      Werengani 2 Timoteyo 2:24, 25, kenako mukambirane mafunso awa:

      • Kodi anzanu ndi achibale anu amanena zotani chifukwa choti mukuphunzira Baibulo?

      • Malinga ndi mavesiwa, kodi muyenera kuchita chiyani ngati winawake sakusangalala chifukwa chakuti mukuphunzira Baibulo? N’chifukwa chiyani mukutero?

      6. Muzidalira Yehova kuti akuthandizeni

      Ubwenzi wathu ndi Yehova ukamalimba, m’pamenenso timafunitsitsa kuchita zinthu zomusangalatsa. Komabe nthawi zina tingavutike kusintha zinthu zina pa moyo wathu kuti tizichita zimene iye amafuna. Ngati mumamva choncho, musafooke. Yehova adzakuthandizani. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

      VIDIYO: Yehova Amatithandiza Kuti Tisinthe (3:56)

      • Muvidiyoyi, ndi zinthu ziti zimene Jim anasintha kuti azisangalatsa Yehova?

      • Ndi zinthu ziti zimene zakuchititsani chidwi mukaona zimene anachita kuti asinthe?

      Werengani Aheberi 11:6, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

      • Kodi Yehova amawachitira zotani anthu amene “amamufunafuna ndi mtima wonse,” kutanthauza anthu amene amachita khama kuti amudziwe ndi kuchita zinthu zomusangalatsa?

      • Mogwirizana ndi lembali, kodi inuyo mukuona kuti Yehova amamva bwanji akamaona khama limene mukuchita kuti muziphunzira Baibulo?

      MUNTHU WINA ATAKUFUNSANI KUTI: “N’chifukwa chiyani mukuphunzira Baibulo?”

      • Kodi mungayankhe bwanji?

      ZOMWE TAPHUNZIRA

      Ngati mukukumana ndi mavuto chifukwa chakuti mukuphunzira Baibulo, musasiye kudalira Yehova ndipo iye adzakudalitsani kuti muzisangalala ndi moyo mpaka kalekale.

      Kubwereza

      • N’chifukwa chiyani mumaona kuti choonadi cha m’Baibulo ndi chamtengo wapatali?

      • Kodi mungatani kuti “muzitha kusankha zinthu zimene ndi ­zofunikadi kwambiri”?

      • N’chifukwa chiyani muyenera kupemphera kuti Yehova akuthandizeni kupitiriza kuphunzira Baibulo?

      Zoti Muchite

      ONANI ZINANSO

      Onani njira 4 zomwe zathandiza anthu ambiri kuti azi ntchito nthawi mwanzeru.

      “Kodi Mungatani Kuti Muzigwiritsa Ntchito Bwino Nthawi?” (Galamukani!, February 2014)

      Onani mmene Yehova anathandizira mayi wina yemwe mwamuna wake sankamvetsa chifukwa chake ankayesetsa kuchita zinthu zosangalatsa Mulungu.

      Yehova Amatilimbikitsa Kuti Tithe Kulimbana Ndi Mavuto Athu (5:05)

      Onani mmene bambo wina anapindulira chifukwa choti mkazi wake sanasiye kuphunzira Baibulo.

      Ndinkaphunzira N’cholinga Chofuna Kupeza Zifukwa (6:30)

      Anthu ena amati a Mboni za Yehova amathetsa mabanja a anthu. Koma kodi zimenezi n’zoona?

      “Kodi a Mboni za Yehova Amapangitsa Kuti Mabanja a Anthu Athe Kapena Alimbe?” (Nkhani yapawebusaiti)

  • N’chiyani Chingatithandize Kuti Tizisankha Zinthu Mwanzeru?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • Phunziro 35. Bambo akufufuza pawebusaiti magalimoto omwe ali pamsika ndipo mkazi ndi ana ake akuyang’ana zomwe bamboyo akuchita.

      PHUNZIRO 35

      N’chiyani Chingatithandize Kuti Tizisankha Zinthu Mwanzeru?

      Tonsefe timafunika kusankha zochita pa moyo wathu. Komabe, zimene tingasankhe zingakhudze kwambiri moyo wathu komanso ubwenzi wathu ndi Yehova. Mwachitsanzo, timafunika kusankha komwe tikufuna kukakhala, mmene tingapezere ndalama komanso ngati tikufuna kukhala pabanja kapena ayi. Tikamasankha zinthu mwanzeru timasangalala komanso timasangalatsa Yehova.

      1. Kodi Baibulo lingakuthandizeni bwanji kuti muzisankha zinthu mwanzeru?

      Musanasankhe zochita pa nkhani inayake, muzipemphera kwa Yehova ndipo muzifufuza m’Baibulo kuti mudziwe maganizo a Yehova pa nkhaniyo. (Werengani Miyambo 2:3-6.) Nthawi zina Yehova amapereka lamulo lomveka bwino lokhudza nkhani inayake. Zikatero, mungachite bwino kwambiri kumvera lamulolo.

      Ndiye kodi mungasankhe bwanji zochita pa nkhani imene m’Baibulo mulibe lamulo lachindunji lokhudza nkhaniyo? Yehova sadzasiya kukutsogolerani “m’njira imene mukuyenera kuyenda.” (Yesaya 48:17) Kodi angachite bwanji zimenezi? M’Baibulo muli mfundo zimene zingakuthandizeni kusankha zochita. Mfundo za choonadi zomwe zimapezeka m’Baibulo zingakuthandizeni kudziwa maganizo a Mulungu pa nkhani yomwe mukufuna kusankhayo. Tikamawerenga Baibulo, nthawi zambiri timapeza mfundo zotithandiza kudziwa mmene Mulungu amaonera nkhani inayake. Choncho, tikazindikira mmene Yehova amamvera, timasankha zimene zimamusangalatsa.

      2. Kodi muyenera kuganizira zinthu ziti musanasankhe zochita?

      Baibulo limanena kuti: “Wochenjera amaganizira zotsatira za zimene akufuna kuchita.” (Miyambo 14:15) Zimenezi zikutanthauza kuti timafunika kuganiza kaye mofatsa tisanasankhe zochita. Choncho, musanasankhe zochita pa nkhani inayake, muzidzifunsa kuti: ‘Ndi mfundo ziti za m’Baibulo zomwe zingandithandize kuti ndisankhe zoyenera kuchita pa nkhaniyi? Kodi zimene ndingasankhe zikhudza bwanji moyo wanga? Nanga anthu ena ziwakhudza bwanji?’ Chofunika kwambiri, muzidzifunsa kuti, ‘Kodi zimene ndingasankhe zisangalatsa Yehova?’​—Deuteronomo 32:29.

      Yehova ali ndi ufulu wotiuza zoyenera kuchita ndi zosayenera kuchita. Tikadziwa bwino malamulo ndi mfundo zake n’kumayesetsa kuzigwiritsa ntchito pa moyo wathu, timakhala tikuphunzitsa chikumbumtima chathu kuti chikhale chabwino. Chikumbumtima ndi chimene chimatithandiza kuzindikira kuti zomwe tikufuna kuchita kapena zomwe tachita ndi zolondola kapena zolakwika. (Aroma 2:14, 15) Choncho, tikamaphunzitsa bwino chikumbumtima chathu, chidzatithandiza kuti tizisankha zochita mwanzeru.

      FUFUZANI MOZAMA

      Fufuzani kuti muone mmene mfundo za m’Baibulo komanso chikumbumtima zingatithandizire kuti tizisankha zochita mwanzeru.

      3. Muzitsatira mfundo za m’Baibulo

      Kodi mfundo za m’Baibulo zingatithandize bwanji tikamasankha zochita? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.

      VIDIYO: Muzitsatira Mfundo za M’Baibulo Mukamasankha Zochita (5:54)

      • Kodi Yehova anatipatsa mphatso yamtengo wapatali iti?

      • N’chifukwa chiyani Yehova anatipatsa mphatso imeneyi?

      • Kodi Yehova watipatsa chiyani pofuna kutithandiza kuti tizisankha zinthu mwanzeru?

      Kuti muone chitsanzo cha mfundo ya m’Baibulo, werengani Aefeso 5:15, 16. Kenako mukambirane mmene ‘mungagwiritsire ntchito bwino nthawi yanu’ . . .

      • powerenga Baibulo tsiku lililonse.

      • kuti mukhale mwamuna kapena mkazi wabwino, kholo kapenanso mwana wabwino.

      • kuti muzichita nawo misonkhano yampingo.

      4. Muziphunzitsa chikumbumtima chanu kuti muzisankha zinthu mwanzeru

      Sitimavutika kusankha zochita pa nkhani inayake ngati m’Baibulo muli lamulo lomveka bwino lokhudza nkhaniyo. Koma nanga bwanji ngati m’Baibulo mulibe lamulo lotithandiza kusankha zochita pa nkhani inayake? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.

      VIDIYO: “Khalani ndi Chikumbumtima Chabwino” (5:13)

      • Muvidiyoyi, kodi mlongoyu anachita chiyani kuti aphunzitse chikumbumtima chake komanso kuti asankhe zinthu zomwe zingasangalatse Yehova?

      Tikafuna kusankha zochita pa nkhani inayake, n’chifukwa chiyani sitiyenera kupempha anthu ena kuti atisankhire zochita? Werengani Aheberi 5:14, kenako mukambirane mafunso awa:

      • Zingakhale zosavuta kupempha anthu ena kuti atisankhire zochita pa nkhani inayake. Koma kodi ifeyo patokha tiyenera kusiyanitsa chiyani?

      • N’chiyani chomwe chingakuthandizeni kuti muziphunzitsa chikumbumtima chanu komanso kuti muzisankha zochita mwanzeru?

      Munthu akuyendetsa galimoto. Waika GPS patsogolo pa galimoto yake kuti asasochere.

      Mofanana ndi mapu chikumbumtima chimatithandiza kusankha bwino zoyenera kuchita pa moyo wathu

      5. Muzilemekeza chikumbumtima cha anthu ena

      Anthufe ndife osiyana choncho timasankhanso zinthu mosiyana. Ndiye tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza chikumbumtima cha anthu ena? Taganizirani zochitika ziwiri izi:

      Choyamba: Mlongo amene anazolowera kuphoda wasamukira mumpingo wina umene alongo amumpingomo amaona kuti kuphoda si koyenera.

      Werengani Aroma 15:1 ndi 1 Akorinto 10:​23, 24, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

      • Malinga ndi mavesiwa, kodi mlongoyo angasankhe kuchita chiyani? Nanga inuyo mungatani ngati muli ndi munthu wina amene chikumbumtima chake sichikumulola kuchita zimene inuyo chikumbumtima chanu chikukulolani kuchita?

      Chachiwiri: M’bale akudziwa bwino kuti Baibulo silimaletsa kumwa mowa mosapitirira malire, koma iyeyo wasankha kuti asamamwe mowa n’komwe. Kenako m’baleyo waitanidwa kuphwando ndipo akuona kuti abale ena akumwa mowa.

      Werengani Mlaliki 7:16 ndi Aroma 14:1, 10, kenako mukambirane mafunso awa:

      • Malinga ndi mavesiwa, kodi m’baleyu angasankhe kuchita chiyani? Nanga inuyo mungatani ngati mwaona munthu wina amene chikumbumtima chake chikumulola kuchita zimene inuyo chikumbumtima chanu sichikukulolani kuchita?

      Kodi ndi zinthu ziti zimene zingathandize munthu kuti azisankha zinthu mwanzeru?

      Mzimayi akupemphera.

      1. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kusankha zoyenera kuchita.​—Yakobo 1:5.

      Mzimayi yemweyu akufufuza pogwiritsa ntchito Baibulo, mabuku athu komanso kompyuta.

      2. Muzifufuza m’Baibulo, mabuku ndi zinthu zina zimene gulu lathu limafalitsa kuti mupeze mfundo zimene zingakuthandizeni. Mukhozanso kulankhulana ndi Akhristu amene amayesetsa kutsatira mfundo za Yehova pa moyo wawo.

      Mzimayi yemweyu akuganiza.

      3. Muziganizira mmene zosankha zanu zingakhudzire chikumbumtima chanu komanso zikumbumtima za anthu ena.

      ANTHU ENA AMANENA KUTI: “Aliyense ali ndi ufulu wochita zimene akufuna. Kaya anthu ena azinena zotani, ndi zawo zimenezo!”

      • N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira mmene zochita zathu zingakhudzire Mulungu komanso anthu ena?

      ZOMWE TAPHUNZIRA

      Tikadziwa maganizo a Yehova pa nkhani inayake timasankha zochita mwanzeru, kenako timaganizira mmene zochita zathuzo zingakhudzire anthu ena.

      Kubwereza

      • Kodi mungasankhe bwanji zochita zimene zingasangalatse Yehova?

      • Kodi mungaphunzitse bwanji chikumbumtima chanu?

      • Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumalemekeza chikumbumtima cha anthu ena?

      Zoti Muchite

      ONANI ZINANSO

      Mungatani kuti muzisankha zinthu zomwe zingakuthandizeni kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Mulungu?

      “Zosankha Zanu Zizilemekeza Mulungu” (Nsanja ya Olonda, April 15, 2011)

      Dziwani zambiri zokhudza mmene Yehova amatipatsira malangizo.

      Yehova Amatsogolera Anthu Ake (9:50)

      Onani zimene zinathandiza munthu wina kusankha zochita mwanzeru pa nkhani yovuta.

      Yehova Amatipatsa Zinthu Zabwino Zokhazokha (5:46)

      Onani zimene tingachite kuti tizisangalatsa Yehova ngakhale pa nkhani zimene palibe lamulo lachindunji.

      “Kodi Mumafunikira Lamulo la M’Baibulo Nthawi Zonse?” (Nsanja ya Olonda, December 1, 2003)

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena