Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Anthu Amtima Wapachala Ndingachite Nawo Bwanji?
    Galamukani!—2001 | December 8
    • “Anali atakwiya mosati n’kugwirika. Ndikukhulupirira kuti ankafuna kundimenya chifukwa chakuti anangondipezerera poti ndine mwana. Ndinam’funsa kwinaku ndikubwerera chafutambuyo kuti: ‘Kodi ukufuna kundimenyeranji? Taima kaye! Ndikuti taima kaye! Inetu Sindinakulakwire chilichonse. Kodi n’chifukwa chiyani ukufuna kundimenya? Sindikudziŵa n’komwe chimene chakukwiyitsa. Tatiye tingokambirana basi,’” anatero David mnyamata wa zaka 16.

  • Kodi Anthu Amtima Wapachala Ndingachite Nawo Bwanji?
    Galamukani!—2001 | December 8
    • Baibulo limapereka malangizo anzeru aŵa: “Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mau owawitsa aputa msunamo.” (Miyambo 15:1) Inde, kubwezera munthu wa mtima wapachala pomuuza “mawu owawitsa” kumangomukwiyitsa kwambiri munthuyo. Koma kuyankha mofatsa nthaŵi zambiri kumaziziritsa zinthu n’kukhazikitsa anthu mitima pansi.

      Kumbukirani nkhani ya David uja tam’tchula poyamba paja. Iye anakambirana ndi mnyamata wokonda zomenya anzake uja kuti alongosole chimene chinam’kwiyitsa. Ndiye anatulukira kuti winawake anali atam’bera chakudya chake, motero pamenepa anali kuthera ukali wake pa iyeyo chifukwa chakuti anali munthu woyamba kukumana naye. David anam’thandiza maganizo mnyamatayo pomuuza kuti, “Ukandimenya si ndiye kuti upeza chakudya chakocho.” Kenaka anamuuza kuti bwanji apitire limodzi kukhitchini. David anati: “Chifukwa chakuti mkulu wopereka chakudya kukhitchini ndinkadziŵana naye, ndinam’pezera chakudya china mnyamata wovuta uja. Ndiye anandigwira chanza ndipo kuyambira pamenepo anayamba kugwirizana nane.” Kodi mukuona pankhaniyi kuti mawu ofatsa n’ngamphamvudi? Mwambi wina unanenadi zoona kuti, “Lilime lofatsa lithyola fupa.”—Miyambo 25:15.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena