-
“Nzeru Itchinjiriza”Nsanja ya Olonda—2007 | July 15
-
-
Kodi kukhala ndi nzeru kumasintha bwanji zimene timalankhula? Mfumu yanzeruyi inati: “Wolabadira mawu adzapeza bwino; ndipo wokhulupirira Yehova adala. Wanzeru mtima adzatchedwa wochenjera; ndipo kukoma kwa milomo kuyenjezera kuphunzira. Nzeru ndi kasupe wa moyo kwa mwini wake; koma mwambo wa zitsiru ndi utsiru. Mtima wa wanzeru uchenjeza m’kamwa mwake, nuphunzitsanso milomo yake.”—Miyambo 16:20-23.
-
-
“Nzeru Itchinjiriza”Nsanja ya Olonda—2007 | July 15
-
-
Motero n’zosabwitsa kuti “wanzeru mtima”amatchedwa wochenjera,”kapena kuti wozindikira. (Miyambo 16:21) Inde, nzeru yotereyi ndi “kasupe wa moyo” kwa anthu amene ali nayo. Nanga bwanji anthu opusa? Iwo ‘amanyoza nzeru ndi mwambo.’ (Miyambo 1:7) Kodi kusamvera chilango cha Yehova kumawabweretsera zotani? Amapitiriza kulangidwa, ndipo nthawi zambiri chilango chake chimakhala chachikulu kwambiri. Monga tanenera pamwambapa, Solomo anati: “Nzeru ndi kasupe wa moyo kwa mwini wake; koma mwambo wa zitsiru ndi utsiru.” (Miyambo 16:22) Anthu opusa angathenso kudziika m’mavuto, kudzichititsa manyazi, kudziputira matenda, ndiponso kufa msanga.
-