Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g21 No. 3 tsamba 14-15
  • Chifukwa Chake Yankho la Funsoli Ndi Lofunika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifukwa Chake Yankho la Funsoli Ndi Lofunika
  • Galamukani!—2021
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mudzayamba kusangalala kwambiri ndi moyo wanu
  • Mudzapeza malangizo odalirika amene angakuthandizeni
  • Mudzapeza mayankho a mafunso anu
  • Mudzakhala ndi chiyembekezo cha zinthu za m’tsogolo
  • Kodi Kukhulupirira Zoti Kuli Mulungu N’kothandiza Bwanji?
    Galamukani!—2015
  • Kodi Zoona Zenizeni za Mulungu N’zotani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Baibulo Limatithandiza Kukhala Ndi Chiyembekezo
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Baibulo Limatithandiza Kukhala Ndi Chiyembekezo
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Yambani Kuphunzira Baibulo
Onani Zambiri
Galamukani!—2021
g21 No. 3 tsamba 14-15
Anthu akuyang’ana mwachidwi nyama zomwe zili mumtengo.

Chifukwa Chake Yankho la Funsoli Ndi Lofunika

N’chifukwa chiyani n’zofunika kudziwa ngati kuli Mlengi? Ngati mukukhutira ndi umboni wakuti kuli Mulungu yemwe ndi wamphamvuyonse, ndiye kuti mungakonde kuonanso umboni wakuti Baibulo linauziridwa ndi iye. Ngati mukukhulupirira zimene Baibulo limanena, zikhoza kukuthandizani m’njira zotsatirazi:

Mudzayamba kusangalala kwambiri ndi moyo wanu

BAIBULO LIMANENA KUTI: “[Mulungu] anachita zabwino. Anakupatsani mvula kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambiri. Anadzaza mitima yanu ndi chakudya komanso chimwemwe.”​—Machitidwe 14:17.

KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI?: Zinthu zonse zimene timasangalala nazo m’chilengedwechi ndi mphatso zochokera kwa Mlengi. Mukhoza kuyamikira kwambiri mphatso zimenezi mukazindikira kuti amene anazipereka amakuganizirani.

Mudzapeza malangizo odalirika amene angakuthandizeni

BAIBULO LIMANENA KUTI: “Udzamvetsa zinthu zolondola, zolungama, zowongoka, ndiponso njira yonse ya zinthu zabwino.”​—Miyambo 2:9.

KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI?: Monga Mlengi wanu, Mulungu amadziwa zimene mumafunikira kuti muzisangalala. Mukamawerenga Baibulo, mukhoza kuphunzira zinthu zimene zingakuthandizeni pa moyo wanu.

Mudzapeza mayankho a mafunso anu

BAIBULO LIMANENA KUTI: “Udzamudziwadi Mulungu.”​—Miyambo 2:5.

KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI?: Kudziwa kuti Mlengi alipo kungakuthandizeni kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri monga: Kodi cholinga cha moyo n’chiyani? N’chifukwa chiyani timavutika? Kodi chimachitika n’chiyani tikamwalira? Mukhoza kupeza mayankho ogwira mtima m’Baibulo.

Mudzakhala ndi chiyembekezo cha zinthu za m’tsogolo

BAIBULO LIMANENA KUTI: “‘Maganizo anga kwa inu ndikuwadziwa bwino. Ndikuganizira zokupatsani mtendere osati masoka, kuti mukhale ndi chiyembekezo chabwino ndiponso tsogolo labwino,’ watero Yehova.”​—Yeremiya 29:11.

Onerani vidiyo yakuti Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Baibulo Limanena Zoona? komanso yakuti Kodi Analemba Baibulo Ndi Ndani? pa jw.org. Kuti mupeze mavidiyowa lembani mawu akuti “Baibulo limanena zoona” kapena “analemba Baibulo” m’kabokosi kofufuzira.

KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI?: Mulungu akulonjeza kuti m’tsogolomu adzachotsa zinthu zoipa, adzathetsa mavuto komanso imfa. Mukamakhulupirira malonjezo a Mulungu, chiyembekezo chanu cha zinthu za m’tsogolo chidzakuthandizani kupirira molimba mtima mavuto amene mumakumana nawo tsiku ndi tsiku.

Mmene Kukhulupirira Kuti Kuli Mlengi Kwathandizira Anthu Ena

Cyndi.

“Nthawi zonse ndimagoma ndikaona mmene Mulungu amatithandizira m’njira zosiyanasiyana pa moyo wathu. Amatithandiza kudziwa zinthu zofunika kwambiri pa moyo, mmene tingathetsere kusamvana komanso zimene tingachite kuti tikhale anzake.”​—Cyndi, U.S.A.

Elise.

“Kukhulupirira kuti kuli Mlengi kumandithandiza kuti ndizikhala ndi moyo wokhutira komanso wosangalala. Chifukwa chakuti ndaphunzira zinthu zambiri zokhudza iye, zinthu zimene analenga komanso Mawu ake, zimandithandiza kukhala wanzeru.”—Elise, France.

Peter.

“Kugwiritsa ntchito zinthu zimene Mlengi wathu amatiphunzitsa kudzera m’Baibulo kwandithandiza kukhala munthu wosangalala. Kwandithandiza kuti ndizichita chidwi ndi ena, ndizikhala wokhutira komanso ndisakhale wovuta. Kwandithandizanso kuti ndikhale bambo wabwino.”​—Peter, Netherlands.

Liz.

“Kale, chomwe ndinkadziwa ndi kudya, kugona komanso kuvutika kupita kuntchito pa nthawi yake. Sunali moyo wosangalatsa. Koma pano ndimaona kuti moyo ndi mphatso yamtengo wapatali kwambiri ndipo ndiyenera kumasangalala nawo komanso kuusamalira.”​—Liz, Estonia.

Adrien.

“Sindimachedwa kuda nkhawa ndi zinthu. Koma kudziwa kuti zinthu zoipa, zopanda chilungamo komanso mavuto zitha posachedwa, kumandithandiza kuti ndipirire.”​—Adrien, France.

Onani mmene Baibulo limayankhira mafunso ofunika kwambiri okhudza moyo. Onerani vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo?​—Vidiyo Yathunthu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena