Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 1/15 tsamba 32
  • Monga Maapulo Agolidi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Monga Maapulo Agolidi
  • Nsanja ya Olonda—1994
Nsanja ya Olonda—1994
w94 1/15 tsamba 32

Monga Maapulo Agolidi

MAAPULO​—mmene amakomera m’maso ndi m’kamwa! Baibulo limagwiritsira ntchito chipatso chokoma chimenechi m’fanizo losonkhezera maganizo pamene limati: “Mawu oyenera a panthaŵi yake akunga [maapulo agolidi, NW] m’nsengwa zasiliva.” (Miyambo 25:11) Kodi mawu ameneŵa akutanthauzanji?

“Maapulo agolidi m’nsengwa zasiliva” angatanthauze chinthu chosema, monga mbale yasiliva yochembedwa yokhala ndi zipatso zagolidi. Popeza kuti mavesi oyambirira m’chaputala chimenechi akutchula mafikidwe a kwa mfumu, vesili lingakhale likutchula mphatso zoperekedwa kwa wolamulira​—zokometsera zagolidi za mpangidwe wonga wa maapulo zoikidwa pambale zasiliva. (Miyambo 25:6, 7) Nzokongola chotani nanga zimenezo!

Muli kukongola kofanana ndi kumeneko m’mawu a panthaŵi yake, oyenera, ndi aulemu, kaya akhale olembedwa kapena olankhulidwa. Amakhala okoma, olimbikitsa ndi opindulitsa mwanjira zambiri. Makamaka mawu ouziridwa mwaumulungu a m’Baibulo ndiwo ali okongola monga “maapulo agolidi m’nsengwa zasiliva.”

Monga momwe kwasonyezedwera ndi mwambi wanzeru wa Mfumu Solomo pa Miyambo 25:11, iye “anasanthula akapeze mawu okondweretsa, ndi zolemba zowongoka ngakhale mawu owona.” (Mlaliki 12:10; Miyambo 25:1) Zaka mazana ambiri pambuyo pake, mtumwi Wachikristu Paulo analemba kuti: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa.” (2 Timoteo 3:16) Inde, Baibulo lili ndi uphungu wopindulitsa, maulosi, mafanizo, ndi chowonadi zoŵala ndi zokongola kwambiri kwakuti zimaposa zopanga za amisiri. Ndiponso, aliyense wopeza nzeru m’Mawu a Mulungu, Baibulo, amapeza chuma chamtengo wake ndipo angakhale ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya.​—Miyambo 4:7-9; Yohane 17:3.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena